Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 42

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Umbeta na Ukwati?

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Umbeta na Ukwati?

Ku madela ena, anthu amakhulupilila kuti munthu angakhale wosangalala kokha ngati waloŵa m’banja. Komabe, sikuti onse ali pa banja ali na cimwemwe, komanso sikuti mbeta zonse zilibe cimwemwe. Ndiye cifukwa cake Baibo imaonetsa kuti umbeta, komanso ukwati, zonse ni mphatso zocokela kwa Mulungu.

1. Kodi umbeta uli na mapindu otani?

Baibo imati: “Amene walekana ndi moyo wokhala yekha n’kulowa m’banja wacita bwino, koma amene sanalowe m’banja wacita bwino koposa.” (Ŵelengani 1 Akorinto 7:32, 33, 38.) Kodi munthu amene ni mbeta amacita “bwino koposa” pa mbali ziti? Akhristu amene ni mbeta amakhala alibe nkhawa yosamalila zosoŵa za mnzawo wa mu ukwati. Motelo, iwo amakhala na ufulu wokulilapo. Mwacitsanzo, ena amawonjezela utumiki wawo m’njila zosangalatsa, monga kupita ku madela ena kukathandiza nchito yolalikila uthenga wabwino. Coposa zonse, iwo amakhala na nthawi yoculuka yolimbitsa ubwenzi wawo na Yehova.

2. Kodi kukwatilana mwalamulo kuli na mapindu otani?

Monga mmene zilili na umbeta, ukwati nawonso umabweletsa mapindu abwino kwambili. Baibo imakamba kuti “awili amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Mfundo imeneyi ni yoona maka-maka kwa Akhristu amene amagwilitsa nchito mfundo za m’Baibo mu ukwati wawo. Okwatilana mwalamulo amalonjezana kuti adzakondana, kulemekezana, komanso kusamalilana wina na mnzake. Cifukwa ca zimenezi, iwo amadzimva otetezeka kuposa aja amene amangotengana osamangitsa ukwati. Komanso ukwati walamulo umakhala malo otetezeka olelelamo ana.

3. Kodi Yehova amauona bwanji ukwati?

Yehova pomangitsa ukwati woyamba anati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Genesis 2:24) Yehova amafuna kuti mwamuna na mkazi wake azikondana na kukhalila limodzi kwa moyo wawo wonse. Iye amalola kusudzulana pokhapo ngati mmodzi wa aŵiliwo wacita cigololo. Zikatelo, Yehova amalola wolakwilidwayo kusankha kuthetsa ukwatiwo kapena ayi. a (Mateyu 19:9) Cina, Yehova salola kuti Akhristu azikwatila cipali.—1 Timoteyo 3:2.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mmene mungakhalile wacimwemwe komanso wokondweletsa Yehova, kaya ndinu mbeta kapena muli pabanja.

4. Igwilitseni nchito mwanzelu mphatso ya umbeta

Yesu anaona kuti umbeta ni mphatso. (Mateyu 19:11, 12) Ŵelengani Mateyu 4:23, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Yesu anaseŵenzetsa bwanji mphatso ya umbeta wake, kutumikila Atate wake komanso kuthandiza anthu ena?

Akhristu amene ni mbeta akhoza kusangalala na umoyo wawo mmene Yesu anacitila. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi Akhristu amene ni mbeta angaseŵenzetse bwanji mphatso yawo imeneyo mwaphindu?

Kodi mudziŵa?

Baibo siikamba zaka zakubadwa zimene munthu ayenela kufikapo kuti aloŵe m’banja. Ngakhale n’conco, imalimbikitsa munthu kuti ayambe wayembekeza mpaka apitilile “pacimake pa unyamata.” Pacimake pa unyamata ni nyengo pamene cilakolako ca kugonana cimakhala camphamvu kwambili cakuti cingalepheletse wacinyamata kupanga zisankho zanzelu.—1 Akorinto 7:36.

5. Sankhani mwanzelu munthu wokwatilana naye

Kusankha munthu womanga naye banja ni nkhani yaikulu kwambili. Ŵelengani Mateyu 19:4-6, 9, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani Mkhristu sayenela kuthamangila kuloŵa m’banja?

Baibo ingakuthandizeni kudziŵa makhalidwe abwino a munthu amene mungakwatilane naye. Koma cofunika kwambili ni kupeza munthu amene amakonda Yehova. b Ŵelengani 1 Akorinto 7:39 na 2 Akorinto 6:14. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukwatilana na Mkhristu mnzathu cabe?

  • Kodi muganiza kuti Yehova angamve bwanji tikakwatilana na munthu amene sakonda Mulungu?

Mukamanga mujoko nyama ziŵili zosiyana kwambili, zonse zidzavutika. Mofananamo Mkhristu akamanga ukwati na munthu wosakhulupilila, adzakhala na mavuto ambili

6. Kuona ukwati mmene Yehova amauonela

Mu nthawi ya Aisiraeli akale, amuna ena anali kusudzula akazi awo pa zifukwa zadyela. Ŵelengani Malaki 2:13, 14, 16, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani Yehova amadana nako kuthetsa ukwati pa zifukwa zisali za m’Malemba?

Cigololo na kusudzulana zimam’pweteka kwambili wa mu ukwati wosalakwayo komanso ana awo

Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Ngati muli pa banja na munthu wosakhulupilila, kodi mungacite ciyani kuti ukwati wanu ukhale wopambana?

7. Sungani malamulo a Yehova mu ukwati wanu

Pafunikila khama kuti munthu azitsatila malamulo a Yehova mu ukwati. c Ndipo Yehova amadalitsa amene amayesetsa kutelo. Tambani VIDIYO.

Ŵelengani Aheberi 13:4, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi muganiza n’zotheka kutsatila malamulo a Yehova a mu ukwati? Mwayankha conco cifukwa ciyani?

Yehova amafuna kuti Akhristu akakwatilana kapena kusudzulana azilembetsa ku boma. M’maiko ambili, izi n’zimene malamulo amafuna. Ŵelengani Tito 3:1, na kukambilana funso ili:

  • Ngati muli pabanja, kodi mukutsimikiza kuti ukwati wanu ni wolembetsa ku boma?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’kwanji kumangitsa ukwati? Kodi mwamuna na mkazi sangangotengana n’kumakhalila limodzi?”

  • Kodi inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Umbeta komanso ukwati, zonse ni mphatso zocokela kwa Yehova. Anthu ali pabanja komanso mbeta, onse akhoza kukhala na umoyo wacimwemwe, malinga ngati acita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Yehova.

Mafunso Obweleza

  • Kodi munthu ayenela kucita motani kuti agwilitsile nchito mphatso yake ya umbeta mwanzelu?

  • N’cifukwa ciyani Baibo imatilangiza kukwatilana na Mkhristu mnzathu cabe?

  • Kodi pali cifukwa cimodzi cokha citi ca m’Malemba colola kuthetsa ukwati?

Colinga

FUFUZANI

Kodi kukwatila kokha “mwa Ambuye” kutanthauza ciyani?

“Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2004)

Tambani mavidiyo aŵili amene angakuthandizeni kupanga zisankho zabwino pa nkhani ya kukhala pacibwenzi komanso ukwati.

Kukonzekera Banja (11:53)

Onani cifukwa cake m’bale wina akuona kuti zimene Yehova wam’patsa n’zamtengo wapatali kuposa ciliconse cimene anasiya.

N’naganiza Kuti Mtsikanayo Angaphunzile Coonadi (1:56)

Ni zinthu ziti zimene munthu ayenela kuganizilapo mosamala asanapange cisankho ca kusudzulana kapena kusalana na mnzake wa mu ukwati?

“Muzilemekeza ‘Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi’” (Nsanja ya Mlonda, December 2018)

a Onani Mfundo yakumapeto 4 pa nkhani ya kusalana apaukwati (separation) ngati sipanacitike cigololo.

b Kumadela ena, makolo ndiwo amasankhila mwana wawo munthu wokwatilana naye. Zikakhala conco, makolo acikondi sayang’ana cuma cimene munthu ali naco, kapena kuchuka kwake iyayi. M’malo mwake, amafuna kudziŵa ngati munthuyo amakonda Yehova.

c Ngati munangotengana cabe na munthu amene simunamange naye ukwati, muyenela kupanga cisankho inu mwini, cokamangitsa naye ukwati kapena kusiyana naye.