Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 12

Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima

Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima

1 Atesalonika 2:7, 8

MFUNDO YAIKULU: Mukamalankhula, anthu aziona kuti mumawaganizira komanso mumawafunira zabwino.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muziganizira anthu. Pokonzekera nkhani yanu muziganizira mavuto amene anthu akukumana nawo. Muziganiziranso mmene anthuwo akumvera chifukwa cha mavuto awo.

  • Muzisankha bwino mawu. Cholinga chanu chizikhala kuwalimbikitsa, kuwatonthoza komanso kuwapatsa mphamvu. Pewani kukhumudwitsa anthu, kudzudzula anthu omwe si Mboni kapena kutsutsa kwambiri mfundo zimene anthu ena amazikhulupirira kwambiri.

  • Muzisonyeza kuti mumakonda anthu. Mawu komanso nkhope yanu zizisonyeza kuti mumaganizira anthu. Muzikondanso kumwetulira.