Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 30

N’zotheka Okondedwa Anu Kudzakhalanso na Moyo!

N’zotheka Okondedwa Anu Kudzakhalanso na Moyo!

Imfa imabweletsa cisoni cacikulu kwa ife anthu. Ndiye cifukwa cake Baibo imati imfa ni mdani. (1 Akorinto 15:26) M’phunzilo 27, munaphunzila zakuti Yehova adzamugonjetsa mdani ameneyu. Koma kodi n’ciyani cidzacitike kwa anthu amene anamwalila? M’phunzilo lino, mudzaphunzila zambili ponena za lonjezo lina losangalatsa limene Yehova anapeleka, lakuti iye adzaukitsa anthu mabiliyoni kuti akasangalale na moyo kwamuyaya. Kodi zimenezi zidzacitikadi? Kodi amenewo akadzaukitsidwa, akakhala kumwamba kapena padziko lapansi?

1. Kodi Yehova akulakalaka kudzacita ciyani kwa anthu amene timakonda omwe anamwalila?

Yehova ni wofunitsitsa kudzaukitsa anthu amene anamwalila. Munthu wokhulupilila Yobu anali na cidalilo cakuti Mulungu sadzamuiŵala akadzamwalila. Iye anauza Mulungu kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha [kucokela ku Manda].”—Ŵelengani Yobu 14:13-15.

2. Kodi tidziŵa bwanji kuti akufa angaukitsidwe?

Pamene Yesu anali padziko lapansi, Mulungu anam’patsa mphamvu zoukitsa akufa. Yesu anaukitsa mtsikana wa zaka 12, komanso mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye. (Maliko 5:41, 42; Luka 7:12-15) Patapita nthawi, Lazaro mnzake wa Yesu anamwalila. Ngakhale kuti Lazaro anakhala m’manda kwa masiku anayi, Yesu anamuukitsa n’kukhalanso na moyo. Atapemphela kwa Mulungu, Yesu anafuula mokweza mawu moyang’ana mandawo kuti, “Lazaro, tuluka!” Ndipo “amene anali wakufa uja anatuluka,” wamoyo! (Yohane 11:43, 44) Tangoganizilani cisangalalo cimene acibale a Lazaro komanso mabwenzi ake anakhala naco!

3. Kodi pali ciyembekezo cotani ponena za okondedwa anu amene anamwalila?

Baibo imalonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka” kwa akufa. (Machitidwe 24:15) Anthu amene Yesu anaukitsa kumbuyoku sanapite kumwamba. (Yohane 3:13) Iwo anakondwela kwambili kuona kuti akhalanso na moyo pom’mpano padziko lapansi. Mofananamo, Yesu posacedwa adzaukitsa mabiliyoni a anthu kuti adzakhalenso na moyo wacimwemwe kwamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. Iye ananena kuti “onse ali m’manda acikumbutso”—ngakhale amene angaoneke monga anaiŵalika, koma ali m’maganizo mwa Mulungu, adzaukitsidwa.—Yohane 5:28, 29.

KUMBANI MOZAMILAPO

Ŵelengani umboni wa m’Baibo woonetsa kuti akufa adzaukitsidwadi. Phunzilani mmene ciyembekezo ca kuuka kwa akufa cingakupatsileni citonthozo.

4. Yesu anaonetsa kuti akhoza kuukitsa akufa

Dziŵani zambili pa zimene Yesu anacitila bwenzi lake Lazaro. Ŵelengani Yohane 11:14, 38-44, na kukambilana mafunso aya:

  • Tidziŵa bwanji kuti Lazaro anamwaliladi? Onani vesi 39.

  • Kukanakhala kuti Lazaro anapitadi kumwamba atamwalila, kodi muganiza Yesu akanamubwezanso padziko lapansi?

Tambani VIDIYO.

5. Anthu ambili adzaukitsidwa!

Ŵelengani Salimo 37:29, na kukambilana funso ili:

  • Kodi anthu mabiliyoni amene adzaukitsidwe adzakhala kuti?

Yesu adzaukitsanso anthu ena ambili, osati cabe amene anali kulambila Yehova. Ŵelengani Machitidwe 24:15, na kukambilana funso ili:

  • Ndani amene mungakonde kudzaona ataukitsidwa?

Ganizilani izi: Yesu adzaukitsa anthu mosavuta mmene tate angautsile mwana wake ku tulo

6. Ciyembekezo ca ciukitso cingatipatse citonthozo

Nkhani ya m’Baibo ya mwana wamkazi wa Yairo yalimbikitsa anthu ambili ofeledwa na kuwatonthoza. Ŵelengani za nkhani imeneyi pa Luka 8:40-42, 49-56.

Yesu asanaukitse mwana wamkazi wa Yairo, anamuuza kuti: “Usaope, ingokhala ndi cikhulupililo basi.” (Onani vesi 50.) Kodi kudziŵa kuti akufa adzauka kungakuthandizeni bwanji pamene  . . .

  • munthu amene mukonda wamwalila?

  • moyo wanu uli pa ciopsezo?

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi ciyembekezo cakuti kudzakhala ciukitso cinawalimbikitsa bwanji makolo a Phelicity na kuwatonthoza?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nkhani yakuti akufa adzauka ni yovuta kuikhulupilila.”

  • Nanga inu muganiza bwanji?

  • Kodi munthu mungamuŵelengele lemba liti pomutsimikizila kuti ciukitso cidzakhalakodi?

CIDULE CAKE

Baibo imalonjeza kuti anthu mabiliyoni amene anamwalila adzaukitsidwa. Cifukwa Yehova amafuna kuti anthuwo adzakhalenso na moyo, iye anapatsa Yesu mphamvu zowaukitsa.

Mafunso Obweleza

  • Timadziŵa bwanji kuti Yehova na Yesu akuyembekezela mwacidwi kudzaukitsa akufa?

  • Kodi anthu mabiliyoni amene adzaukitsidwe adzakhala kuti—kumwamba kapena padziko lapansi? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

  • N’ciyani cimakupangitsani kukhulupilila kuti anthu amene mumakonda omwe anamwalila adzakhalanso na moyo?

Colinga

FUFUZANI

Ŵelengani za masitepe amene mungatenge okuthandizani pamene muli pa cisoni.

Thandizo kwa Ofedwa” (Galamuka! Na. 3 2018)

Kodi mfundo za m’Baibo zingathandizedi munthu amene ali pa cisoni cofeledwa?

Munthu Amene Timakonda Akamwalila (5:06)

Kodi ana angathane bwanji na cisoni ca imfa ya bwenzi lokondedwa kapena wacibale?

Dipo (2:07)

Kodi munthu aliyense adzaukitsidwa kukakhala kumwamba? Nanga ndani amene sadzaukitsidwa?

“Kodi Ciukitso N’ciyani?” (Nkhani ya pawebusaiti)