Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 9

Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo

Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo

Pemphelo lingakuthandizeni m’njila zambili. Mwacitsanzo, lingakuthandizeni pamene mufunikila citsogozo mu umoyo wanu, komanso pamene mukufuna mayankho pa mafunso ofunika amene muli nawo. Pemphelo lingakuthandizeninso pamene mwafunikila citonthozo kapena cilimbikitso. Pamwamba pa izi, lingakuthandizeninso kumuyandikila Yehova. Koma mungafunse kuti: ‘Kodi kapempheledwe kovomelezeka ni kabwanji? Kodi Mulungu amamvela mapemphelo onse? Kodi cofunika n’ciyani kuti Mulungu aziyankha mapemphelo anga?’ Tiyeni tione.

1. Kodi tiyenela kupemphela kwa ndani, ndipo tingapemphelele zinthu zotani?

Yesu anaphunzitsa kuti tiyenela kupemphela kwa Atate wathu wakumwamba yekhayo basi. Yesu nayenso anali kupemphela kwa Yehova. Iye anakamba kuti: “Koma inu muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba . . . ’” (Mateyu 6:9) Tikamapemphela kwa Yehova, timalimbitsa ubwenzi wathu na iye.

Kwenikweni, tikhoza kupemphelela nkhani iliyonse. Ngakhale n’telo, kuti Mulungu ayankhe mapemphelo athu, mapemphelowo ayenela kugwilizana na cifunilo cake. “Ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake [Mulungu], amatimvela.” (1 Yohane 5:14) Yesu anapeleka citsanzo ca zinthu zoyenela kupemphelela. (Ŵelengani Mateyu 6:9-13.) Tiyenela kupemphela kwa Mulungu ponena za nkhawa zathu. Ndiponso, tisamaiŵale kumuyamikila pa zimene amaticitila, komanso kum’pempha kuti athandize anthu ena.

2. Kodi tiyenela kupemphela motani?

Baibo imatilimbikitsa kuti: “Mukhuthulileni [Mulungu] za mumtima mwanu.” (Salimo 62:8) Mapemphelo athu ayenela kukhala ocokela pansi pa mtima. Tingapemphele motulutsa mawu kapena camumtima, pa nthawi iliyonse komanso malo aliwonse. Ndiponso, Yehova amalola kupemphela kwa iye kaya cogwada, cokhala pansi, kapena coimilila. Cacikulu ni kuonetsa ulemu kwa iye.

3. Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphelo athu?

Amatiyankha m’njila zosiyana-siyana. Yehova anatipatsa Mawu ake Baibo, mmene nthawi zambili timapezamo mayankho ku mafunso athu. Kuŵelenga Mawu a Mulungu ‘kumapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.’ (Salimo 19:7; ŵelengani Yakobo 1:5.) Mulungu angatipatse mtendele wa mumtima pamene tikumana na zovuta. Ndipo angakhudze mitima ya olambila ake kuti atithandize pamene tafunikila thandizo.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mmene mungapelekele mapemphelo ocokela pansi pa mtima olandilika kwa Mulungu, na mmene pemphelo lingakuthandizileni.

4. Zimene Mulungu amafuna popemphela

Kodi n’ciyani cingapangitse Mulungu kumvela mapemphelo athu kapena kusawamvela? Tambani VIDIYO.

Yehova amafuna kuti tizipemphela kwa iye. Ŵelengani Salimo 65:2, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi muganiza kuti “Wakumva pemphelo” amafunadi kuti inu muzipemphela kwa iye? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Ngati tifuna kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu, tiyenela kuyesetsa kumvela malamulo ake pa umoyo wathu. Ŵelengani Mika 3:4 na 1 Petulo 3:12, kenako kambilanani funso ili:

  • Kodi tiyenela kutsimikiza kucita ciyani kuti Yehova aziyankha mapemphelo athu?

Pa nthawi ya nkhondo, asilikali a mbali zonse ziŵili angapemphele kuti agonjetse anzawo. Kodi Mulungu angayankhe mapemphelo otelo?

5. Mapemphelo athu azicokela pansi pa mtima

Anthu ena anaphunzitsidwa mapemphelo ocita kuloŵeza. Koma kodi ni mmene Mulungu amafunila kuti tizipemphela kwa iye? Ŵelengani Mateyu 6:7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi tingapewe bwanji kukamba “zinthu mobwelezabweleza” popemphela?

Tsiku lililonse yesani kuganizila dalitso linalake mu umoyo wanu, ndipo muyamikileni Yehova pa dalitso limenelo. Citani zimenezi tsiku lililonse kwa mlungu wonse. Mukatelo, mudzakhala mutapemphelela zinthu 7 zosiyana-siyana popanda kubweleza-bweleza.

Tate wacikondi amafuna kuti mwana wake azimuuza za kumtima kwake. Mofananamo, Yehova naye amafuna kuti tizipemphela kwa iye mocokela pansi pa mtima

6. Mwayi wa pemphelo ni mphatso yocokela kwa Mulungu

Kodi pemphelo lingatipatse bwanji mphamvu pa nthawi yabwino komanso pa nthawi yovuta? Tambani VIDIYO.

Baibo imatitsimikizila kuti pemphelo lingatithandize kupeza mtendele wa mumtima. Ŵelengani Afilipi 4:6, 7, na kukambilana mafunso aya:

  • Olo kuti si nthawi zonse pamene kupemphela kungacotsepo vuto, n’cifukwa ciyani kumakhalabe kothandiza?

  • Kodi ni zinthu ziti zimene mungapemphelele?

Kodi mudziŵa?

Liwu lakuti ‘Ameni’ limatanthauza “zikhaledi momwemo,” kapena kuti “ndithudi.” Kucokela m’nthawi ya anthu ochulidwa m’Baibo, liwu lakuti ‘ameni’ lakhala likuchulidwa kumapeto kwa pemphelo.—1 Mbiri 16:36.

7. Patulani nthawi yopemphela

Nthawi zina tingatangwanike kwambili moti n’kuiŵala kupemphela. N’cifukwa ciyani kupeleka pemphelo kunali kofunika kwambili kwa Yesu? Ŵelengani Mateyu 14:23, komanso Maliko 1:35, kenako kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Yesu anacita bwanji kuti apatule nthawi yopemphela?

  • Nanga inu mungapatule nthawi iti yopemphela?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Pemphelo ni yongokumvetsako bwino cabe.”

  • Nanga inu muganiza bwanji?

CIDULE CAKE

Mapemphelo oona mtima amatiyandikizitsa kwa Mulungu, na kutipatsa mtendele wa mumtima. Amatipatsanso mphamvu yocita zinthu zokondweletsa Yehova.

Mafunso Obweleza

  • Kodi tiyenela kupemphela kwa ndani?

  • Kodi tiyenela kupemphela motani?

  • Nanga pemphelo limatithandiza bwanji?

Colinga

FUFUZANI

Pezani mayankho pa mafunso amene anthu ambili ali nawo pa nkhani ya pemphelo.

“Mfundo 7 Zimene Muyenela Kudziŵa pa Nkhani ya Pemphelo” (Nsanja ya Mlonda, October 1, 2010)

Dziŵani zifukwa zazikulu zopemphelela, komanso mmene mungapelekele mapemphelo abwino.

“N’cifukwa Ciyani Niyenela Kupemphela?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani zimene Baibo imaphunzitsa za amene tiyenela kupemphelako.

“Kodi Niyenela Kupemphela kwa Oyela Mtima?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Mu vidiyo ya nyimbo iyi, onani ngati zili n’kanthu, malo kapena nthawi yopempelela.

Muzipemphela Nthawi Zonse (1:22)