Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 19

Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela

Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela

Miyambo 3:1

ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kuona kufunika kwa zimene akuphunzila kuti acitepo kanthu.

MOCITILA:

  • Thandizani omvela anu kudziunika. Funsani mafunso othandiza omvela anu kuunikanso maganizo awo.

  • Kambani mowalimbikitsa. Athandizeni kuganizila cifukwa cacikulu cocitila zinthu zabwino. Alimbikitseni kukhala na zolinga zabwino, monga kukonda Yehova, anthu anzawo, na ziphunzitso za m’Baibo. Kambilanani nawo omvela anu; osakamba mowalamula. M’malo mowacotsela ulemu, onetsetsani kuti atsala olimbikitsika, komanso ofunitsitsa kucitapo kanthu.

  • Apangitseni kumaonapo Yehova. Unikani mmene ziphunzitso za m’Baibo, mfundo zake, na malamulo opezekamo, zimaonetsela makhalidwe a Mulungu na cikondi cake pa ife. Limbikitsani omvela anu kukhala na mtima wofuna kudziŵa maganizo a Yehova kuti azicita zom’kondweletsa.