Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 35

Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino

Mmene Tingapangile Zisankho Zabwino

Tonsefe timayenela kupanga zisankho. Ndipo zambili mwa zisankho zimene tingapange, zikhoza kukhudza kwambili umoyo wathu, komanso ubwenzi wathu na Yehova. Mwacitsanzo, tingafunikile kusankha malo okhala, njila yopezela ndalama, komanso kukwatila kapena kukwatiwa. Tikamapanga zisankho zabwino, tidzakhala na umoyo wacimwemwe komanso wokondweletsa Yehova.

1. Kodi Baibo ingakuthandizeni bwanji kupanga zisankho zabwino?

Musanapange cisankho, yambani mwapemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni. Kenako, fufuzani m’Baibo kuti mudziŵe mmene iye akuionela nkhaniyo. (Ŵelengani Miyambo 2:3-6.) Pa nkhani zina, Yehova amapeleka lamulo lacindunji lomveka bwino. Zikakhala conco, cisankho canzelu cimene muyenela kupanga ni kungotsatila lamulo limenelo.

Koma bwanji ngati palibe lamulo lacindunji la m’Baibo lokuuzani zocita? Yehova adzakutsogolelanibe mu “njila imene muyenela kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Kodi amacita zimenezo motani? Mwa kupeleka mfundo za m’Baibo zimene zingakutsogoleleni. Kodi mfundo za m’Baibo n’ciyani? Ni mfundo za coonadi zotiunikila maganizo a Mulungu na mmene amaonela zinthu. Nthawi zambili tikaŵelenga nkhani m’Baibo, timatha kudziŵa mmene Yehova akuionela nkhaniyo.

2. Kodi muyenela kuganizilanso ciyani musanapange cisankho?

Baibo imakamba kuti: “Wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.” (Miyambo 14:15) Izi zitanthauza kuti tisanapange cisankho kapena kuti cigamulo, tiyeni tiganizilenso njila zina zimene zingakhalepo. Pamene mukuganizila njila iliyonse, dzifunseni kuti, ‘Kodi ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingathandize pa nkhani imeneyi? Kodi ni njila iti imene inganipatse mtendele wa maganizo? Kodi cisankho cimene nifuna kupanga, cidzakhudza bwanji anthu ena? Koposa zonse, kodi cisankhoco cidzakondweletsa Yehova?’—Deuteronomo 32:29.

Yehova ndiye woyenela kutiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. Tikayamba kuwadziŵa bwino malamulo a Yehova na mfundo zake, maka-maka kuwatsatila, tidzakhala tikuphunzitsa cikumbumtima cathu. Cikumbumtima ni liwu la mumtima mwathu limene limatiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. (Aroma 2:14, 15) Cikumbumtima cophunzitsidwa bwino, cidzatithandizanso kupanga zisankho zabwino.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mmene mfundo za m’Baibo, na cikumbumtima, zimathandizila popanga zisankho.

3. Lolani kuti Baibo ikutsogoleleni

Kodi mfundo za m’Baibo zingatitsogolele motani popanga zisankho? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Kodi ufulu wodzisankhila zocita n’ciyani?

  • Nanga n’cifukwa ciyani Yehova anatipatsa ufulu wodzisankhila zocita?

  • Kodi iye anatipatsa ciyani cotithandiza kugwilitsa nchito bwino ufulu wodzisankhila zocita?

Kuti muone citsanzo ca mfundo za m’Baibo, ŵelengani Aefeso 5:15, 16. Ndiyeno kambilanani mmene mungagwilitse “nchito bwino nthawi yanu” kuti . . .

  • muziŵelenga Baibo nthawi zonse.

  • mukhale mnzake wa mu ukwati wabwino, kholo labwino, kapena mwana womvela.

  • muzipezeka pa misonkhano ya mpingo.

4. Phunzitsani cikumbumtima canu kupanga zisankho zabwino

Ngati pali lamulo la m’Malemba lomveka bwino pa nkhani inayake, kupanga cisankho cabwino kungakhale kosavuta. Koma bwanji ngati palibe lamulo lililonse? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi mlongoyu anatenga masitepe ati kuti aphunzitse cikumbumtima cake, komanso kupanga cisankho cokondweletsa Yehova?

N’cifukwa ciyani sitiyenela kupempha anthu ena kutipangila zisankho zimene ni udindo wathu kuzipanga? Ŵelengani Aheberi 5:14, na kukambilana mafunso aya:

  • Ngakhale kuti cingaoneke copepuka kupempha anthu ena kutipangila zisankho, kodi ni udindo wathu kusiyanitsa ciyani?

  • Kodi n’ciyani cingakuthandizeni kuphunzitsa cikumbumtima canu, na kupanga zisankho zabwino?

Monga mmene mapu imatilongozela kopita, cikumbumtima cimatitsogolela mu umoyo wathu

5. Lemekezani zikumbumtima za ena

Anthufe timapanga zisankho zosiyana-siyana. Koma kodi tingalemekeze bwanji zikumbumtima za ena? Onani zocitika ziŵili izi:

Cocitika Coyamba: Mlongo wina wokonda kuvala tufupi komanso tothina wasamukila ku mpingo kumene alongo ambili amakhumudwa na mavalidwe amenewo.

Ŵelengani Aroma 15:1, komanso 1 Akorinto 10:23, 24, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga na Malemba aya, kodi mlongoyu ayenela kucita motani? Kodi mungacite bwanji ngati munthu wina cikumbumtima cake cikumuletsa kucita cinthu cimene cikumbumtima canu cikukulolani kucita?

Cocitika Caciŵili: M’bale akudziŵa kuti Baibo siiletsa kumwako moŵa pamlingo wabwino, koma iye anapangabe cisankho ca kusamwa moŵa. M’baleyu waitanidwa kumaceza, ndipo akuona abale ena akumwa moŵa kumeneko.

Ŵelengani Mlaliki 7:16, komanso Aroma 14:1, 10, kenako kambilanani mafunso aya:

  • Malinga na Malemba aya, kodi m’bale ameneyu ayenela kucita motani? Kodi mungacite bwanji mukaona kuti munthu wina akucita cinthu cimene cikumbumtima canu cimakuletsani?

 Kodi ni masitepe ati othandiza kupanga zisankho zabwino?

1. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kudziŵa zocita.—Yakobo 1:5.

2. Fufuzani m’Baibo komanso m’zofalitsa zozikika m’Baibo, kuti mupeze mfundo zothandiza pa nkhaniyo. Komanso mungafunsile kwa Akhristu acidziŵitso.

3. Ganizilani mmene cisankho canu cingakhudzile cikumbumtima canu na zikumbumtima za anthu ena.

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Muli na ufulu wocita ciliconse cimene mufuna. Zimene ena angaganize zisakukhudzeni.”

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kuganizila mmene zocita zathu zimakhudzila Mulungu, komanso anthu ena?

CIDULE CAKE

Tikadziŵa mmene Yehova amaionela nkhani, timapanga zisankho zabwino. Ndipo tisanacite ciliconse tiyenela kuona ngati zimene tikufuna kucitazo zidzathandiza anthu ena kapena kuwavulaza.

Mafunso Obweleza

  • Kodi mungapange motani zisankho zokondweletsa Yehova?

  • Kodi mungaciphunzitse bwanji cikumbumtima canu?

  • Nanga mungaonetse bwanji kuti mumalemekeza zikumbumtima za anthu ena?

Colinga

FUFUZANI

Kodi mungapange bwanji zisankho zolimbikitsa ubwenzi wanu na Mulungu?

“Pangani Zisankho Zimene Zimalemekeza Mulungu” (Nsanja ya Mlonda, April 15, 2011)

Mvetsetsani mmene Yehova amatipatsila malangizo.

Yehova Amatsogolela Anthu Ake (9:50)

Onani zimene zinathandiza munthu wina kupanga cisankho covuta.

Yehova Akulonjeza Kutipatsa Zonse Zabwino (5:46)

Dziŵani mmene mungakondweletsele Yehova, pamene sanapeleke malangizo acindunji pa nkhani inayake.

“Kodi Mumafunikila Lamulo la m’Baibo Nthawi Zonse?” (Nsanja ya Mlonda, December 1, 2003)