Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 44

Kodi Zikondwerero Zonse Zimasangalatsa Mulungu?

Kodi Zikondwerero Zonse Zimasangalatsa Mulungu?

Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi moyo komanso amafuna kuti nthawi zina tizichita zikondwerero. Koma kodi ndi zikondwerero komanso maholide onse amene amasangalatsa Mulungu? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova posankha zoyenera kuchita pa nkhani imeneyi?

1. N’chifukwa chiyani zikondwerero zambiri sizisangalatsa Yehova?

Mungadabwe kudziwa kuti zikondwerero zambiri sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo zina zinayambitsidwa ndi zipembedzo zonyenga. Komanso zikondwerero zina zimakhala zokhudzana ndi zamizimu kapena zinayamba chifukwa cha chikhulupiriro chakuti pali chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira. Pali zinanso zimene zinayamba chifukwa chokhulupirira zaufiti kapena chikhulupiriro chakuti zinthu zina zimachitika chifukwa cha mwayi. (Yesaya 65:11) Choncho Yehova anachenjeza atumiki ake kuti: “Lekanani nawo, . . . Musakhudze chinthu chodetsedwa.”​—2 Akorinto 6:17. a

2. Kodi Yehova amamva bwanji akamaona anthu akuchita zikondwerero polemekeza anthu enaake?

Yehova amatichenjeza kuti tiyenera kupewa ‘kukhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi.’ (Werengani Yeremiya 17:5.) Pali maholide ena omwe anakhazikitsidwa pofuna kulemekeza olamulira kapena asilikali. Pamene ena amachita zikondwerero zokumbukira tsiku limene analandira ufulu wodzilamulira kapena zizindikiro za dziko lawo monga mbendera. (1 Yohane 5:21) Pomwe ena amachita zikondwerero pofuna kulemekeza magulu andale kapena mabungwe omenyera ufulu wa anthu. Kodi Yehova angamve bwanji ngati titamachita zikondwerero zolemekeza anthu enaake kapena mabungwe, makamaka amene amalimbikitsa mfundo zosiyana ndi zimene Mulungu amafuna?

3. Kodi ndi makhalidwe ati amene amapangitsa kuti zikondwerero zina zikhale zosayenera?

Baibulo limaletsa zinthu monga “kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, [komanso] kumwa kwa mpikisano.” (1 Petulo 4:3) Anthu akamachita zikondwerero zina amachita zinthu mosadziletsa komanso amachita zachiwerewere. Kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kupeweratu zikondwerero zimene zimalimbikitsa makhalidwe oipa ngati amenewa.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti muzisangalatsa Yehova posankha zinthu moyenera pa nkhani ya maholide komanso zikondwerero.

4. Musamachite nawo zikondwerero zomwe Yehova sasangalala nazo

Werengani Aefeso 5:10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi tiyenera kutsimikizira chiyani kuti tidziwe ngati ndi zoyenera kuchita nawo chikondwerero chinachake?

  • Kodi ndi zikondwerero ziti zimene ndi zotchuka kumene mumakhala?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amasangalala ndi zikondwerero zimenezo?

Mwachitsanzo, kodi munayamba mwaganizirapo kuti maganizo a Mulungu pa nkhani yokondwerera tsiku lakubadwa ndi otani? Baibulo silitchula mtumiki wa Yehova aliyense yemwe anakondwererapo tsiku lakubadwa. Koma limatchula anthu awiri okha omwe anachita zimenezi ndipo onse sankatumikira Mulungu. Werengani Genesis 40:20-22 ndi Mateyu 14:6-10. Kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi pa zikondwerero ziwiri zonsezi, panachitika chinthu chofanana chiti?

  • Mogwirizana ndi zimene tawerenga m’mavesi aja, kodi mukuona kuti maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani yokondwerera masiku akubadwa?

Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova angakhumudwe ngati nditachita nawo zikondwerero za masiku akubadwa kapena zikondwerero zina zosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo?’ Werengani Ekisodo 32:1-8. Kenako, onerani VIDIYO n’kukambirana mafunso otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kutsimikizira kaye ngati zimene tikufuna kuchita ndi zovomerezeka kwa Yehova?

  • Nanga tingachite bwanji zimenezi?

Kodi mungadziwe bwanji zikondwerero zimene Mulungu sasangalala nazo?

  • Kodi chikondwererochi ndi chogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Kuti mudziwe, fufuzani mmene chinayambira.

  • Kodi chikondwererochi chimalemekeza anthu, mabungwe kapena zizindikiro zimene dziko limaziona kuti ndi zofunika kwambiri? Timafunika kulemekeza Yehova kuposa aliyense ndipo timakhulupirira kuti iyeyo ndi amene adzathetse mavuto onse padzikoli.

  • Kodi zimene anthu amachita pa chikondwererochi zimagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo? Tiyenera kuyesetsa kukhalabe oyera pamaso pa Mulungu.

5. Muzithandiza ena kuti azilemekeza zimene mumakhulupirira

Sizikhala zophweka kukana ena akamakukakamizani kuti muchite nawo zikondwerero zimene sizisangalatsa Yehova. Komabe, mungachite bwino kuwafotokozera modekha komanso mosamala chifukwa chake simungachite nawo zikondwererozo. Kuti muone chitsanzo cha mmene mungachitire zimenezi, onerani VIDIYO.

Werengani Mateyu 7:12, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Mogwirizana ndi vesili, kodi muyenera kumauza achibale anu kuti asiye kuchita chikondwerero chinachake?

  • Kodi mungatsimikizire bwanji achibale anu kuti mumawakonda komanso mumawaganizira ngakhale kuti simuchita nawo limodzi chikondwerero chinachake?

6. Yehova amafuna kuti tizisangalala

Yehova amafuna kuti tizisangalala limodzi ndi achibale komanso anzathu. Werengani Mlaliki 8:15, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi vesili likusonyeza bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?

Yehova amafuna kuti anthu ake azisangalala. Onerani VIDIYO yosonyeza mmene zimenezi zimachitikira pamisonkhano yathu yamayiko.

Werengani Agalatiya 6:10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi tiyenera kumachita nawo maholide otchuka ngati njira ‘yochitira ena zabwino’?

  • Kodi mungasangalale mutakakamizidwa kupereka mphatso chifukwa cha chikondwerero chinachake kapena chifukwa chakuti mukufunitsitsa kupereka?

  • Nthawi zina, a Mboni ambiri amachitira ana awo zinthu zinazake zapadera. Ndipo nthawi zina, amawagulira mphatso zomwe samaziyembekezera. Ngati muli ndi ana, kodi ndi zinthu zapadera ziti zimene mungawachitire?

ZIMENE ENA AMANENA: “Zilibe ntchito kuti holideyo inayamba bwanji. Chofunika ndi choti pa nthawiyi timapeza mwayi wosangalala limodzi ndi achibale komanso anzathu.”

  • Kodi mungamufotokozere zotani munthu wotereyu?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti tizisangalala limodzi ndi achibale komanso anzathu. Komabe iye amafuna kuti tisamachite nawo zikondwerero zimene sizimamusangalatsa.

Kubwereza

  • Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tidziwe ngati chikondwerero chinachake chimasangalatsa Yehova kapena ayi?

  • Kodi tingathandize bwanji achibale ndi anzathu kuti amvetse chifukwa chake sitichita nawo maholide enaake?

  • Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zifukwa 4 zomwe zimatichititsa kukhulupirira kuti zikondwerero za masiku akubadwa sizisangalatsa Mulungu.

“N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Masiku Akubadwa?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zimene achinyamata amene amakonda Yehova amachita pofuna kumusangalatsa pa nthawi ya maholide.

Yehova Amakuona Kuti Ndiwe Wofunika (11:35)

Akhristu ambiri anasankha kuti asamakondwerere nawo Khirisimasi. Kodi amamva bwanji akaganizira zimene anasankhazi?

“Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi” (Nsanja ya Olonda, December 1, 2012)

a Onani Mawu Akumapeto 5 kuti mudziwe zimene mungachite pamene anthu ena akukondwerera holide inayake.