Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 8

Mukhoza Kukhala Bwenzi la Yehova

Mukhoza Kukhala Bwenzi la Yehova

Yehova amafuna kuti mufike pom’dziŵa bwino. Cifukwa ciyani? Adziŵa kuti mukadziŵa zambili za makhalidwe ake, njila zake, na colinga cake kwa inu, mudzakhala wofunitsitsa kupalana naye ubwenzi. Koma kodi n’zothekadi kupalana ubwenzi na Mulungu? (Ŵelengani Salimo 25:14) Kodi muyenela kucita ciyani kuti mukhale bwenzi la Mulungu? Baibo imayankha mafunso amenewa, ndipo imaonetsa kuti ubwenzi na Yehova umaposa ubwenzi umene mungakhale nawo na munthu wina aliyense.

1. Kodi Yehova akukupemphani kuti mucite ciyani?

“Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Kodi izi zitanthauza ciyani? Yehova akukupemphani kuti mukhale bwenzi lake. Anthu ena cimawavuta kukhulupilila kuti angakhale bwenzi la Mulungu cifukwa n’zosatheka kumuona. Koma m’Mawu ake Baibo, Yehova amatiuza zonse zimene tifunika kudziŵa zokhudza makhalidwe ake kuti tikhale naye pa ubwenzi. Ngati timaŵelenga uthenga wa Mulungu kwa ife m’Baibo, ubwenzi wathu na Yehova udzalimba ngakhale kuti sitinamuonepo.

2. N’cifukwa ciyani Yehova ndiye Bwenzi labwino koposa limene mungakhale nayo?

Yehova amakukondani kupambana munthu wina aliyense. Amafuna kuti muzikhala acimwemwe, komanso kuti muzipemphela kwa iye nthawi ina iliyonse mukafuna thandizo. Mukhoza kumutulila “nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Yehova ni wokonzeka kuthandiza mabwenzi ake, kuwatonthoza komanso kuwamvetsela.—Ŵelengani Salimo 94:18, 19.

3. Kodi Yehova amafuna kuti mabwenzi ake azicita ciyani?

Yehova amakonda anthu onse, koma maka-maka, “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Yehova amafuna kuti mabwenzi ake aziyesetsa kucita zinthu zabwino na kupewa kucita zoipa. Anthu ena amaona kuti n’zosatheka kucita zonse zimene Yehova amafuna, komanso kupewa zonse zoipa. Komabe, Yehova ni wacifundo. Iye amalandila munthu aliyense amene amam’konda m’ceniceni, amenenso amayesetsa kucita zokondweletsa Mulungu.—Salimo 147:11; Machitidwe 10:34, 35.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani zimene mungacite kuti mukhale bwenzi la Yehova. Ndipo dziŵani cifukwa cake iye ndiye Bwenzi labwino kopambana.

4. Abulahamu anali bwenzi la Yehova

Nkhani ya m’Baibo ya Abulahamu (wochedwanso Abulam) imatithandiza kumvetsa zimene kukhala bwenzi la Mulungu kumatanthauza. Ŵelengani zokhudza Abulahamu pa Genesis 12:1-4. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Yehova anauza Abulahamu kucita ciyani?

  • Nanga Yehova anamulonjeza ciyani?

  • Kodi Abulahamu analabadila motani malangizo a Yehova?

5. Zimene Yehova amayembekezela kwa mabwenzi ake

Pali zinthu zimene timayembekezela kwa mabwenzi athu.

  • Kodi mungafune kuti mabwenzi anu azicita zinthu motani kwa inu?

Ŵelengani 1 Yohane 5:3, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Yehova amayembekezela ciyani kwa mabwenzi ake?

Kuti tizimvela Yehova, tiyenela kusintha zocita kapena makhalidwe athu. Ŵelengani Yesaya 48:17, 18, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti mabwenzi ake apange masinthidwe?

Mnzathu amatikumbutsa zinthu zimene zingatiteteze na kutipindulila. N’zimene nayenso Yehova amacita kwa mabwenzi ake

6. Yehova amathandiza mabwenzi ake

Yehova amathandiza mabwenzi ake kuthana na mavuto. Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Kodi Yehova anam’thandiza bwanji mzimayi wa mu vidiyo iyi kupewa kuganizila zinthu zomulefula?

Ŵelengani Yesaya 41:10, 13, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Yehova akulonjeza kuti adzacita ciyani kwa mabwenzi ake onse?

  • Kodi muganiza kuti Yehova angakhale bwenzi lanu labwino? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Mabwenzi apamtima amatithandiza tikakhala pa mavuto. Yehova nayenso adzakuthandizani

7. Kukhala bwenzi la Yehova kumafuna kukambilana naye

Kukambilana kumalimbitsa ubwenzi. Ŵelengani Salimo 86:6, 11, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Yehova tingakambe naye bwanji?

  • Nanga Yehova amakamba nafe bwanji?

Ife timakamba na Yehova kupitila m’pemphelo; nayenso amakamba nafe kupitila m’Baibo

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “N’zosatheka kukhala bwenzi la Mulungu.”

  • Kodi mungaseŵenzetse lemba liti loonetsa kuti n’zotheka kukhala bwenzi la Yehova?

CIDULE CAKE

Yehova afuna mukhale bwenzi lake, ndipo adzakuthandizani kuti mumuyandikile.

Mafunso Obweleza

  • Kodi Yehova amawathandiza bwanji mabwenzi ake?

  • N’cifukwa ciyani Yehova amalimbikitsa mabwenzi ake kupanga masinthidwe pa umoyo wawo?

  • Kodi muganiza Yehova amauza mabwenzi ake kucita zinthu zimene sangakwanitse kucita? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Colinga

FUFUZANI

Kodi kupalana ubwenzi na Mulungu kungasinthe bwanji umoyo wanu?

“Yehova Ndiye Mulungu Wofunika Kum’dziŵa” (Nsanja ya Mlonda, February 15, 2003)

Pezani cifukwa cake mzimayi wina akuona kuti ubwenzi wake na Yehova unam’pulumutsa.

“N’nali Kuopa Imfa!” (Nsanja ya Mlonda Na. 1 2017)

Mvelani zimene acinyamata akukamba za mmene amamuonela Yehova.

Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kutanthauza Ciyani? (1:46)