Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 41

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kugonana?

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kugonana?

Anthu ambili amacita manyazi kukambilana nkhani ya kugonana. Koma Baibo ikamanena za kugonana imakamba mosapita m’mbali, komabe mwaulemu. Ndipo zimene imakamba zimakhala zaphindu kwa ife. Zimenezi n’zomveka cifukwa Yehova ndiye anatilenga. Iye amadziŵa zimene zingatipindulile bwino kwambili. Amatiuzanso zimene tiyenela kucita kuti timusangalatse, na zimene zingatithandize kuti tikondwele na moyo kwamuyaya.

1. Kodi Yehova Amaiona bwanji nkhani ya kugonana?

Kugonana ni mphatso yabwino kwambili imene Yehova anakonzela anthu. Iye amafuna kuti mwamuna na mkazi wake azisangalala nayo mphatso imeneyi. Mphatso ya kugonana imeneyi imalola okwatilana kubeleka ana. Komanso, ni njila imene aŵiliwo amaonetselana cikondi m’njila yoyenela yacibadwa, komanso yopatsa cisangalalo. Ndiye cifukwa cake Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.” (Miyambo 5:18, 19) Yehova amafuna kuti Akhristu okwatilana azikhala okhulupilika kwa wina na mnzake. Akatelo, adzapewelatu kucita cigololo.—Ŵelengani Aheberi 13:4.

2. Kodi ciwelewele n’ciyani?

Baibo imatiuza kuti “adama sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Olemba Baibo mu Cigiriki anagwilitsa nchito liwu lakuti por-nei’a pofotokoza khalidwe la ciwelewele. Liwu lakuti por-nei’a limatanthauza (1) kugonana a kwa anthu osakwatilana, (2) kugonana kwa anthu ofanana ziwalo (mathanyula), ndipo (3) kugona nyama. Ngati tipewa dama tidzakondweletsa Yehova, ndiponso tidzakhala na moyo waphindu.—1 Atesalonika 4:3.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani mmene mungapewele zaciwelewele, komanso mapindu amene mungapeze ngati mukhala oyela m’makhalidwe.

3. Thaŵani ciwelewele

Mnyamata wina wokhulupilika, Yosefe, anakanitsitsa zakuti agone na mkazi wa mwiniwake pofuna kukhala woyela m’makhalidwe. Ŵelengani Genesis 39:1-12, na kukambilana mafunso aya:

  • N’ciyani cinalimbikitsa Yosefe kuti athaŵe? Onani vesi 9.

  • Kodi muganiza kuti Yosefe anapanga cisankho canzelu? Cifukwa ciyani?

Kodi acinyamata masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca Yosefe cothaŵa ciwelewele? Tambani VIDIYO.

Yehova amafuna kuti tizipewa zaciwelewele. Ŵelengani 1 Akorinto 6:18, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi ni zocitika ziti zimene zingapangitse munthu kuti acite ciwelewele?

  • Kodi mungacithaŵe bwanji ciwelewele?

4. Mukhoza kuwagonjetsa mayeselo

Kodi n’ciyani cingapangitse kuti zikhale zovuta kupewa mayeselo ocita ciwelewele? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi m’bale wa mu vidiyo iyi, anacita ciyani atazindikila kuti maganizo ake na zocita zake zidzapangitsa kuti asakhale wokhulupilika kwa mkazi wake?

Ngakhale kwa Akhristu okhulupilika, nthaŵi zina cimakhala covuta kusungabe maganizo awo ali oyela. Kodi mungacite ciyani kuti mupewe kumangoganizila zinthu zoipa? Ŵelengani Afilipi 4:8, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi tiyenela kumaika maganizo athu pa zinthu zotani?

  • Kodi kuŵelenga Baibo komanso kukhala wotangwanika potumikila Yehova, kungatithandize bwanji kuti tipewe mayeselo amene angaticimwitse?

5. Malamulo a Yehova amatipindulitsa

Yehova ndiye amadziŵa bwino zimene timafunikila. Iye amatiuza mmene tingakhalile na makhalidwe oyela komanso mapindu amene tingapeze tikatelo. Ŵelengani Miyambo 7: 7-27 kapena Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Kodi wacinyamatayu anadziloŵetsa bwanji m’mayeselo? Onani Miyambo 7:8, 9.

  • Malinga na Miyambo 7:23, 26, khalidwe laciwelewele lingatigwetsele m’mavuto aakulu. Ngati tili na makhalidwe oyela, kodi tingapewe mavuto ati?

  • Kodi makhalidwe oyela angatithandize bwanji kukondwela na moyo kwamuyaya?

Anthu ena amaona kuti zimene Baibo imakamba pa nkhani ya mathanyula, kapena kuti kugonana kwa anthu ofanana ziwalo, ni nkhanza. Koma Yehova Mulungu wacikondi amafuna kuti aliyense akondwele na moyo kwamuyaya. Kuti zimenezi zitheke tiyenela kusunga malamulo ake. Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11, na kukambilana funso ili:

  • Kwa Mulungu, kodi mathanyula ndiwo khalidwe lokha limene tiyenela kupewa?

Kuti timukondweletse Mulungu, tonsefe tiyenela kupanga masinthidwe pa umoyo wathu. Ngati talimbikila kutelo, tidzapindula. Ŵelengani Salimo 19:8, 11, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi muganiza kuti malamulo a Yehova pa makhalidwe abwino ni ovuta kwambili kuwatsatila? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Yehova wathandiza anthu ambili kutsatila malamulo ake pa umoyo wawo. Inunso angakuthandizeni

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Palibe vuto anthu aŵili alionse kugonana, malinga ngati amakondana.”

  • Nanga inu muona bwanji?

CIDULE CAKE

Kugonana ni mphatso yabwino kwambili imene Yehova anapeleka kwa mwamuna na mkazi wake kuti azisangalala nayo.

Mafunso Obweleza

  • Kodi ciwelewele cimaphatikizapo macitidwe otani?

  • Kodi n’ciyani cingatithandize kupewa mcitidwe waciwelewele?

  • Kodi timapindula bwanji ngati titsatila malamulo a Yehova pa makhalidwe abwino?

Colinga

FUFUZANI

Onani cifukwa cake Mulungu amafuna kuti mwamuna na mkazi azimangitsa ukwati, m’malo mongotengana cabe.

“Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?”(Nkhani ya pawebusaiti)

Onani cifukwa cake mfundo ya m’Baibo yoletsa mathanyula siitanthauza kuti anthuwo tizidana nawo.

“Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Dziŵani mmene malamulo a Mulungu pa nkhani ya kugonana amatitetezela.

“Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Mu nkhani yakuti “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri,” Onani cinalimbikitsa mwamuna wina wocita zamathanyula kusintha moyo wake kuti akondweletse Mulungu.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2011)

a Macitidwe osayenela amenewa amaphatikizapo kugonana m’kamwa, kugonana kumbuyo, komanso kuseŵeletsa malisece a munthu wina.