Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 54

Udindo wa “Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu”

Udindo wa “Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu”

Yesu ndiye Mutu wa Mpingo wacikhristu. (Aefeso 5:23) Masiku ano, Yesu kucokela kumwamba kumene ali, amatsogolela otsatila ake padziko lapansi kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Ŵelengani Mateyu 24:45.) Yesu iyemwini anapeleka ulamulilo winawake kwa kapolo ameneyu. Ngakhale n’telo, iye akukhalabe pansi pa Khristu monga “kapolo” wake, ndipo amatumikila abale a Khristu. Kodi kapolo ameneyu ndani? Ndipo amatisamalila motani ife?

1. Kodi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” ndani?

Nthawi zonse, Yehova wakhala akugwilitsa nchito munthu, kapena kagulu ka anthu kutsogolela anthu ake. (Malaki 2:7; Aheberi 1:1) Yesu atamwalila, atumwi ake komanso akulu ku Yerusalemu ndiwo anapitiliza kutsogolela Akhristu. (Machitidwe 15:2) Potengela citsanzo cimeneco, masiku anonso, kagulu kocepa ka akulu—Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova—ndiko kamagaŵila cakudya cauzimu, komanso kuyang’anila nchito yolalikila. Kagulu kameneka kamachedwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” ndipo kanasankhidwa na Yesu. (Mateyu 24:45a) Onse a m’Bungwe Lolamulila ni Akhristu odzozedwa, amene akuyembekezela kukagwilizana na Khristu mu Ufumu wakumwamba, akadzamwalila padziko lapansi.

2. Kodi kapolo wokhulupilika ameneyu amagaŵila cakudya cauzimu cotani?

Yesu ananena kuti kapolo wokhulupilika ameneyu, ‘aziwapatsa cakudya [Akhristu anzake] pa nthawi yoyenela.’ (Mateyu 24:45b) Monga mmene cakudya ceniceni cimatipatsila nyonga na thanzi, cakudya cauzimu—kutanthauza cilangizo cocokela m’Mawu a Mulungu—cimatipatsa mphamvu zofunikila kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova, na kugwila nchito imene Yesu anatipatsa. (1 Timoteyo 4:6) Cakudya cauzimu cimeneco, timacilandila pa misonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo. Timacilandilanso m’mabuku ozikika pa Baibo, komanso mavidiyo otithandiza kumvetsetsa cifunilo ca Mulungu na kulimbitsa ubwenzi wathu na iye.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake timafunika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”—amene ndiyenso Bungwe Lolamulila.

Bungwe Lolamulila limapatsa Mboni za Yehova padziko lonse lapansi cakudya cauzimu, malangizo, komanso cithandizo

3. Anthu a Yehova ayenela kukhala gulu locita zinthu mwadongosolo

Pansi pa utsogoleli wa Yesu, Bungwe Lolamulila limalinganiza nchito ya Mboni za Yehova. Ni mmenenso zinalili kwa Akhristu oyambilila. Tambani VIDIYO.

Ŵelengani 1 Akorinto 14:33, 40, na kukambilana funso ili:

  • Kodi lemba ili lionetsa bwanji kuti Yehova amafuna Mboni zake kukhala gulu locita zinthu mwadongosolo?

4. Kapolo wokhulupilika ndiye amalinganiza nchito yolalikila

Kulalikila ndiyo inali nchito yofunika kwambili kwa Akhristu oyambilila. Ŵelengani Machitidwe 8:14, 25, na kukambilana mafunso aya:

  • Kwa Akhristu oyambilila, kodi ndani anali kupeleka malangizo pa nchito yolalikila?

  • Kodi Petulo na Yohane anacita bwanji atalandila malangizo ocokela kwa atumwi anzawo?

Kulalikila ndiyo nchito yofunika kwambili imene a Bungwe Lolamulila akuiyang’anila. Tambani VIDIYO.

Yesu anatsindika kufunika kwa nchito yolalikila. Ŵelengani Maliko 13:10, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani nchito yolalikila ni yofunika kwambili kwa a Bungwe Lolamulila?

  • N’cifukwa ciyani timafunikiladi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti aziyendetsa nchito ya padziko lonse imeneyi?

5. Kapolo wokhulupilika ndiye amapeleka citsogozo

A Bungwe Lolamulila ndiwo amapeleka citsogozo kwa Akhristu onse padziko lapansi. Kodi iwo amadziŵa bwanji malangizo ofunika kupelekedwa? Onani mmene bungwe lolamulila la Akhristu oyambilila linacitila zimenezi. Ŵelengani Machitidwe 15:1, 2, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi ni nkhani iti inabutsa mkangano pakati pa ena mwa Akhristu oyambilila?

  • Ndipo Paulo, Baranaba, na ena nkhaniyi anakaitula kuti?

Ŵelengani Machitidwe 15:12-18, 23-29, na kukambilana funso ili:

  • Asanapange cigamulo, kodi a bungwe lolamulila la panthawiyo, anayamba ayang’ana mbali iti popempha citsogozo ca Mulungu pa nkhani imeneyi?—Onani mavesi 12, 15, na 28.

Ŵelengani Machitidwe 15:30, 31, komanso 16:4, 5, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Akhristu oyambilila anacita bwanji atalandila malangizo ocokela ku bungwe lolamulila?

  • Ndipo Yehova anawadalitsa bwanji cifukwa ca kumvela kwawo?

Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16, komanso Yakobo 1:5, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Bungwe Lolamulila lamakono limapeza kuti cithandizo popanga zigamulo?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ngati mumamvela Bungwe Lolamulila, ndiye kuti mumangotsatila anthu.”

  • N’cifukwa ciyani inu mumakhulupilila kuti Yesu ndiye amatsogolela Bungwe Lolamulila?

CIDULE CAKE

Bungwe Lolamulila ndilo “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” ndipo Khristu ndiye anamusankha. Bungwe limeneli ndilo limayang’anila Akhristu onse padziko lapansi, komanso kuwapatsa cakudya cauzimu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi ndani anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”?

  • Ndipo Bungwe Lolamulila limatisamalila bwanji?

  • Kodi inu mumakhulupilila kuti Bungwe Lolamulila ndilodi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”?

Colinga

FUFUZANI

Onani mmene Bungwe Lolamulila linakonzedwela kuti lizigwila bwino nchito yake.

“Kodi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova Limachita Zotani?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani mmene Bungwe Lolamulila limacitila zotheka kuti tizilandila cakudya cauzimu codalilika.

Kufalitsa Nkhani Zolondola (17:18)

Kodi a m’Bungwe Lolamulila amamva bwanji pa nchito imene Yesu anawapatsa kuti aigwile?

Ni Mwayi Wapadela (7:04)

Kodi misonkhano ya pampingo komanso misonkhano ikulu-ikulu, imaonetsa bwanji kuti Yehova ndiyedi amatsogolela Bungwe Lolamulila?

Yehova Akuphunzitsa Anthu Ake (9:39)