Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 50

Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2

Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2

Ana ni mphatso zocokela kwa Yehova. Ndipo iye amayembekezela makolo kuwasamalila bwino ana awo monga mphatso. Yehova amapeleka ulangizi wanzelu wothandiza makolo kusamalila bwino ana awo. Ulangizi wake ungathandize ngakhale ana kucita mbali yawo kuti banja lawo likhale lopambana.

1. Kodi Yehova amapeleka ulangizi wotani kwa makolo?

Yehova amafuna kuti makolo azikonda ana awo, komanso kuti azipatula nthawi yokwanila yokhala nawo pamodzi. Amafunanso kuti makolo aziteteza ana awo ku civulazo ciliconse, na kuwaphunzitsa mfundo za m’Baibo. (Miyambo 1:8) Iye amauza atate kuti: “Muwalele [ana anu] m’malangizo a Yehova.” (Ŵelengani Aefeso 6:4.) Makolo akamatsatila cilangizo ca Yehova polela ana awo, komanso kusapeleka udindo wawo kwa munthu wina, Yehova amakondwela ngako.

2. Kodi Yehova amapeleka malangizo otani kwa ana?

Yehova amalangiza ana kuti: “Muzimvela makolo anu.” (Ŵelengani Akolose 3:20.) Ana akamamvela makolo awo na kuwalemekeza, amapangitsa Yehova na makolo awo kukhala acimwemwe. (Miyambo 23:22-25) Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili pamene anali mwana. Ngakhale kuti anali wangwilo, iye anali kumvela makolo ake na kuwalemekeza.—Luka 2:51, 52.

3. Kodi mungamuyandikile bwanji Mulungu monga banja?

Ngati ndinu kholo, ndithudi mumafuna kuti ana anu azikonda Yehova kwambili, mmene inunso mumamukondela. Kodi mungawathandize bwanji pa mbali imeneyi? Muyenela kucita zimene Baibo imanena kuti: ‘Uzikhomeleza [Mawu a Yehova] mwa ana ako. Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako,’ komanso “poyenda pamsewu.” (Deuteronomo 6:7) “Kukhomeleza” kumatanthauza kuphunzitsa cinthu mobweleza-bweleza. Monga mudziŵila, kuti mwana akumbukile cinthu, muyenela kumuuza cinthuco kangapo konse. N’zimene lembali likutanthauza. Muyenela kufunafuna mipata nthawi zonse yomauzako ana anu za Yehova. Ni cinthu canzelu kupatula nthawi mlungu uliwonse yolambilila pamodzi monga banja. Ngati mulibe ana, mungapindulebe ngati mupatula nthawi mlungu uliwonse yophunzila Mawu a Mulungu.

KUMBANI MOZAMILAPO

Ganizilani njila zimene zingathandize banja lanu kukhala lacimwemwe komanso lotetezeka.

4. Phunzitsani ana anu mwacikondi

Kuphunzitsa ana si nchito yopepuka. Kodi Baibo ingakuthandizeni bwanji? Ŵelengani Yakobo 1:19, 20, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi makolo angaonetse bwanji cikondi pokamba na ana awo?

  • N’cifukwa ciyani kholo siiyenela kulanga mwana wake pamene ili yokwiya? a

5. Tetezani ana anu

Kuti muteteze ana anu, ni cinthu cofunika kwambili kuti muzikambilana na mwana wanu aliyense payekha za nkhani ya kugonana. N’zoona kuti mungaume pakamwa pocita zimenezi. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • N’cifukwa ciyani ili nkhani yovutilapo kwa makolo ena kukambilana na ana awo zakugonana?

  • Kodi makolo ena acita motani kuti afotokozele ana awo zakugonana?

Monga mwa ulosi wa m’Baibo, dziko la Satana likungoipila-ipila nthawi zonse. Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1, 13, na kukambilana funso ili:

  • Anthu ena oipa ochulidwa pa vesi 13 amacita nkhanza zogona ana. Conco, n’cifukwa ciyani kuli kofunika kwambili kuti makolo aziunikila ana awo nkhani ya kugonana, komanso mmene anawo angadzitetezele kwa anthu ankhanza otelo?

Kodi mudziŵa?

A Mboni za Yehova amakonza zida zambili zothandiza makolo kuunikila ana awo pa nkhani yakugonana, komanso mmene anawo angadzitetezele kwa anthu ankhanza. Mwacitsanzo, onani:

6. Lemekezani makolo anu

Ana komanso acinyamata angalemekeze makolo awo mwa njila imene amakambila kwa iwo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • N’cifukwa ciyani n’cinthu cofunika kuti wacicepele azilankhula kwa makolo ake mwaulemu?

  • Kodi wacicepele angalankhule motani kwa makolo ake mowapatsa ulemu?

Ŵelengani Miyambo 1:8, na kukambilana funso ili:

  • Kodi wacicepele ayenela kucita bwanji pamene makolo ake akumuuza zocita?

7. Muzilambila Yehova capamodzi monga banja

Mabanja a Mboni za Yehova amapatula nthawi mlungu uliwonse kuti alambile capamodzi monga banja. Kodi kulambila kwa pabanja kumeneku kuyenela kucitika motani? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Kodi mungaikonze bwanji pulogilamu ya Kulambila kwa Pabanja kwa mlungu uliwonse?

  • Kodi kholo lingacite bwanji kuti kulambila kwa pabanja kuzikhala kothandiza komanso kosangalatsa?—Onani cithunzi coyambilila m’phunzilo lino.

  • N’cifukwa ciyani mwina cingakhale covuta kwa inu kuphunzilila pamodzi monga banja?

Mu Isiraeli wakale, Yehova anali kufuna kuti mabanja azikambilana Malemba nthawi zonse. Ŵelengani Deuteronomo 6:6, 7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mfundo ya palembali mungaigwilitse nchito bwanji?

Mungacite kulambila kwa pabanja m’njila izi:

  • Kukonzekela misonkhano ya mpingo.

  • Kuŵelenga na kukambilana nkhani ya m’Baibo imene banja lanu lingakonde.

  • Ngati ana anu ni ang’ono-ang’ono, citani daunilodi kapena pulintani zocita za ana pa jw.org.

  • Ngati ana anu ni acinyamata, kambilanani nkhani yokhudza acinyamata ya pa jw.org.

  • Yeselelani nkhani ya m’Baibo na ana anu.

  • Tambani na kukambilana vidiyo ya pa jw.org.

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Baibo ni buku lovuta kwa ana.”

  • Inu muganiza bwanji?

CIDULE CAKE

Yehova amafuna kuti makolo azikonda ana awo, kuwaphunzitsa, na kuwateteza. Amafunanso kuti ana azimvela makolo awo na kuwalemekeza. Ndiponso amafuna kuti mabanja azimulambila capamodzi.

Mafunso Obweleza

  • Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo na kuwateteza?

  • Nanga ana angalemekeze bwanji makolo awo?

  • Kodi pali mapindu otani ngati tipatula nthawi mlungu uliwonse kuti tizilambila capamodzi monga banja?

Colinga

FUFUZANI

Kodi ni maphunzilo ati angathandize ana anu kukula bwino?

“Zinthu 6 Zimene Ana Afunika Kuphunzila” (Galamuka! Na. 2 2019)

Dziŵani ulangizi wothandiza umene Baibo imapeleka kwa amene akusamalila makolo.

“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yosamalira Makolo Achikulire?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani mmene mwamuna wosadziŵa kulela ana anadzakhalila tate wabwino kwambili.

Yehova Anatiphunzitsa Kulela Bwino Ana Athu (5:58)

a M’Baibo, “kulanga” kumatanthauza kuphunzitsa, kulangiza, komanso kuwongolela. Sikutanthauza nkhanza, iyayi.—Miyambo 4:1.