Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 4

Kodi Mulungu Woona Ndani?

Kodi Mulungu Woona Ndani?

M’mbili yonse ya anthu, anthu akhala akulambila milungu yambili yosiyana-siyana. Koma Baibo imatiuza kuti kuli Mulungu mmodzi yekha “wamkulu kuposa milungu ina yonse.” (2 Mbiri 2:5) Kodi Mulungu ameneyo ndani? Ndipo n’ciyani cimene cimam’pangitsa kukhala wamkulu kuposa milungu ina yonse imene anthu amapembedza? M’phunzilo lino, mudzaona mmene Mulungu ameneyu akudzifotokozela yekha kuti mum’dziŵe.

1. Kodi Mulungu dzina lake ndani, ndipo tingatsimikize bwanji kuti amafuna tilidziŵe dzina lake?

M’Baibo, Mulungu amadzifotokoza yekha kwa ife. Amanena kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Ŵelengani Yesaya 42:5, 8.) Dzina lakuti “Yehova” analimasulila kucokela ku Ciheberi, ndipo limatanthauza kuti “Amacititsa Kukhala.” Yehova amafuna kuti dzina lake tilidziŵe. (Ekisodo 3:15) Nanga tingatsimikize bwanji zimenezi? Iye anaonetsetsa kuti dzina lake lalembedwa m’Baibo maulendo oposa 7,000! a Dzina lakuti Yehova ni la “Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.”—Deuteronomo 4:39.

2. Kodi Baibo imatiunikila ciyani za Yehova?

Baibo imakamba kuti pa milungu yonse imene anthu amailambila, Yehova yekha ndiye Mulungu woona. Cifukwa ciyani? Pali zifukwa zingapo. Yehova ndiye ali na mphamvu zopambana, ndipo iye yekhayo ndiye “Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” (Ŵelengani Salimo 83:18, Buku Lopatulika.) Iye ni ‘Wamphamvuzonse,’ kutanthauza kuti angacite ciliconse cimene angafune. Ndiye ‘analenga zinthu zonse’—za kumwamba ndiponso za padziko lapansi. (Chivumbulutso 4:8, 11) Yehova yekhayo ndiye amene wakhalako nthawi zonse, ndipo adzakhalakobe mpaka muyaya.—Salimo 90:2.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani kusiyana kumene kulipo pakati pa maina audindo ochulila Mulungu, na dzina lake lenileni. Dziŵaninso mmene iye anaululila dzina lake kuti tilidziŵe, ndiponso cifukwa cake.

3. Mulungu ali na maina audindo ambili, koma dzina lenileni ni limodzi cabe

Kuti muone kusiyana pakati pa maina audindo a munthu na dzina lake lenileni, Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Kodi pali kusiyana kotani pakati pa maina audindo monga lakuti “Ambuye,” na dzina lenileni?

Baibo imakamba kuti anthu amalambila milungu yambili komanso ambuye ambili. Ŵelengani Salimo 136:1-3, na kukambilana funso ili:

  • Kodi “Mulungu wa milungu” komanso “Mbuye wa ambuye” ndani?

4. Yehova amafuna kuti dzina lake mulidziŵe na kumalichula

Kodi mudziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti dzina lake mulidziŵe? Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Muganiza n’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti dzina lake lidziŵike?

Yehova amafuna kuti anthu azilichula dzina lake. Ŵelengani Aroma 10:13, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani n’kofunika kumachula dzina la Mulungu lakuti Yehova?

  • Kodi mumamva bwanji munthu akamakumbukila dzina lanu na kumalichula?

  • Nanga muganiza Yehova amamva bwanji mukamachula dzina lake?

5. Yehova amafuna kuti mukhale bwenzi lake

Mzimayi wina wa ku Cambodia dzina lake Soten, pamene anadziŵa dzina la Mulungu ‘anamva bwino kwambili.’ Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Mu vidiyo imene tatamba, kodi Soten anamva bwanji atadziŵa dzina la Mulungu?

Kuti mukhale bwenzi la munthu wina, coyamba mumafuna kudziŵa dzina lake. Ŵelengani Yakobo 4:8a, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Yehova akukupemphani kuti mucite ciyani?

  • Kodi kudziŵa dzina la Mulungu na kumalichula kudzakuthandizani bwanji?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Kuli Mulungu mmodzi yekha, conco zilibe kanthu kuti umuchula dzina liti.”

  • Kodi mumakhulupilila kuti dzina la Mulungu ni Yehova?

  • N’cifukwa ciyani Mulungu amafuna kuti dzina lake tizilichula?

CIDULE CAKE

Yehova ndilo dzina la Mulungu woona yekhayo. Iye amafuna kuti dzina limeneli tilidziŵe na kumalichula kuti tikhale mabwenzi ake.

Mafunso Obweleza

  • Kodi Yehova amasiyana bwanji na milungu ina yonse imene anthu amaipembedza?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kumalichula dzina la Mulungu?

  • Timadziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tikhale mabwenzi ake?

Colinga

FUFUZANI

Pezani zifukwa zamphamvu zisanu zotsimikizila kuti Mulungu alikodi.

“Kodi Mulungu Alikodi?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani cifukwa cake n’zomveka kukhulupilila kuti Mulungu wakhala aliko nthawi zonse.

“Ndani Anapanga Mulungu?” (Nsanja ya Mlonda, August 1, 2014)

Dziŵani cifukwa cake tiyenela kumachula dzina la Mulungu, ngakhale kuti sitidziŵa kachulidwe kake kenikeni kapoyamba.

“Kodi Yehova N’ndani?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Kodi zili n’kanthu dzina limene tikumuchula nalo Mulungu? Onani cifukwa cake tikunena kuti dzina lake lenileni ni limodzi cabe.

“Kodi Mulungu Ali na Maina Angati?” (Nkhani ya pawebusaiti)

a Kuti mumve zambili pa tanthauzo la dzina la Mulungu limeneli, na cifukwa cimene analicotsela m’ma Baibo ena, onani Mutu 1 wa Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu.