Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 17

Muzikamba Zosavuta Kumvetsa

Muzikamba Zosavuta Kumvetsa

1 Akorinto 14:9

ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kumvetsa tanthauzo la zimene mukukamba.

MOCITILA:

  • Iŵelengeni mokwanila nkhani yanu. Muimvetsetse bwino-bwino kuti mukaikambe mosavuta komanso m’mawu anu-anu.

  • Muzikamba ziganizo zifupi-zifupi na mawu osavuta. Ngakhale kuti ziganizo zazitaliko zili bwino, mveketsani mfundo zofunika mwa kukamba ziganizo zofupikilapo.

  • Fotokozelani mawu acilendo. Cepetsani mawu acilendo kwa omvela anu. Koma ngati m’pofunika kuti muchule liwu lacilendo, kapena munthu wosadziŵika kwambili wa m’Baibo, muyeso kapena mwambo wamakedzana, fotokozelani.