Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 3

Kugwiritsa Ntchito Mafunso

Kugwiritsa Ntchito Mafunso

Mateyu 16:13-16

MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito mafunso oyenera kuti anthu akhale ndi chidwi, kuti mukambirane ndi anthu, komanso kuti mutsindike mfundo zofunika.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzithandiza anthu kuti akhale ndi chidwi. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kuti azifuna kumva zambiri.

  • Muzikambirana ndi anthu. Kuti anthu akhulupirire mfundo zimene mukunena, muyenera kufunsa mafunso angapo owathandiza kuti atsatire mpaka kufika potsimikizira mfundozo.

  • Muzitsindika mfundo zofunika. Funsani funso limene lingachititse anthu kuyembekezera kuti amve mfundo yofunika. Muzifunsa mafunso obwereza pambuyo pa mfundo yofunika iliyonse kapena pomaliza nkhani yanu.