Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 13

Kumveketsa Phindu ya Nkhani

Kumveketsa Phindu ya Nkhani

Miyambo 3:21

ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kumvetsa mmene nkhani yanu ikukhudzila umoyo wawo. Komanso afotokozeleni mocitila nazo zimene aphunzila.

MOCITILA:

  • Ganizilani omvela anu. Ganizilani cifukwa cake kuli kofunikila kuti anthuwo amvele nkhani yanu, ndipo onani mfundo zimene zingawathandize kweni-kweni.

  • M’nkhani yanu yonse, onetsani omvela anu zimene afunika kucita. Kungoyamba nkhani yanu, womvela aliyense afunika kukamba mu mtima mwake kuti, ‘Nkhani iyi ni yothandizadi kwa ine.’ Pamene mutambasula mfundo iliyonse, onetsani mmene ingawathandizile kweni-kweni. Pewani kumangokamba mwacisawawa.