Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 10

Kusintha-sinthako Mawu

Kusintha-sinthako Mawu

Miyambo 8:4, 7

ZOFUNIKILA: Mveketsani bwino malingalilo, ndipo akhudzeni mtima omvela anu posintha-sinthako mphamvu ya mawu, kuwakweza kapena kuwatsitsa, komanso liŵilo lake.

MOCITILA:

  • Muzisintha-sinthako mphamvu ya mawu anu. Wonjezelani mphamvu ya mawu pogogomeza mfundo yaikulu, komanso polimbikitsa omvela anu. Citaninso cimodzi-modzi poŵelenga mawu a ciweluzo a m’Malemba. Cepetsani mphamvu ya mawu pofuna kukopa cidwi, kapena pochula zoopsa, olo zodetsa nkhawa.

  • Muzisiyanitsa kamvekedwe ka mawu anu. Kwezani kamvekedwe ka mawu anu poonetsa kusangalala, ukulu wa cinthu, msenga kaya kuti mtunda. Tsitsani mawu anu poonetsa cisoni kapena nkhawa.

  • Siyanitsani liŵilo la mawu anu. Lankhulani mofulumila kuonetsa cisangalalo. Koma musathamange pofuna kumveketsa mfundo zofunika.