Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 18

Mmene Akhristu Enieni Tingawadziŵile

Mmene Akhristu Enieni Tingawadziŵile

Anthu mabiliyoni amanena kuti ni Akhristu. Ngakhale n’telo, iwo ali na zikhulupililo zosiyana-siyana, ndipo amayendela mfundo za cikhalidwe zosiyana-siyana pa umoyo wawo. Conco, kodi Akhristu enieni tingawadziŵe bwanji?

1. Kodi Mkhristu weniweni ndani?

Akhristu ni ophunzila a Yesu Khristu, kapena kuti otsatila ake. (Ŵelengani Machitidwe 11:26.) Nanga iwo amaonetsa bwanji kuti alidi ophunzila a Yesu? Iye anakamba kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga.” (Yohane 8:31) Izi zitanthauza kuti Akhristu enieni ayenela kutsatila zimene Yesu anaphunzitsa. Yesu pophunzitsa anali kugwilitsa nchito Malemba. Akhristu enieni nawonso, zimene amakhulupilila zimacokela m’Baibo.—Ŵelengani Luka 24:27.

2. Kodi Akhristu enieni amaonetsa bwanji cikondi?

Yesu anauza otsatila ake kuti: “Mukondane monga mmene inenso ndakukondelani.” (Yohane 15:12) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwakonda ophunzila ake? Anali kupatula nthawi yoceza nawo, anali kuwalimbikitsa, komanso anali kuwathandiza. Pothela pake, iye anataya ngakhale moyo wake weniweniwo kaamba ka iwo. (1 Yohane 3:16) Akhristu enieni nawonso cikondi cawo si capakamwa cabe ayi. Amacionetsa kwa wina na mnzake m’mawu komanso m’zocita zawo.

3. Kodi nchito yofunika kwambili imene Akhristu enieni amagwila ni yotani?

Yesu anawapatsa nchito ophunzila ake. “Anawatumiza kukalalikila Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:2) Akhristu oyambilila sanali kulalikila cabe m’malo awo olambilila, anali kulalikilanso kulikonse kopezeka anthu, komanso ku makomo a ŵanthu. (Ŵelengani Machitidwe 5:42; 17:17.) Masiku anonso, Akhristu enieni amalalikila coonadi ca m’Baibo kulikonse kumene kumapezeka anthu. Cifukwa cokonda anthu anzawo, iwo ni okonzeka kutayilapo nthawi yawo na mphamvu zawo kuti auzeko ena uthenga wa m’Baibo wopeleka ciyembekezo na citonthozo.—Maliko 12:31.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani mmene mungasiyanitsile Akhristu enieni na ŵanthu amene satsatila ziphunzitso za Yesu na citsanzo cake.

4. Amafufuza coonadi m’Baibo

Akhristu oyambilila anali kulemekeza Mawu a Mulungu, anali kulalikila kwa ena, ndiponso anali kukondana wina na mnzake

Si onse omwe amati ni Akhristu amene amatsatila coonadi ca m’Baibo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

  • Kodi machalichi ena ochedwa acikhristu amaphunzitsa ziti zimene n’zosemphana na zimene Yesu anaphunzitsa?

Yesu anaphunzitsa coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Ŵelengani Yohane 18:37, na kukambilana funso ili:

  • Malinga na mawu a Yesu, tingawadziŵe bwanji Akhristu “amene ali kumbali ya coonadi”?

5. Amalalikila coonadi ca m’Baibo

Akhristu oyambilila anali kulalikila kwa ena

Yesu asanapite kumwamba, anapatsa otsatila ake nchito imene ikucitikabe mpaka pano. Ŵelengani Mateyu 28:19, 20, komanso Machitidwe 1:8, na kukambilana funso ili:

  • Kodi nchito yolalikila iyenela kucitika mpaka liti komanso kufika kuti?

6. Amacita zimene amalalikila

N’ciyani cinakhutilitsa munthu wina, dzina lake Tom, kuti wapeza Akhristu enieni? Tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso otsatila.

  • Mu vidiyo iyi, n’ciyani cinapangitsa Tom kuleka kukhulupilila za cipembedzo?

  • N’cifukwa ciyani lomba ni wokhutila kuti anapeza coonadi?

Anthu amaona zimene umacita kuposa zimene umakamba. Ŵelengani Mateyu 7:21, na kukambilana funso ili:

  • Kodi cofunika kwambili kwa Yesu n’ciyani—kukamba kuti timakhulupilila zakuti-zakuti, kapena kuonetsa mwa zocita zathu zimene timakhulupilila?

7. Amakondana wina na mnzake

Akhristu oyambilila anali kukondana wina na mnzake

Kodi zacitikapodi kuti Akhristu n’kuika miyoyo yawo paciopsezo kuti apulumutse Akhristu anzawo? Tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso otsatila.

  • Mu vidiyo iyi, n’ciyani cinapangitsa M’bale Likhwide kuika moyo wake paciopsezo kuti apulumutse M’bale Johansson?

  • Muona bwanji, kodi iye anacita zinthu monga Mkhristu weniweni?

Ŵelengani Yohane 13:34, 35, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi ophunzila a Yesu (Akhristu enieni) ayenela kucita motani kwa anthu a mtundu wina kapena dziko lina?

  • Nanga pa nthawi ya nkhondo angacitenso bwanji zimenezo?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Akhristu onse amalambila Mulungu mmodzi—conco palibe vuto kupemphela ku chalichi iliyonse”

  • Ni lemba liti limene mungaŵelengele munthu lothandiza kuzindikila Akhristu enieni?

CIDULE CAKE

Akhristu oona amatsatila zimene Baibo imaphunzitsa, amaonetsa cikondi codzimana, komanso amalalikila coonadi ca m’Baibo.

Mafunso Obweleza

  • Kodi zimene Akhristu enieni amakhulupilila zimatsamila pa ciyani?

  • Ni khalidwe lanji limene ndiye cizindikilo cowadziŵila Akhristu enieni?

  • Kodi Akhristu enieni amacita nchito yanji?

Colinga

FUFUZANI

Dziŵani zambili zokhudza anthu amene amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu Khristu na ziphunzitso zake.

Mboni za Yehova—Kodi Ndife Anthu Otani? (1:13)

Onani cinathandiza amene anali sisitere kupeza “banja lauzimu.”

“Anali Kugwilitsa Nchito Baibo Poyankha Funso Lililonse!” (Nsanja ya Mlonda, April 1, 2014)

Onani mmene Akhristu enieni amaonetsela cikondi kwa olambila anzawo ofunikila thandizo.

Kuthandiza Abale Athu Pakagwa Tsoka—Mbali Yake (3:57)

Onani mmene Akhristu oyambilila, komanso Akhristu enieni masiku ano, amaonetsela cizindikilo codziŵila otsatila a Yesu, cimene Yesu anachula.

“Kodi Mungawadziŵe Bwanji Akhristu Oona?” (Nsanja ya Mlonda, March 1, 2012)