Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 6

Kumveketsa Bwino Cifukwa Coŵelengela Lemba

Kumveketsa Bwino Cifukwa Coŵelengela Lemba

Yohane 10:33-36

ZOFUNIKILA: Osangoŵelenga lemba basi n’kupita pa mfundo yotsatila iyai. Onetsetsani kuti omvela anu akuona bwino-bwino kugwilizana kwa lemba imene mwaŵelenga na mfundo imene mukufotokoza.

MOCITILA:

  • Onetsani mawu ofunikila. Mukaŵelenga lemba, onetsani mawu okhudzana na mfundo yanu yaikulu. Mungacite zimenezi mwa kuwabweleza mawu amenewo, kapena kufunsapo funso lopangitsa omvela anu kuwachula mawu ofunikilawo.

  • Gogomezani mfundo yanu. Ngati poŵelenga lemba mwamveketsa bwino cifukwa coliŵelengela, fotokozani mmene mawu ofunikila a pa lembalo amaonetsela cifukwaco.

  • Mveketsani mosavuta colinga ca lembalo. Pewani kufotokozapo mfundo zina zosathandiza kweni-kweni kumveketsa mfundo yaikulu. Malinga na zimene omvela anu akudziŵa kale pa nkhaniyo, onani kuti ni mfundo zingati zimene mungafunike kufotokoza kuti mumveketse mfundo yanu.