Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 43

Kodi Nkhani ya Kumwa Moŵa Akhristu Ayenela Kuiona Bwanji?

Kodi Nkhani ya Kumwa Moŵa Akhristu Ayenela Kuiona Bwanji?

Padziko lonse lapansi, anthu ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani ya kumwa moŵa. Anthu ena amamwako nthaŵi zina poceza na anzawo. Ena amasankha kusamwa ngakhale pang’ono. Komanso pali anthu ena amene amamwa mpaka kuledzela. Koma kodi Baibo imakamba ciyani pa nkhani ya moŵa?

1. Kodi kumwa moŵa n’kulakwa?

Baibo siiletsa kumwa moŵa. M’malo mwake, pofotokoza mphatso zambili zimene Mulungu anatipatsa, Baibo imaphatikizapo “vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.” (Salimo 104:14, 15) Amuna ena okhulupilika ochulidwa m’Baibo, ngakhalenso akazi, anali kumwako moŵa.—1 Timoteyo 5:23.

2. Kodi Baibo imapeleka ulangizi wotani kwa amene amamwa moŵa?

Yehova amaletsa kumwa kwambili moŵa, komanso kuledzela amadana nako. (Agalatiya 5:21) Mawu ake amati: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambili.” (Miyambo 23:20) Conco, ngati tisankha kumwa moŵa, ngakhale tili kwatokha, tiyenela kusamala kuti tisamwe kwambili cakuti n’kulephela kuganiza bwino, kukangiwa kugwila lilime, kulephela kudziletsa pa zocita zathu, kapena kuika thanzi lathu paciopsezo. Ngati tiona kuti zikutivuta kudziletsa pa kamwedwe kathu, ni bwino kungoulekelatu moŵa.

3. Kodi tingalemekeze bwanji zisankho za ena pa nkhani ya moŵa?

Munthu aliyense ayenela kusankha yekha kumwa moŵa kapena kusamwa. Tisaweluze munthu amene wasankha kumwa moŵa pang’ono. Komanso, munthu amene wasankha kusamwa moŵa tisamukakamize kuti amwe. (Aroma 14:10) Ngati taona kuti ena angakhumudwe akationa tikumwa moŵa, ni bwino kusamwa. (Ŵelengani Aroma 14:21.) “Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—Ŵelengani 1 Akorinto 10:23, 24.

KUMBANI MOZAMILAPO

Pezani mfundo za m’Baibo zomwe zingakuthandizeni kuona ngati muyenela kumwa kapena ayi, na mlingo umene mungamwe. Cina, pezaninso zimene mungacite ngati muli na vuto la kamwedwe.

4. Pangani cisankho cakuti mudzamwa moŵa kapena ayi

Kodi Yesu anali na maganizo otani pa nkhani ya kumwa moŵa? Kuti mupeze yankho, ganizilani cozizwitsa coyamba cimene iye anacita. Ŵelengani Yohane 2:1-11, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga na cozizwitsa ici, kodi tingati Yesu moŵa amauona bwanji? Nanga anthu amene amamwa moŵa tingati amawaona bwanji?

  • Popeza Yesu sanaletse kumwa moŵa, kodi Mkhristu ayenela kumuona bwanji munthu amene amamwa moŵa?

Mkhristu aliyense ali na ufulu wa kumwa moŵa. Koma izi sizitanthauza kuti basi azimwa nthawi zonse iyayi. Ŵelengani Miyambo 22:3, ndiyeno ganizilani zocitika zili pansi izi, kuti mudziŵe ngati mungamwe moŵa kapena ayi:

  • Mudzayendetsa motoka kapena kuseŵenzetsa makina ena ake.

  • Muli na pathupi, kapena kuti ndinu woyembekezela.

  • Dokotala wakulangizani kuti musamamwe moŵa.

  • Mumalephela kudziletsa pakamwedwe.

  • Malamulo a dziko amakuletsani kumwa moŵa.

  • Muli na munthu wina amene safunanso kumwa moŵa cifukwa kumbuyoku anali na vuto la kamwedwe.

Kodi muyenela kupatsa anthu moŵa pacikwati, kapena pa zocitika zina zamaceza? Kuti mudziŵe mmene mungapangile cisankho cabwino, Tambani VIDIYO.

Ŵelengani Aroma 13:13, komanso 1 Akorinto 10:31, 32. Pambuyo poŵelenga lililonse la malemba aya, kambilanani funso ili:

  • Kodi kuseŵenzetsa mfundo ya pa lembali kungakuthandizeni bwanji kupanga cisankho cokondweletsa Yehova?

Mkhristu aliyense payekha, ayenela kupanga cisankho ca iyemwini pa nkhani ya kumwa moŵa. Ngakhale kuti amamwa moŵa, nthawi zina angasankhe kusamwa

5. Ikilan’tuni mlingo wa moŵa umene mufuna kumwa

Ngati mwasankha kumwa moŵa, kumbukilani izi: Ngakhale kuti Yehova saletsa kumwa moŵa, iye amati kumwa moŵa kwambili n’kulakwa. Cifukwa ciyani? Ŵelengani Hoseya 4:11,18, na kukambilana funso ili:

  • Kodi cingacitike n’ciyani munthu akamamwa moŵa kwambili?

N’ciyani cimene cingatithandize kuti tizipewa kumwa kwambili moŵa? Kukhala odzicepetsa na kuzindikila mlingo wathu. Ŵelengani Miyambo 11:2, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani n’cinthu canzelu kudziikila mlingo wa moŵa umene mungamwe?

6. Zimene zingathandize pa vuto la kamwedwe

Onani zimene zinathandiza munthu amene anali na vuto la kamwedwe. Tambani VIDIYO, kenako kambilana mafunso aya.

  • Malinga na zimene taona mu vidiyo, kodi moŵa unam’bweletsela mavuto otani Dmitry?

  • Kodi iye anangosiya kumwa moŵa kamodzi n’kamodzi?

  • Kodi pamapeto pake, n’ciyani cinam’thandiza kuleka kumwa moŵa mwaucidakwa?

Ŵelengani 1 Akorinto 6:10, 11, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi kuledzela ni colakwa coopsa motani?

  • N’ciyani cimaonetsa kuti munthu amene amamwa moŵa kwambili akhoza kusintha?

Ŵelengani Mateyu 5:30, na kukambilana funso ili:

  • Kudula dzanja pa lembali, kutanthauza kuyesetsa kusiya cinthu cina pofuna kukondweletsa Yehova. Kodi mungacite ciyani ngati zikukuvutani kucepetsako kamwedwe ka moŵa? a

Ŵelengani 1 Akorinto 15:33, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mabwenzi anu angakusintheni bwanji pa nkhani ya kumwa moŵa?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Kodi Baibo imaletsa kumwa moŵa?”

  • Kodi inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Yehova anapeleka moŵa kuti tizisangalala nawo. Ngakhale n’telo, iye amadana nako kumwa moŵa kwambili, ngakhalenso kuledzela.

Mafunso Obweleza

  • Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya kumwa moŵa?

  • Kodi kumwa moŵa kwambili kumabweletsa mavuto otani?

  • Kodi tingalemekeze bwanji zisankho za anthu ena pa nkhani ya kumwa moŵa?

Colinga

FUFUZANI

Kodi acinyamata akapange bwanji cisankho pa nkhani ya kumwa moŵa?

Ganizilani Zotulukapo za Kumwa Moŵa (2:31)

Onani zimene muyenela kucita kuti mugonjetse vuto la kamwedwe.

“Khalani na Maganizo Oyenela pa Nkhani ya Kumwa Moŵa” (Nsanja ya Mlonda, January 1, 2010)

Kodi Mkhristu ayenela kucitako tositi [kugundanitsa zomwela]?

“Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” (Nsanja ya Mlonda, February 15, 2007)

M’nkhani yakuti “Ndinkamwa Mowa Mwauchidakwa,” onani mmene mwamuna wina anasiyila kumwa moŵa mwaucidakwa.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2012)

a Aja amene anafika paucidakwa, angafunikile thandizo la akatswili kuti aleke. Madokotala ambili amakamba kuti, kwa aja ali na vuto la kamwedwe, ni bwino kungosiyilatu kumwa moŵa.