Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 5

Kuwerenga Molondola

Kuwerenga Molondola

1 Timoteyo 4:13

MFUNDO YAIKULU: Muziwerenga momveka bwino komanso mosalakwitsa.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikonzekera bwino. Muzidzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani mawu amenewa analembedwa? Muziwerenga magulu a mawu osati kumangotchula liwu ndi liwu. Muzipewa kuwonjezera mawu, kudumpha mawu kapena kusemphanitsa mawu. Muzitsatira zizindikiro zonse za m’kalembedwe.

  • Muzitchula mawu alionse molondola. Ngati simukudziwa katchulidwe kabwino ka mawu, muyenera kufufuza, kumvetsera nkhani zojambulidwa kapena kufunsa anzanu omwe amadziwa bwino.

  • Muzilankhula momveka bwino. Kuti mawu anu azituluka bwino muyenera kukweza bwino mutu komanso kutsegula pakamwa mokwanira. Muzitchula mawu alionse momveka bwino.