Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 14

Kodi Tiyenela Kum’lambila Motani Mulungu Kuti Tim’kondweletse?

Kodi Tiyenela Kum’lambila Motani Mulungu Kuti Tim’kondweletse?

Monga tinaonela m’phunzilo lapita, si zipembedzo zonse zimene zimakondweletsa Mulungu. Komabe n’zotheka kulambila Mlengi wathu m’njila imene imam’kondweletsa. Kodi “kupembedza [olo, cipembedzo]” kumene kumam’kondweletsa n’kotani? (Yakobo 1:27) Onani zimene Baibo imaphunzitsa.

1. Kodi kulambila kwathu kuyenela kutsamila pa ciyani?

Kulambila kwathu kuyenela kutsamila pa Baibo. Yesu anati kwa Mulungu: “Mawu anu ndiwo coonadi.” (Yohane 17:17) Zipembedzo zina zimanyalanyaza coonadi ca m’Mawu ouzilidwa a Mulungu, Baibo. M’malo mwake, amaloŵetsapo ziphunzitso za anthu na miyambo yawo. Yehova sakondwela nawo anthu amene ‘amakankhila pambali malamulo a Mulungu.’ (Ŵelengani Maliko 7:9.) Koma ngati kulambila kwathu kutsamila pa Baibo, ndipo tikamatsatila uphungu wake, tidzakondweletsa mtima wa Mulungu.

2. Kodi tiyenela kum’lambila motani Yehova?

Cifukwa Yehova ndiye anatilenga, tiyenela kulambila iye yekhayo basi. (Chivumbulutso 4:11) Izi zitanthauza kuti tiyenela kumukonda na kumulambila, popanda kuseŵenzetsa fano lililonse kapena cifanizilo.—Ŵelengani Yesaya 42:8.

Kulambila kwathu kuyenela kukhala ‘koyela ndi kovomelezeka’ kwa Yehova. (Aroma 12:1) Conco, tiyenela kutsatila malamulo ake. Mwacitsanzo, aja okonda Yehova, ayenela kukondanso malamulo ake okhudza cikwati na kuwatsatila. Ndipo ayenela kupewa zinthu zowononga thanzi monga fodya, mankhwala osokoneza bongo, komanso ucidakwa. a

3. N’cifukwa ciyani tiyenela kulambila Yehova pamodzi na olambila anzathu?

Misonkhano yathu ya mlungu na mlungu imatipatsa mwayi ‘wotamanda Yehova . . . pamsonkhano.’ (Salimo 111:1, 2) Njila imodzi yocitila zimenezi ni kuimba nyimbo zotamanda Yehova. (Ŵelengani Salimo 104:33.) Yehova amatilangiza kuti tizipezeka pa misonkhano cifukwa amatikonda. Ndipo akudziŵa kuti misonkhano idzatithandiza kukapeza moyo wosatha. Kumisonkhano timalimbikitsidwa, ifenso timalimbikitsa ena.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake Yehova savomekeza kugwilitsa nchito zifanizilo pomulambila. Phunzilani njila zofunika zotamandila Mulungu.

4. Sitiyenela kuseŵenzetsa zifanizilo polambila

Tidziŵa bwanji kuti kugwilitsa nchito zifanizilo kumam’khumudwitsa Mulungu? Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • N’ciyani cinacitika pamene anthu a Mulungu ena m’nthawi za m’Baibo anayesa kumulambila mwa kuseŵenzetsa fano?

Anthu ena amakamba kuti amamva kumuyandikila Mulungu ngati agwilitsa nchito mafano pomulambila. Koma kodi n’kutheka kuti pocita zimenezo amamukankhila patali Mulungu? Ŵelengani Ekisodo 20:4-6, komanso Salimo 106:35, 36, kenako kambilanani mafunso aya:

  • Ni zinthu ziti kapena zifanizilo zimene mwaonapo anthu akuseŵenzetsa polambila?

  • Kodi Yehova amakuona bwanji kuseŵenzetsa zifanizilo polambila?

  • Nanga inu mumakuona bwanji kuseŵenzetsa zifanizilo polambila?

5. Kulambila Yehova yekhayo kumatiwombola ku zikhulupililo zabodza

Onani mmene kulambila Yehova movomelezeka kumatiwombolela ku zikhulupililo zabodza. Tambani VIDIYO.

Ŵelengani Salimo 91:14, na kukambilana funso ili:

  • Tikamaonetsa cikondi kwa Yehova polambila iye yekhayo, kodi iye akulonjeza kuti adzaticitila ciyani?

6. Timalambila Mulungu pa misonkhano ya mpingo

Timatamanda Yehova na kulimbikitsana poimba nyimbo zacitamando, komanso mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano ya mpingo. Ŵelengani Salimo 22:22, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi mumasangalala kumva ena akupeleka ndemanga pa misonkhano?

  • Kodi mungakonzekele kuti inunso mukapelekepo ndemanga?

7. Yehova amakondwela tikamauzako ena zimene timaphunzila

Pali mipata yambili youzako ena mfundo za m’Baibo. Ŵelengani Salimo 9:1, komanso 34:1, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mwaphunzilako ciyani m’Baibo cimene mungafune kuuzako munthu wina?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Cipembedzo cilibe vuto, Mulungu amayang’ana mtima wa munthu.”

  • Nanga inu muganiza bwanji?

CIDULE CAKE

Timakondweletsa Mlengi wathu pamene tilambila iye yekha, kumutamanda pa misonkhano ya mpingo, komanso kuuzako ena zimene timaphunzila.

Mafunso Obweleza

  • Kodi tingaidziŵe bwanji njila yolambilila Mulungu movomelezeka?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kulambila Yehova yekhayo basi?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kulambila pamodzi na ŵena ofuna kukondweletsa Mulungu?

Colinga

FUFUZANI

Mu nkhani yakuti “Ndinali Kulambira Mafano,” ŵelengani mmene mzimayi wina anamasukila pa kulambila mafano.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2011)

Dziŵani cingakuthandizeni kuti muzipeleka ndemanga pa misonkhano ya mpingo.

“Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo” (Nsanja ya Mlonda, January 2019)

Onani mmene mnyamata wina anapindulila popezeka pa misonkhano olo kuti cinali covuta kwa iye kutelo.

Yehova Amanikonda (3:07)

Anthu ambili amakhulupilila kuti mtanda ni cizindikilo ca Akhristu. Koma kodi tiyenela kugwilitsa nchito mtanda polambila?

“N’cifukwa Ciyani Mboni za Yehova Siziseŵenzetsa Mtanda Polambila?” (Nkhani ya pawebusaiti)

a Nkhani zimenezi tidzazikambilana m’maphunzilo apatsogolo.