Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 18

Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela

Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela

1 Akorinto 9:19-23

ZOFUNIKILA: Kambani mwa njila yopangitsa omvela anu kuganizilapo pa nkhaniyo, na kuona kuti aphunzilapodi kanthu.

MOCITILA:

  • Ganizilani zimene omvela anu amazidziŵa kale. M’malo mongobweleza zimene iwo anamvelapo kale, athandizeni kuona nkhaniyo mwatsopano.

  • Fufuzani na kusinkha-sinkha. Ngati n’kotheka, phatikizanipo mfundo zomvekako zacilendo, kapena zocitika za pa nyuzi monga zitsanzo pofuna kumveketsa mfundo zazikulu. Ganizilani mozama mmene zitsanzo zimenezo zikugwilizanila na nkhani yanu.

  • Onetsani phindu ya nkhani yanu. Unikani mmene mfundo za m’Malemba zingathandizile omvela anu mu umoyo wawo wa tsiku na tsiku. Fotokozani mikhalidwe yakuti-yakuti, kapena maganizo, kapenanso zocitika zoyenelela kwa omvela anu.