Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 24

Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?

Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?

Yehova amafuna kuti tidziŵe za banja lake la kumwamba. Banja limenelo ni la angelo, ochedwa “ana a Mulungu.” (Yobu 38:7) Kodi Baibo imakamba ciyani za angelo? Kodi iwo amacita ciyani? Ndipo kodi angelo onse ali m’banja la Mulungu?

1. Kodi Angelo Ndani?

Yehova anayamba walenga angelo asanapange dziko lapansi. Mofanana na Mulungu, iwo ni anthu auzimu osaoneka okhala kumwamba. (Aheberi 1:14) Angelowo ali mamiliyoni ambili-mbili kumwambako, ndipo aliyense ni wosiyana na mnzake. (Chivumbulutso 5:11) Iwo amacita “zimene Yehova wanena mwa kumvela malamulo ake.” (Salimo 103:20) M’nthawi zamakedzana, Yehova nthawi zina anali kutumiza angelo ake kukapeleka mauthenga kwa anthu ake, kapena kukawathandiza, kapenanso kukawapulumutsa. Masiku ano, angelo amatsogolela Akhristu kwa anthu ofuna kuphunzila za Mulungu.

2. Kodi Satana na ziŵanda zake ndani?

Angelo ena anamupandukila Yehova. Mngelo woyamba kupanduka anali “iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Satana anali kufuna ulamulilo, conco ananyengelela anthu aŵili oyambawo, komanso angelo ena, kuti agwilizane naye pa kupandukila Mulungu. Angelo amene anapanduka amenewo amachedwa ziŵanda. Yehova anawapitikitsa kumwamba n’kuwagwetsela padziko lapansi, ndipo pothela pake adzawawonongelatu.—Ŵelengani Chivumbulutso 12:9, 12.

3. Kodi Satana na Ziŵanda zake amayesa bwanji kutisoceletsa?

Satana na ziŵanda zake amasoceletsa anthu ambili kupitila mu zamizimu, zimene ni mcitidwe woipa woyesa kukambilana na mizimu. Mwacitsanzo, anthu ena amafunsila kwa openda nyenyezi, olosela zam’tsogolo, owombeza, komanso kwa asing’anga. Ena amafuna cithandizo ca mankhwala coloŵetsapo zamizimu. Ndiponso anthu amanamizidwa kuti akhoza kukambilana na anthu amene anafa. Koma Yehova amaticenjeza kuti: “Musatembenukile kwa olankhula ndi mizimu ndipo musafunsile olosela zam’tsogolo.” (Levitiko 19:31) Amatipatsa cenjezo limeneli pofuna kutiteteza kwa Satana na ziŵanda zake. Iwo ni adani a Mulungu, ndipo amafuna kuticita zoipa.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phuzilani zinthu zabwino zimene angelo amacita, kuopsa kwa zamizimu, na mmene tingadzitetezele kwa Satana na ziŵanda zake.

4. Angelo amathandiza anthu kuphunzila za Yehova

Angelo a Mulungu salalikila mwacindunji kwa anthu. M’malo mwake, amatsogolela alambili a Mulungu kwa anthu ofuna kuphunzila za iye. Ŵelengani Chivumbulutso 14:6, 7, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani tifunikila thandizo la angelo polalikila?

  • Kodi zimakulimbikitsani kudziŵa kuti angelo akhoza kukutsogolelani kwa anthu ofuna kumva za m’Baibo? Cifukwa ciyani?

5. Pewani zamizimu

Satana na ziŵanda zake ni adani a Yehova. Iwo alinso adani kwa ife. Ŵelengani Luka 9:38-42, na kukambilana funso ili:

  • Kodi ziŵanda zimacita ciyani kwa anthu?

Tisadziitanile tokha ziŵanda mu umoyo wathu. Ŵelengani Deuteronomo 18:10-12, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi ziŵanda zimayesa kutikopa na kukambilana nafe m’njila ziti? Nanga kwanuko anthu amakonda kulankhula na ziŵanda m’njila ziti?

  • Kodi inu mukuona kuti n’cinthu cabwino kuti Yehova amaletsa kucitako zamizimu? Cifukwa ciyani?

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

  • Kodi mukuona kuti cithumwa cimene Palesa anaveka mwana wake padzanja ndico cinabweletsa vutolo? Cifukwa ciyani?

  • Kodi Palesa anayenela kucita ciyani kuti onse atetezeke ku ziŵanda?

Akhristu enieni nthawi zonse akhala akuzitsutsa ziŵanda. Ŵelengani Machitidwe 19:19, komanso 1 Akorinto 10:21, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani muyenela kuwononga cinthu ciliconse cokhudza zamizimu?

6. Pambanani nkhondo yolimbana na Satana komanso ziŵanda zake

Satana ndiye amalamulila ziŵanda. Koma angelo okhulupilika amatsogoleledwa na mngelo wamkulu Mikayeli, dzina lina la Yesu. Kodi Mikayeli ali na mphamvu zoculuka bwanji? Ŵelengani Chivumbulutso 12:7-9, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi amene ali na mphamvu zambili ndani, Mikayeli na angelo ake, kapena Satana na ziŵanda zake?

  • Kodi muganiza otsatila a Yesu ayenela kumuopa Satana na ziŵanda zake?

Mukhoza kupambana nkhondo yolimbana na Satana na ziŵanda zake. Ŵelengani Yakobo 4:7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mungadziteteze bwanji kwa Satana na ziŵanda zake?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Palibe vuto kucitako maseŵelo a zamizimu, kapena kutamba mafilimu ake. Zangokhala zosangalatsa cabe.”

  • N’cifukwa ciyani maganizo amenewa ni olakwika?

CIDULE CAKE

Angelo okhulupilika amatithandiza. Koma Satana na ziŵanda zake ni adani a Yehova, ndipo iwo amaseŵezetsa zamizimu kusoceletsa anthu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi angelo a Yehova amathandiza bwanji anthu kuphunzila za iye?

  • Kodi Satana na ziŵanda zake ndani?

  • N’cifukwa ciyani muyenela kutalikilana nazo zamizimu?

Colinga

FUFUZANI

Onani umboni woonetsa kuti Yesu ndiye mngelo wamkulu, Mikayeli.

“Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani umboni wotsimikizila kuti Mdyelekezi si maganizo cabe oipa mumtima mwa munthu.

“Kodi Mdyerekezi Alipodi?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani mmene mayi wina anamasukila ku ziŵanda.

“Anapeza Chifuno cha Moyo” (Nsanja ya Olonda, July 1, 1993)