PHUNZIRO 17
Kulankhula Zomveka
MMENE MUNGACHITIRE:
-
Yesetsani kuti muidziwe bwino nkhani yanu. Mukaidziwa bwino nkhani yanu mukhoza kuifotokoza mosavuta m’mawu anuanu.
-
Muzigwiritsa ntchito ziganizo zifupizifupi zosavuta kumva. Ngakhale kuti pena mukhoza kugwiritsa ntchito ziganizo zitalizitali, muzizidula moyenerera mukamafotokoza mfundo yofunika.
-
Muzifotokoza mawu ovuta. Pewani kugwiritsa ntchito mawu amene anthu sawadziwa. Muzifotokozera mawu ovuta, anthu a m’Baibulo osadziwika kwambiri komanso miyeso ndi zikhalidwe zakale.