Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 20

Mawu Otsiliza Ogwila Mtima

Mawu Otsiliza Ogwila Mtima

Mlaliki 12:13, 14

ZOFUNIKILA: M’mawu anu othela, limbikitsani omvela anu kuona ubwino wa zimene aphunzila kuti akazigwilitsile nchito.

MOCITILA:

  • Gwilizanitsani mawu anu otsiliza na mfundo yaikulu ya nkhani yanu. Bwelezaninso mfundo zazikulu, kapena zikambeninso m’mawu ena.

  • Limbikitsani omvela anu. Afotokozeleni zofunika kucita, komanso zifukwa zake zomveka. Kambani mocokela pa mtima, komanso mwa cidalilo.

  • Mawu anu otsiliza azikhala osavuta kumva komanso acidule. Osabweletsaponso mfundo zatsopano. Mwa mawu ocepa cabe, alimbikitseninso kucitapo kanthu.