Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 12

Mungatani Kuti Musasiye Kuphunzira Baibulo?

Mungatani Kuti Musasiye Kuphunzira Baibulo?

Kuphunzira Baibulo ndi kothandiza kwambiri. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Mwina mungamakayikire ngati mungakwanitse kupitiriza kuphunzira Baibulo. N’chifukwa chiyani muyenera kuchita khama kuti musasiye kuphunzira? N’chiyani chingakuthandizeni kuti musasiye kuphunzira ngakhale muzikumana ndi mavuto?

1. N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri?

Baibulo limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheberi 4:12) Baibulo ndi lothandiza kwambiri chifukwa lingakuthandizeni kudziwa mmene Mulungu amaganizira komanso mmene amakuonerani. Sikuti Baibulo limangokuthandizani kudziwa zinthu, koma lingakuthandizeninso kupeza nzeru zodalirika ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chabwino. Koposa zonse, Baibulo lingakuthandizeni kuti mukhale mnzake wa Yehova. Mukamaphunzira Baibulo mumakhala mukulola kuti mphamvu yake ikuthandizeni kusintha moyo wanu.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali?

Choonadi cha m’Baibulo chili ngati chuma chamtengo wapatali. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Gula choonadi ndipo usachigulitse.” (Miyambo 23:23) Tikamaganizira kufunika kwa choonadi cha m’Baibulo, timachita khama poliphunzira ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto.​—Werengani Miyambo 2:​4, 5.

3. Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji kuti musasiye kuphunzira?

Popeza kuti Yehova ndi Mlengi Wamphamvuyonse komanso Mnzanu, iye amakudziwani bwino ndipo amafuna kukuthandizani kuti mumudziwe. Mulungu ‘angalimbitse zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.’ (Werengani Afilipi 2:13.) Choncho, ngati nthawi zina mungafunikire kulimbikitsidwa kuti mupitirize kuphunzira kapenanso kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzira, iye angakuthandizeni. Ngati mukukumana ndi mavuto kapena kutsutsidwa, Mulungu angakupatseni mphamvu kuti mukwanitse kupirira. Muzipemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti akuthandizeni kupitiriza kuphunzira Baibulo.​—1 Atesalonika 5:17.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti muone zimene mungachite kuti musasiye kuphunzira Baibulo ngakhale mumatanganidwa kapenanso mumatsutsidwa. Kenako ganizirani mmene Yehova angakuthandizireni kuti mupitirize kuphunzira.

4. Muziona kuti kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri

Nthawi zina anthufe timatanganidwa kwambiri moti zingaoneke ngati n’zosatheka kupeza nthawi yophunzira Baibulo. Kodi n’chiyani chingatithandize? Werengani Afilipi 1:​10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi mumaona kuti ndi zinthu ziti zimene zili m’gulu la “zinthu zofunika kwambiri” pa moyo?

  • Mungatani kuti muziona kuti kuphunzira Baibulo ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu?

  1. Ngati mungayambe kuika mchenga m’chitini pambuyo pake n’kuika miyala, miyalayo singakwanemo yonse

  2. Ngati mungayambe kuika miyala m’chitinimo sizingavute kuti mchenga wambiri ulowemo. N’chimodzimodzinso ndi zimene zimachitika mukaika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba m’moyo wanu. Mumatha kuzikwaniritsa komanso mumapeza nthawi yochitira zinthu zina

Tikamaphunzira Baibulo timakhala tikudzidyetsa mwauzimu chifukwa chozindikira kuti tikufunikira kudziwa Mulungu ndi kumulambira. Werengani Mateyu 5:​3, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi timapindula bwanji tikamayesetsa kupeza nthawi yophunzira Baibulo?

5. Muzipirira mukamatsutsidwa

Nthawi zina anthu ena angayese kukufooketsani kuti musiye kuphunzira Baibulo. Onani zimene zinachitikira Francesco. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Muvidiyoyi, kodi anzake a Francesco ndi mayi ake anachita chiyani iyeyo atawauza zimene akuphunzira?

  • Nanga anadalitsidwa bwanji chifukwa chakuti sanasiye kuphunzira?

Werengani 2 Timoteyo 2:24, 25, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi anzanu ndi achibale anu amanena zotani chifukwa choti mukuphunzira Baibulo?

  • Malinga ndi mavesiwa, kodi muyenera kuchita chiyani ngati winawake sakusangalala chifukwa chakuti mukuphunzira Baibulo? N’chifukwa chiyani mukutero?

6. Muzidalira Yehova kuti akuthandizeni

Ubwenzi wathu ndi Yehova ukamalimba, m’pamenenso timafunitsitsa kuchita zinthu zomusangalatsa. Komabe nthawi zina tingavutike kusintha zinthu zina pa moyo wathu kuti tizichita zimene iye amafuna. Ngati mumamva choncho, musafooke. Yehova adzakuthandizani. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Muvidiyoyi, ndi zinthu ziti zimene Jim anasintha kuti azisangalatsa Yehova?

  • Ndi zinthu ziti zimene zikukuchititsani chidwi mukaona zimene anachita kuti asinthe?

Werengani Aheberi 11:6, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yehova amawachitira zotani anthu amene “amamufunafuna ndi mtima wonse,” kutanthauza anthu amene amachita khama kuti amudziwe ndi kuchita zinthu zomusangalatsa?

  • Mogwirizana ndi lembali, kodi inuyo mukuona kuti Yehova amamva bwanji akamaona khama lomwe mukuchita pophunzira Baibulo?

MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “N’chifukwa chiyani mukuphunzira Baibulo?”

  • Kodi mungayankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Ngakhale kuti mungakumane ndi mavuto pophunzira Baibulo, musasiye kudalira Yehova ndipo iye adzakudalitsani kuti muzisangalala ndi moyo mpaka kalekale.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani mumaona kuti choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali?

  • Mungatani kuti “muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti”?

  • N’chifukwa chiyani muyenera kupemphera kuti Yehova akuthandizeni kupitiriza kuphunzira Baibulo?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani njira 4 zomwe zathandiza anthu ambiri kugwiritsa ntchito nthawi mwanzeru.

“Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi?” (Galamukani!, February 2014)

Onani mmene Yehova anathandizira mayi wina yemwe mwamuna wake sankamvetsa chifukwa chake ankayesetsa kusangalatsa Mulungu.

Yehova Amatilimbikitsa Kuti Tithe Kulimbana Ndi Mavuto Athu (5:05)

Onani mmene bambo wina anapindulira chifukwa choti mkazi wake sanasiye kuphunzira Baibulo.

Ndinkaphunzira N’cholinga Chofuna Kupeza Zifukwa (6:30)

Anthu ena amati a Mboni za Yehova amathetsa mabanja a anthu. Koma kodi zimenezi n’zoona?

“Kodi a Mboni za Yehova Amapangitsa Kuti Mabanja a Anthu Athe Kapena Alimbe?” (Nkhani yapawebusaiti)