Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 1

Mawu Oyamba Ogwila Mtima

Mawu Oyamba Ogwila Mtima

Machitidwe 17:22

ZOFUNIKILA: Mawu anu oyamba afunika kukopa cidwi, kuchula nkhani yanu, komanso kuonetsa mmene nkhaniyo ikuwakhudzila omvela anu.

MOCITILA:

  • Kukopa cidwi. Sankhani funso, mfundo, cocitika, kapena nkhani ya pa nyuzi imene omvela anu angacite nayo cidwi.

  • Chulani nkhani yanu. Onetsetsani kuti mawu anu oyamba akumveketsa bwino nkhani yanu kwa omvela, na colinga ca ulaliki wanu.

  • Onetsani cifukwa cake nkhaniyo ni yofunika. Kambani zinthu zothandizadi kwa omvela anu. Afunika kumvetsa bwino-bwino mmene nkhaniyo ingawathandizile.