Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 4

Kachulidwe ka Malemba Koyenela

Kachulidwe ka Malemba Koyenela

Mateyu 22:41-45

ZOFUNIKILA: Konzekeletsani maganizo a omvela anu musanaŵelenge lemba.

MOCITILA:

  • Dziŵani cifukwa cimene mufuna kuŵelengela lembalo. Chulani lemba iliyonse mwa njila yokopa cidwi omvela anu ku mfundo yanu yofunika pa vesilo.

  • Muzichula Baibo kuonetsa maziko a mfundo zanu. Pokamba na ŵanthu okhulupilila za Mulungu, muzichula Baibo kuti ni Mawu a Mulungu, poonetsa kuti ndilo gwelo la nzelu zopambana.

  • Kopelani cidwi pa lembalo. Funsani funso limene lembalo lidzayankha. Kapena chulani vuto limene lembalo lidzaonetsa molithetsela. Kapenanso chulani mfundo imene lembalo lidzawathandiza kuimvetsa.