PHUNZIRO 43

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?

Anthu padzikoli amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mowa. Ena amasankha kumwa mowa ndi anzawo akamacheza. Pomwe ena amasankha kuti asamamwe mowa. Anthu enanso amamwa mowa n’kufika poledzera. Ndiye kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya mowa?

1. Kodi kumwa mowa n’kulakwa?

Baibulo silinena kuti kumwa mowa n’kulakwa. M’malomwake, likamanena za zinthu zabwino zambiri zimene Mulungu watipatsa, limatchulanso za “vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.” (Salimo 104:​14, 15) Ndipotu, amuna ndi akazi ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankamwa mowa.​—1 Timoteyo 5:23.

2. Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa amene asankha kumwa mowa?

Yehova amaletsa kumwa mowa mwauchidakwa komanso kuledzera. (Agalatiya 5:21) Mawu ake amati: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” (Miyambo 23:20) Choncho tikasankha kumwa mowa, ngakhale tili patokha, sitiyenera kumwa wambiri mpaka kufika polephera kuganiza bwino, kulephera kulankhula ndi kuchita zinthu zanzeru kapenanso kufika powononga thanzi lathu. Komabe, ngati zikutivuta kumwa mowa modziletsa, tingachite bwino kungosiyiratu.

3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene anthu ena anasankha pa nkhani ya mowa?

Munthu aliyense ayenera kusankha yekha ngati akufuna kumamwa mowa kapena ayi. Munthu wina akasankha kumwa mowa mosapitirira malire, tisamamuweruze. Komanso ngati wina wasankha kusamwa mowa, tisamamukakamize kuti ayambe kumwa. (Aroma 14:10) Komabe, tingasankhe kusamwa mowa ngati ena angakhumudwe kapena ngati kumwa mowa kungabweretse mavuto kwa anthu ena. (Werengani Aroma 14:21.) Timayesetsa kupewa kuchita zinthu ‘zopindulitsa ife tokha basi,’ koma timachita ‘zopindulitsanso anthu ena.’​—Werengani 1 Akorinto 10:23, 24.

FUFUZANI MOZAMA

Onani mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusankha kumwa mowa kapena ayi komanso kuchuluka kwa mowa womwe mungamamwe. Onaninso zomwe mungachite ngati muli ndi vuto lomwa mowa mosadziletsa.

4. Mungasankhe kumwa mowa kapena ayi

Kodi maganizo a Yesu anali otani pa nkhani ya mowa? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita. Werengani Yohane 2:1-11, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Malinga ndi zimene tawerengazi, kodi maganizo a Yesu ndi otani pa nkhani ya mowa, nanga amawaona bwanji anthu amene amasankha kumwa mowa?

  • Popeza Yesu saona kuti kumwa mowa n’kulakwa, kodi Mkhristu ayenera kumuona bwanji munthu amene wasankha kumwa mowa?

Ngakhale kuti Mkhristu ali ndi ufulu wosankha kumwa mowa, pa nthawi zina, singakhale nzeru kuchita zimenezi. Werengani Miyambo 22:3, kenako onani mmene mfundo zotsatirazi zingakuthandizireni kudziwa ngati muyenera kumwa mowa kapena ayi:

  • Ngati mukufunika kuyendetsa galimoto kapena kugwiritsa ntchito mashini enaake.

  • Ngati ndinu woyembekezera.

  • Ngati dokotala wakuuzani kuti musamwe mowa.

  • Ngati mumamwa mowa mosadziletsa.

  • Ngati lamulo lam’dziko lanu likukuletsani kumwa mowa.

  • Ngati muli ndi munthu amene wasankha kusamwa mowa chifukwa chakuti m’mbuyomo ankamwa mowa mosadziletsa.

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kudziwa ngati ndi zoyenera kukhala ndi mowa paphwando la ukwati kapena pa zochitika zina? Kuti mudziwe zoyenera kuchita, onerani VIDIYO.

Werengani Aroma 13:13 ndi 1 Akorinto 10:​31, 32. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:

  • Kodi kugwiritsa ntchito mfundo yamulembali kungakuthandizeni bwanji kusankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova?

Mkhristu aliyense amasankha yekha kumwa mowa kapena ayi. Ngakhale mkhristu yemwe amamwa mowa, nthawi zina angasankhe kusamwa

5. Ganizirani kuchuluka kwa mowa womwe mungamwe

Ngati mwasankha kumwa mowa, muzikumbukira mfundo iyi: Ngakhale kuti Yehova saletsa kumwa mowa, koma amaletsa kumwa mowa mwauchidakwa. N’chifukwa chiyani zimenezi zili choncho? Werengani Hoseya 4:11, 18, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chiyani chingachitike ngati munthu atamwa mowa wambiri?

N’chiyani chingatithandize kuti tisamwe mowa wambiri? Tiyenera kuzindikira malire athu n’kupewa kumwa mowa mopitirira muyezo. Werengani Miyambo 11:2, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani muyenera kudziikira malire a mowa womwe muyenera kumamwa?

6. N’chiyani chimene chingathandize munthu kusiya kumwa mowa mopitirira malire?

Onani zomwe zinathandiza munthu wina kusiya kumwa mowa mopitirira malire. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Dmitry ankatani akaledzera?

  • Kodi anakwanitsa kusiya kumwa mowa kamodzin’kamodzi?

  • N’chiyani chinamuthandiza kuti asiyiretu kumwa mowa mwauchidakwa?

Werengani 1 Akorinto 6:10, 11, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya kumwa mowa mwauchidakwa?

  • N’chiyani chikusonyeza kuti munthu yemwe amamwa mowa mopitirira malire akhoza kusintha?

Werengani Mateyu 5:30, kenako mukambirane funso ili:

  • Pamene Yesu amanena za kudula dzanja ankatanthauza kuti tiyenera kulolera kusiya kuchita zinazake ndi cholinga choti tisangalatse Yehova. Kodi mungatani ngati zikukuvutani kusiya kumwa mowa mwauchidakwa? a

Werengani 1 Akorinto 15:33, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi n’chiyani chimene chingakuchitikireni ngati mumacheza ndi anthu omwe amakonda kumwa mowa wambiri?

MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi kumwa mowa n’kulakwa?”

  • Kodi mungamuyankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Mowa ndi mphatso imene Yehova anatipatsa kuti tizisangalala. Koma iye safuna kuti tizimwa mowa wambiri kapena kuledzera.

Kubwereza

  • Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya mowa?

  • Kodi kumwa mowa wambiri kumabweretsa mavuto otani?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene anthu ena anasankha pa nkhani ya mowa?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi achinyamata angasankhe bwanji zinthu mwanzeru pa nkhani ya mowa?

Ganizirani Zimene Zingachitike Ngati Mutamwa Mowa (2:31)

Onani njira zimene muyenera kutsatira kuti muthane ndi vuto lomwa mowa mosadziletsa.

“Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2010)

Munkhani yakuti, “Ndinali Mbiyang’ambe,” onani zimene zinathandiza munthu wina kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2012)

a Anthu amene mowa unawalowerera kwambiri angafunike thandizo lachipatala kuti akwanitse kusiya. Ndipotu madokotala ambiri amanena kuti anthu amene anali ndi vuto limeneli sayenera kumwa mowa n’komwe.