Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 48

Sankhani Anzanu Mwanzelu

Sankhani Anzanu Mwanzelu

Anzathu a pamtima amatikondweletsa pa nthawi yabwino, komanso amatilimbikitsa pa nthawi yovuta. Koma Baibo imaticenjeza kuti si munthu aliyense amene angakhale mnzathu wabwino. Conco, kodi mungasankhe bwanji mabwenzi abwino? Ganizilani mafunso aya.

1. Kodi mabwenzi amene mumasankha angakhudze bwanji khalidwe lanu?

Ife anthu timakonda kutengela makhalidwe a anthu amene timaceza nawo, makhalidwe abwino kapena oipa. Zimenezi zimacitika ndithu kaya poceza nawo tikakhala pamodzi kapena pa soshomidiya. Baibo imanena kuti, “munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa [aja osakonda Yehova] adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mabwenzi amene amakonda Yehova na kum’lambila angakuthandizeni kukhala pafupi na Mulungu, komanso kuti muzipanga zisankho zabwino. Koma anzathu a kunja kwa mpingo, angayambe kutikanganula kwa Yehova. Ndiye cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kusankha mabwenzi mwanzelu. Ngati mabwenzi athu ni anthu okonda Mulungu, amatipindulitsa ifenso timawapindulitsa. Timatonthozana komanso kulimbikitsana wina na mnzake.—1 Atesalonika 5:11.

2. Kodi Yehova amamva bwanji poona anthu amene musankha kukhala anzanu?

Yehova amasankha mabwenzi ake mosamala. Iye “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Kodi Yehova angamve bwanji ngati tisankha anthu osamukonda kukhala anzathu? Angakhumudwe kwambili! (Ŵelengani Yakobo 4:4.) Koma ngati tipewa anthu oipa, m’malo mwake tisankha mabwenzi okonda Yehova, iye adzakondwela nafe, ndipo adzatisankha kukhala mabwenzi ake.—Salimo 15:1-4.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake kusankha bwino mabwenzi ni nkhani yaikulu. Onaninso mmene mungasankhile mabwenzi amene angakupindulitseni pa umoyo wanu.

3. Pewani mayanjano oipa

Kuceza na anthu osakonda Mulungu na malamulo ake, ndiko mayanjano oipa. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Kodi tingayambe bwanji kukhala na mayanjano oipa popanda kuzindikila?

Ŵelengani 1 Akorinto 15:33, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi munthu amene angakhale mayanjano oipa kwa inu ni munthu wotani? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Ŵelengani Salimo 119:63, na kukambilana funso ili:

  • Kodi ni munthu wotani amene mungasankhe kukhala mnzanu?

Cipatso cimodzi cowola cimawononga zonse. Kodi mayanjano oipa na munthu mmodzi angakuyambukileni motani?

4. Ngakhale anthu amene timasiyana nawo angakhale mabwenzi athu abwino

Baibo imasimba za anthu aŵili a mu Isiraeli wakale, Davide na Yonatani. Aŵiliwa anali a misinkhu yosiyana kwambili, koma anali mabwenzi a ponda apa m’pondepo. Ŵelengani 1 Samueli 18:1, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani mabwenzi athu sayenela kungokhala aja a msinkhu wathu, kapena amene timafanana nawo m’zinthu zina?

Ŵelengani Aroma 1:11, 12, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mabwenzi amene amakonda Yehova angalimbikitsane bwanji?

M’citsanzo ca mu vidiyo iyi, onani mmene m’bale wina wacinyamata anapezela mabwenzi ku malo amene sanawaganizile kuti angapezeko mabwenzi. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, n’cifukwa ciyani makolo a Akil anali kumudela nkhawa cifukwa ca anzake a kusukulu?

  • N’cifukwa ciyani poyamba iwo anaoneka monga mabwenzi abwino kwa iye?

  • Ndipo anathana nalo bwanji vuto la kusungulumwa kwake?

5. Mmene mungapezele mabwenzi abwino

Ganizilani mmene mungapezele mabwenzi abwino, na mmene inunso mungakhalile bwenzi labwino. Tambani VIDIYO.

Ŵelengani Miyambo 18:24, komanso 27:17, na kukambilanana mafunso aya:

  • Kodi mabwenzi enieni amathandizana bwanji?

  • Kodi muli nawo mabwenzi abwino otelo? Ngati mulibe, kodi mungawapeze bwanji?

Ŵelengani Afilipi 2:4, na kukambilana funso ili:

  • Kuti mukhale na mabwenzi abwino, inunso muyenela kukhala bwenzi labwino. Kodi mungacite zimenezi motani?

Kuti mukhale na mabwenzi abwino, inunso muyenela kukhala bwenzi labwino

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Olo kuti anzako akhale otani ali bwino, coipa n’kukhala ulibiletu mnzako.”

  • Nanga inu mukuti bwanji?

CIDULE CAKE

Tikasankha mabwenzi mwanzelu, timakondweletsa Yehova, ndiponso timapeza mapindu ambili.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani Yehova amakhudzidwa na mmene timasankhila anzathu?

  • Kodi tiyenela kupewa mabwenzi otani?

  • Kodi mungapeze bwanji mabwenzi abwino okonda Yehova?

Colinga

FUFUZANI

Onani mmene mabwenzi abwino angatithandizile pamene tili pa mayeso.

“Limbitsani Ubwenzi Pakati Panu Mapeto Asanafike” (Nsanja ya Mlonda, November 2019)

Kodi muyenela kudziŵa ciyani za mabwenzi a pa soshomidiya?

Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti (4:12)

Mu nkhani yakuti “Ndinkalakalaka Nditapeza Bambo,” onani cinathandiza munthu wina kuganizilanso za mabwenzi amene anasankha.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2012)