PHUNZIRO 17

Kulankhula Zomveka

Kulankhula Zomveka

1 Akorinto 14:9

MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula m’njira yoti anthu azimvetsa zimene mukunena.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Yesetsani kuti muidziwe bwino nkhani yanu. Mukaidziwa bwino nkhani yanu mukhoza kuifotokoza mosavuta m’mawu anuanu.

  • Muzigwiritsa ntchito ziganizo zifupizifupi zosavuta kumva. Ngakhale kuti pena mukhoza kugwiritsa ntchito ziganizo zitalizitali, muzizidula moyenerera mukamafotokoza mfundo yofunika.

  • Muzifotokoza mawu ovuta. Pewani kugwiritsa ntchito mawu amene anthu sawadziwa. Muzifotokozera mawu ovuta, anthu a m’Baibulo osadziwika kwambiri komanso miyeso ndi zikhalidwe zakale.