Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 58

Khalanibe Wokhulupilika kwa Yehova

Khalanibe Wokhulupilika kwa Yehova

Akhristu oona salola ciliconse kapena aliyense kusokoneza kulambila kwawo Yehova. Mwacidziŵikile, inunso n’cimodzimodzi. Yehova amakukondani cifukwa ca kukhulupilika kwanu. (Ŵelengani 1 Mbiri 28:9.) Kodi ni zocitika ziti zingakuikeni pamayeso pa nkhani ya kukhulupilika, ndipo mungathane nazo bwanji?

1. Kodi anthu ena angakuikeni bwanji pa mayeso cifukwa ca kukhulupilika kwanu kwa Yehova?

Pali anthu ena amene adzafuna kutisiyitsa kutumikila Yehova. Kodi amenewo angakhale ndani? Ena ni aja amene anasiya coonadi ndipo amanena mabodza ponena za gulu la Mulungu kuti awononge cikhulupililo cathu. Amenewo amachedwa ampatuko. Palinso atsogoleli a zipembedzo, amene amafalitsa mabodza n’colinga cakuti ena osakhwima kwenikweni asiye coonadi. Tiyenela kusamala kuti anthu otsutsa amenewo tisamakambilane nawo, kapena kuŵelenga mabuku awo, kapenanso kupita pamawebusaiti awo, ngakhalenso kutamba mavidiyo awo. Ponena za anthu amenewo ofuna kulefula anzawo pa kutumikila Yehova, Yesu anati: “Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleli akhungu. Cotelo ngati munthu wakhungu akutsogolela wakhungu mnzake, onse aŵili adzagwela m’dzenje.”Mateyu 15:14.

Koma bwanji ngati munthu amene timadziŵana naye wasankha kusiya mpingo wa Mboni za Yehova? Cimakhala cinthu copweteka mtima kwambili ngati munthu amene timakonda wacita zimenezi. Munthu ameneyo angatipangitse kuti tisankhe pakati pa iye na Yehova. Koma ife tiyenela kusankha kukhalabe wokhulupilika kwa Mulungu, osati kwa munthu wina aliyense. (Mateyu 10:37) N’cifukwa cake timamvela lamulo la Yehova lakuti tizipewa kuceza na anthu otelowo.—Ŵelengani 1 Akorinto 5:11.

2. Kodi zisankho zimene timapanga zingaonetse bwanji kuti ndife okhulupilika kwa Yehova kapena ayi?

Ngati timam’kondadi Yehova, tidzapewa kucita ciliconse cokhudzana na kulambila konyenga. Nchito imene timagwila, kaya kampani imene timagwilako nchito, kapena gulu lililonse limene timagwilizana nalo, lisakhale la cipembedzo conyenga. Ndipo tisapezeke m’zocita zilizonse zokhudzana na cipembedzo conyenga. Yehova amaticenjeza kuti: “Tulukani mwa iye [m’Babulo Wamkulu] anthu anga.”Chivumbulutso 18:2, 4.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani mmene mungakanizile munthu aliyense kuti asafooketse cikhulupililo canu mwa Yehova. Onaninso mmene mungaonetsele kukhulupilika kwanu mwa kutuluka mu Babulo Wamkulu.

3. Cenjelani na aphunzitsi onyenga

Kodi tiyenela kucita bwanji anthu ena akamakamba zoipa ponena za gulu la Yehova? Ŵelengani Miyambo 14:15, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala kuti tisamakhulupilile ciliconse cimene tamva?

Ŵelengani 2 Yohane 10, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi ampatuko tiyenela kucita nawo motani?

  • Olo kuti tisakambilane nawo mwacindunji, kodi ni njila zina ziti zimene tingakhalile tikumvetsela ziphunzitso zawo?

  • Kodi muganiza Yehova angamve bwanji ngati timvetsela zoipa zimene zikukambidwa ponena za iye kapena gulu lake?

4. Khalanibe wokhulupilika kwa Mulungu pamene m’bale wacimwa

Tikamva kuti winawake mumpingo wacita chimo lalikulu, kodi timakhalapo na udindo wotani? Ganizilani mfundo iyi ya m’Cilamulo ca Mulungu, imene iye anapeleka kwa Aisiraeli akale. Ŵelengani Levitiko 5:1.

Monga atilangizila pa lemba limeneli, tikadziŵa kuti munthu wina wacita chimo lalikulu, tiyenela kuwadziŵitsa akulu. Koma tisanatelo, kudzakhala kukoma mtima kumulimbikitsa wolakwayo kuti apite yekha kwa akulu kukaulula chimo lake. Ngati iye sakucita zimenezo, cikhulupililo cathu mwa Yehova ciyenela kutipangitsa kukawauza akulu zimene tikudziŵapo. Kodi kucita zimenezi kumaonetsa bwanji kuti ndife okhulupilika . . .

  • kwa Yehova Mulungu?

  • kwa munthu amene anacimwayo?

  • kwa ena mumpingo?

Wokhulupilila mnzanu akakhala pavuto, m’thandizeni!

5. Khalani naye kutali Babulo Wamkulu

Ŵelengani Luka 4:8, komanso Chivumbulutso 18:4, 5, kenako yankhani mafunso odziunika nawo aya:

  • Kodi dzina langa likalimo mukaundula wa mamembala a cipembedzo conyenga?

  • Kodi ndine membala wa gulu linalake lokhudzana na cipembedzo conyenga?

  • Kodi nchito imene nimagwila imathandizila cipembedzo conyenga m’njila iliyonse?

  • Kodi pali mbali iliyonse mu umoyo wanga imene niyenela kulekanabe naco cipembedzo conyenga?

  • Ngati nayankha kuti inde pa iliyonse ya mafunso amenewa, kodi niyenela kupanga masinthidwe otani?

Pa nkhani iliyonse, pangani cisankho cimene cidzakusiyani na cikumbumtima coyela, komanso coonetsa kuti ndinu wokhulupilika kwa Yehova

Kodi mungacite ciyani ngati mwapemphedwa kupeleka ndalama ku nchito zacifundo za cipembedzo cinacake?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nimafuna kudziŵa zimene ampatuko amakamba zokhudza Mboni za Yehova, kuti nizicikhalila bwino kumbuyo coonadi.”

  • Kodi kaganizidwe kameneka n’kanzelu? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

CIDULE CAKE

Kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova tiyenela kupewa kumaceza na anthu osakhulupilika kwa iye. Tiyenelanso kudzilekanitsa kothelatu ku cipembedzo conyenga.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani sitiyenela kutamba, kuŵelenga, kapena kumvetsela maganizo a ampatuko?

  • Kodi tiyenela kucita nawo motani aja amene sakufunanso kukhala Mboni za Yehova?

  • Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tilabadile cenjezo lakuti tithaŵemo m’cipembedzo conyenga?

Colinga

FUFUZANI

Dziŵani mocitila ngati anthu ena akufalitsa mabodza okhudza Mboni za Yehova.

“Kodi Mudziŵa Bwino Zoona Zake?” (Nsanja ya Mlonda, August 2018)

Kodi mungawadziŵe bwanji magulu kapena zocitika zocilikiza Babulo Wamkulu?

“Khalanibe Acangu mu Ndime Ino Yothela ya ‘Masiku Otsiliza’” (Nsanja ya Mlonda, October 2019, ndime 16-18)

Kodi otsutsa ena acita ciyani pofuna kufooketsa cikhulupililo cathu?

Cenjelani Naco Cinyengo (9:32)

Mu nkhani yakuti “Kuyambira Ndili Mwana Ndinkafunitsitsa Kudziwa Mulungu,” ŵelengani za wansembe wacishinto amene analekana naco cipembedzo conyenga.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2011)