Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 29

Kodi Munthu Akamwalila, Cimacitikano N’ciyani?

Kodi Munthu Akamwalila, Cimacitikano N’ciyani?

Kodi munataikilidwapo wokondedwa wanu mu imfa? Pa nthawi yacisoni imeneyi, mungadzifunse kuti: ‘N’ciyani cimacitika munthu akamwalila? Kodi pali ciyembekezo ciliconse cakuti tidzaonananso na okondedwa athu amene anamwalila?’ M’phunzilo lino komanso lotsatila, mudzapeza mayankho a m’Baibo otonthoza.

1. N’ciyani cimacitika munthu akamwalila?

Yesu anafanizila imfa na tulo tofa nato. Kodi imfa imafanana bwanji na tulo? Munthu amene ali m’tulo tofa nato sadziŵa zimene zikucitika. Munthu akamwalila, sangamve kupweteka kulikonse, ngakhalenso kusungulumwa, kutanthauza kuti sangathe kuyewa mabwenzi ake, olo abululu ŵake. Baibo imakamba kuti: “Akufa sadziŵa ciliconse.”—Ŵelengani Mlaliki 9:5.

2. Kodi timapindula bwanji tikadziŵa zoona ponena za imfa?

Anthu ambili amaopa kufa—ndipo amaopa ngakhale anthu akufa! Koma zimene Baibo imakamba ponena za imfa zingakucotseni mantha otelowo. Yesu anati: “Coonadi cidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Mosiyana na zimene zipembedzo zina zimaphunzitsa, Baibo siiphunzitsa zakuti munthu ali na mzimu umene sumafa akamwalila. Conco, palibe aliyense amene amavutika akamwalila. Komanso, popeza anthu akufa sadziŵa ciliconse, iwo sangativulaze. Cotelo, palibe cifukwa colambilila akufa kapena kuwapemphelela.

Anthu ena amakamba kuti angakambilane na anthu amene anamwalila. Koma zimenezi n’zosatheka. Monga mmene taphunzilila, anthu “akufa sadziŵa ciliconse.” Anthu amene amaganiza kuti amakambilana na okondedwa awo amene anafa, m’ceniceni amakambilana na ziŵanda zimene zimadziyelekezela kukhala aja anamwalila. Conco, kudziŵa zoona za akufa kumatiteteza ku ziŵanda. Yehova amaticenjeza kuti tisayese ngakhale pang’ono kukambilana na anthu akufa, cifukwa adziŵa kuti kugwilizana na ziŵanda n’kovulaza.—Ŵelengani Deuteronomo 18:10-12.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani zambili zimene Baibo imaphunzitsa ponena za akufa, ndipo limbitsani cikhulupililo canu mwa Mulungu wacikondi amene sazunza akufa.

3. Dziŵani zoona zokhudza mkhalidwe wa akufa

Kuzungulila dziko lonse lapansi, anthu amakhulupilila zosiyana-siyana pa zimene zimacitika munthu akamwalila. Komabe, si zikhulupililo zonse zingakhale zoona.

  • Kodi anthu ambili kwanuko amakhulupilila zotani ponena za akufa?

Kuti mudziŵe zimene Baibo imaphunzitsa, tambani VIDIYO.

Ŵelengani Mlaliki 3:20, na kukambilana mafunso aya:

  • Mogwilizana na vesiyi, n’ciyani cimacitika munthu akamwalila?

  • Kodi lembali lionetsa kuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukakhala na moyo kwina?

Baibo imatiuza za imfa ya Lazaro, mnzake wa Yesu wapamtima. Pamene muŵelenga Yohane 11:11-14, onani zimene Yesu anakamba zokhudza imfa ya Lazaro. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Yesu anayelekezela imfa na ciyani?

  • Kodi kuyelekezela kumeneku kutiuza ciyani za mkhalidwe wa akufa?

  • Muona bwanji, kodi zimene Baibo yafotokoza ponena za imfa n’zomveka kwa inu?

4. Kudziŵa zoona ponena za imfa kumatipindulitsa

Tikadziŵa zenizeni ponena za imfa timaleka kuopa akufa. Ŵelengani Mlaliki 9:10, na kukambilana funso ili:

  • Kodi akufa angaticite coipa ciliconse?

Coonadi ca m’Baibo cimatitetezanso ku bodza lakuti tiyenela kumacita zinthu zosangalatsa akufa kapena kuwalambila. Ŵelengani Yesaya 8:19 komanso Chivumbulutso 4:11, na kukambilana funso ili:

  • Muganiza Yehova amamva bwanji akaona wina wake akulambila munthu amene anafa, kapena kufuna cithandizo kwa iye?

Kudziŵa zenizeni zokhudza imfa kumatimasula ku miyambo imene Yehova sakondwela nayo

5. Kudziŵa zenizeni zokhudza imfa kumatilimbikitsa

Anthu ambili amaphunzitsidwa kuti akadzamwalila adzalangidwa cifukwa ca zoipa zimene anacita ali moyo. Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti palibe munthu amene amavutika mwa njila iliyonse akamwalila, ngakhale amene anacita zoipitsitsa kwambili. Ŵelengani Aroma 6:7, na kukambilana funso ili:

  • Monga taŵelengela m’Baibo kuti imfa imafafaniza machimo, kapena kuti kumasula munthu ku ucimo, kodi muganiza kuti anthu ena akafa amakalangidwa cifukwa ca macimo amene anacita ali moyo?

Tikamafika pomudziŵa bwino Yehova, timazindikilanso kuti sizingacitike olo pang’ono kuti iye azunze anthu amene anafa. Ŵelengani Deuteronomo 32:4, komanso 1 Yohane 4:8, kenako kambilanani mafunso aya:

  • Kodi n’zotheka kuti Mulungu wa makhalidwe amene achulidwa m’mavesi aya, angakonde kuti anthu amene anamwalila azizunzidwa?

  • Kodi kudziŵa zenizeni zokhudza imfa kwakulimbikitsani? Cifukwa ciyani?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nimacita mantha kuti anthu ena amene anamwalila anganicite zoipa.”

  • Kodi ni Malemba olimbikitsa ati amene mungamuŵelengele?

CIDULE CAKE

Munthu akamwalila, moyo wake umatha. Akufa sakuvutika m’njila iliyonse, komanso sangacitile coipa amoyo.

Mafunso Obweleza

  • Kodi tikamwalila, cimacitika pambuyo pake n’ciyani?

  • Kodi kudziŵa zenizeni ponena za imfa kumatipindulitsa bwanji?

  • Kodi kudziŵa zenizeni ponena za imfa kumatilimbikitsa bwanji?

Colinga

FUFUZANI

Fufuzani ngati n’zoona kuti Mulungu amalangadi anthu oipa m’moto ku helo.

Kodi Mulungu Amawotcha Anthu Kumoto? (3:07)

Kodi akufa tiyenela kuwaopa konse?

Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi? (bulosha)

Onani mmene munthu wina zinamulimbikitsila atadziŵa zenizeni zimene zimacitika tikamwalila.

Ndinasangalala Ndi Mayankho Omveka Bwino a m’Baibulo” (Nsanja ya Mlonda, March 1, 2015)