Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 14

Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu

Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu

Aheberi 8:1

ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kukutsatilani m’nkhani yanu. Onetsani bwino mmene mfundo yaikulu iliyonse ikugwilizanila na colinga canu, komanso na mutu wa nkhani.

MOCITILA:

  • Khalani na colinga. Kodi colinga ca nkhani yanu ni kupeleka cidziŵitso, kukhutilitsa omvela anu pa nkhani inayake, kapena ni kuwalimbikitsa? Poikamba, onetsetsani kuti mfundo zazikulu zonse zikuthandizila kukwanilitsa colinga cimeneco.

  • Gogomezani mutu wa nkhani. M’nkhani yanu yonse, muzikumbutsanso mutu wanu wa nkhani mwa kubweleza mawu ake ofunika kwambili, kapena kuchula mawu ena ofanana nawo tanthauzo.

  • Mfundo zanu zazikulu zizimveka bwino komanso mosavuta. Sankhani cabe mfundo zothandizila kumveketsa mutu wa nkhani, zimenenso mungazifotokoze bwino m’nthawi imene mwapatsidwa. Cepetsani mfundo zikulu-zikulu, fotokozani iliyonse payokha-payokha, ndipo cokani pa ina kupita pa inzake moonekela bwino.