Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 49

Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 1

Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 1

Anthu okwatilana caposacedwa, amayembekezela kuti cimwemwe ca patsiku lawo la cikwati cidzakhalapobe nthawi zonse. Ndipo zikhoza kutheka ndithu. Akhristu amene akhala pa banja kwa nthawi yaitali, amenenso ayesetsa kugwilitsa nchito uphungu wa m’Baibo, amadziŵa kuti zimenezi n’zothekadi.

1. Kodi Baibo imapeleka malangizo otani kwa amuna okwatila?

Yehova anaika mwamuna kukhala mutu wa banja. (Ŵelengani Aefeso 5:23.) Yehova amayembekezela mwamuna kupanga zisankho zopindulila banja lake. Baibo imalangiza amuna kuti: “Pitilizani kukonda akazi anu.” (Aefeso 5:25) Kodi imatanthauza ciyani? Imatanthauza kuti mwamuna wacikondi ayenela kucita na mkazi wake mokoma mtima, panyumba ngakhale kwina kulikonse. Iye amateteza mkazi wake ku coopsa ciliconse, ndipo amayesetsa kusamalila zosoŵa za mkazi wake, zakuthupi komanso zokhudza maganizo. (1 Timoteyo 5:8) Koma cofunika kopambana, ayenela kusamalila mkazi wake pa zinthu zauzimu. (Mateyu 4:4) Mwacitsanzo, angamapemphelele pamodzi na mkazi wake komanso kuŵelenga Baibo. Mwamuna akamasamalila mkazi wake mwacikondi, amakhalanso pa ubale wabwino na Yehova.—Ŵelengani 1 Petulo 3:7.

2. Kodi Baibo imapeleka malangizo otani kwa akazi okwatiwa?

Mawu a Mulungu amati “mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Kodi mkazi angacite bwanji zimenezi? Ayenela kuganizila makhalidwe abwino a mwamuna wake, komanso zimene mwamunayo amacita kuti asamalile iye pamodzi na ana ake. Ayenela kulemekezanso mwamuna wake pocilikiza zisankho zimene amapanga, komanso mwa kukamba zabwino za mwamuna wake, ngakhale atakhala kuti si Mboni.

3. Kodi amene ali pabanja angalimbitse bwanji ukwati wawo?

Ponena za okwatilana, Baibo imakamba kuti: “Aŵiliwo adzakhala thupi limodzi.” (Mateyu 19:5) Izi zitanthauza kuti ayenela kucita zonse zotheka kuti asakanganukane m’njila iliyonse. Kuti zimenezi zitheke, ayenela kumapeza nthawi yokhalila pamodzi, komanso kukhala omasukilana kuuzana zakukhosi na mmene amamvela. Sayenela kulola cinthu ciliconse, kapena munthu aliyense kukhala wofunika kupambana mnzawo wa muukwati, kupatula Yehova yekha basi. Cina, ayenela kusamala kwambili kuti asamazoloŵelane ngako na munthu amene si mwamuna wawo kapena mkazi wawo.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mfundo za m’Baibo zimene zingalimbitse ukwati wanu.

4. Inu amuna—muzikonda akazi anu na kuwasamalila bwino

Baibo imanena kuti “amuna akonde akazi awo monga matupi awo.” (Aefeso 5:28, 29) Kodi zimenezi zitanthauza ciyani? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi mwamuna angaonetse m’njila ziti kuti amakonda mkazi wake na kumusamalila?

Ŵelengani Akolose 3:12, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mwamuna angaonetse bwanji makhalidwe amenewa mu ukwati wake?

5. Inu akazi—kondani amuna anu na kuwalemekeza

Baibo imalimbikitsa mkazi kulemekeza mwamuna wake, kaya amatumikila Yehova kapena ayi. Ŵelengani 1 Petulo 3:1, 2, na kukambilana mafunso aya:

  • Ngati mwamuna wanu si Mboni, mwacidziŵikile mumafunitsitsa kuti ayambe kutumikila Yehova. Muganiza ni njila iti ingamufike bwino pamtima—kulimbikila kumamulalikila nthawi zonse, kapena kumuonetsa makhalidwe abwino na kumulemekeza? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Mwamuna na mkazi wake akhoza kumapanga zisankho zabwino mogwilizana. Koma nthawi zina mkazi angakhale na maganizo osiyana na mwamuna wake. Zikakhala conco, mkazi ayenela kufotokoza maganizo ake modekha komanso mwaulemu. Ngakhale n’telo, ayenela kuzindikila kuti Yehova anapatsa mwamuna wake udindo wopanga zigamulo zokomela banja lake. Ndipo mkazi wake ayenela kucilikiza zigamulo za mwamuna wake. Mwa kutelo, mkazi amabweletsa cimwemwe m’banja lake. Ŵelengani 1 Petulo 3:3-5, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Yehova amamva bwanji ngati mkazi amalemekeza mwamuna wake?

6. Mukhoza kugonjetsa mavuto a mu ukwati wanu

Palibe ukwati wangwilo. Conco, mwamuna na mkazi wake ayenela kuthandizana kuti agonjetse mavuto a mu ukwati wawo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi panali zizindikilo zotani zoonetsa kuti mwamuna na mkazi wake anayamba kukanganukana?

  • Koma anatenga masitepe otani kuti alimbitse ukwati wawo?

Ŵelengani 1 Akorinto 10:24, komanso Akolose 3:13. Pambuyo poŵelenga lililonse la malemba awa, kambilanani funso ili:

  • Kodi kugwilitsa nchito uphungu wa pa lembali kungalimbitse bwanji ukwati?

Baibo imakamba kuti tiyenela kulemekezana wina na mnzake. Kulemekeza munthu kumatanthauzanso kucita naye mokoma mtima komanso mwaulemu. Ŵelengani Aroma 12:10, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi mwamuna kapena mkazi wake ayenela kuyembekezela kuti mnzakeyo ndiye ayenela kuyamba kumulemekeza? N’cifukwa ciyani mwayankha conco

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ife mu ukwati wathu sitikondananso mmene tinali kucitila kale.”

  • Kodi mungawafotokozele motani kuti Baibo ikhoza kuwathandiza?

CIDULE CAKE

Mwamuna na mkazi wake angakhale acimwemwe ngati akondana, kulemekezana, komanso kugwilitsa nchito mfundo za m’Baibo.

Mafunso Obweleza

  • Kodi mwamuna ayenela kucita bwanji kuti ukwati wawo ukhale wacimwemwe?

  • Nanga mkazi nayenso angathandizile bwanji kuti ukwati wawo ukhale wacimwemwe?

  • Ngati muli pa banja, ni mfundo iti ya m’Baibo imene muona kuti ingakuthandizeni kulimbitsa ukwati wanu?

Colinga

FUFUZANI

Onani njila zimene zingakuthandizeni kuti banja lanu likhale losangalala.

N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe (bulosha)

Tambani vidiyo ya nyimbo yoonetsa madalitso amene amakhalapo ngati mugwilitsa nchito uphungu wa Mulungu mu ukwati wanu.

Tikondanadi (4:26)

Onani mmene uphungu wa m’Baibo pa zaukwati umakhalila wothandiza kwambili.

Baibo Inapulumutsa Cikwati Cathu (7:12)