Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 3

Gwilitsilani Nchito Mafunso

Gwilitsilani Nchito Mafunso

Mateyu 16:13-16

ZOFUNIKILA: Mafunso aluso angakuthandizeni kuwakopa cidwi omvela anu, kulingalila nawo, na kugogomeza mfundo zofunika.

MOCITILA:

  • Kukopa cidwi na kucipitiliza. Funsani mafunso osafuna yankho othandiza munthu kuganiza.

  • Athandizeni kumvetsa nkhaniyo. Athandizeni kutsatila mfundo zanu mwa kuwafunsa mafunso angapo owathandiza kuona mfundo.

  • Gogomezani mfundo zofunika. Funsani funso locititsa cidwi kuti mumveketse lingalilo lofunika. Pambuyo pokambilana kapena kufotokoza mfundo yofunika, kapenanso potsiliza makambilano anu, funsani mafunso obweleza.