Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 59

Mukhoza Kupilila Pamene Mukuzunzidwa

Mukhoza Kupilila Pamene Mukuzunzidwa

Pa nthawi inayake, Akhristu tonse tidzakumana na anthu otitsutsa ngakhale kutizunza. Kodi zimenezi ziyenela kutidetsa nkhawa?

1. N’cifukwa ciyani tiyenela kuyembekezela mazunzo?

Baibo imakamba momveka bwino kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Timoteyo 3:12) Yesu anazunzidwa cifukwa sanali kumbali ya dziko la Satanali. Ifenso sitili kumbali ya dzikoli. Conco, sitikudabwa pamene maboma kapena zipembedzo za dzikoli zikutizunza.—Yohane 15:18, 19.

2. Kodi mazunzo tingawakonzekele bwanji?

Tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova pali pano. Tsiku lililonse, tiyenela kupemphela kwa Yehova na kuŵelenga Mawu ake. Tiyenelanso kupezeka ku misonkhano nthawi zonse. Izi n’zimene muyenela kucita kuti mukhale na mphamvu, komanso wolimba mtima kupilila cizunzo ciliconse, ngakhale citacokela kwa a m’banja mwanu. Mtumwi Paulo, amenenso anakumana na mazunzo kaŵili-kaŵili, analemba kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”Aheberi 13:6.

Timakhalanso olimba mtima tikamalalikila nthawi zonse. Kulalikila kumatiphunzitsa kudalila Yehova na kusaopa munthu aliyense. (Miyambo 29:25) Mukazoloŵela kulalikila molimba mtima pali pano, simungaleke kulalikila ngakhale boma litaletsa nchito yathu imeneyi.—1 Atesalonika 2:2.

3. Kodi pali ubwino wanji tikapilila cizunzo?

Pamene tikuzunzidwa sikuti timasangalala ayi. Koma tikakwanitsa kupilila, cikhulupililo cathu cimakhala colimba. Ndipo cikondi cathu pa Yehova cimakula, cifukwa timaona mmene amatithandizila pamene sitingathenso kupilila. (Ŵelengani Yakobo 1:2-4.) Pamene anthu ena akutivutitsa, Yehova cimamuŵaŵa kwambili. Koma mtima wake umakondwela akaona kuti tikupilila. Baibo imakamba kuti: “Ngati mukupilila povutika cifukwa ca kucita zabwino, zimenezo n’zabwino kwa Mulungu.” (1 Petulo 2:20) Anthu onse amene amapilila mokhulupilika, Yehova adzawapatsa mphoto. Mphoto imeneyo ni moyo wosatha m’dziko lopanda anthu otsutsa kulambila koona—Mateyu 24:13.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake n’kotheka komanso n’kopindulitsa kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova, ngakhale pamene tikuzunzidwa.

4. Mukhoza kupilila ngati a m’banja mwanu akukutsutsani

Yesu anakambilatu mfundo yakuti zikhoza kucitika a m’banja mwathu kusagwilizana na cisankho cathu colambila Yehova. Ŵelengani Mateyu 10:34-36, na kukambilana funso ili:

  • Kodi cingacitike n’ciyani ngati wina m’banja wasankha kutumikila Yehova?

Kuti muone citsanzo ca zimenezi, tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi mungacite bwanji ngati wacibale wanu, kapena mnzanu, akuyesa kukuletsani kutumikila Yehova?

Ŵelengani Salimo 27:10, komanso Maliko 10:29, 30. Pambuyo poŵelenga lililonse la malembawa, kambilanani funso ili:

  • Kodi lonjezo limeneli lingakuthandizeni bwanji ngati a m’banja mwanu, kapena mabwenzi anu, akukuletsani kutumikila Yehova?

5. Pitilizani kulambila Yehova pamene mukuzunzidwa

Pamafunika kulimba mtima kuti titumikile Yehova pamene ena akutiletsa kutelo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Mu zitsanzo za mu vidiyo imeneyi, kodi cakulimbikitsani n’ciyani?

Ŵelengani Machitidwe 5:27-29, komanso Aheberi 10:24, 25. Pambuyo poŵelenga lililonse la malembawa, kambilanani funso ili:

  • N’cifukwa ciyani sitiyenela kuleka kulambila Yehova, ngakhale pamene boma laletsa nchito yathu yolalikila, kapena kusonkhana kwathu?

6. Yehova adzakuthandizani kuti mupilile

A Mboni za Yehova osiyana-siyana misinkhu na zikhalidwe, akhala akumutumikilibe Yehova mokhulupilika ngakhale pokumana na mazunzo. Kuti muone zimene zawathandiza, tambani VIDIYO. Pambuyo pake kambilanani funso lotsatila.

  • Mu vidiyo iyi, kodi n’ciyani cinathandiza Mboni zimenezi kupilila?

Ŵelengani Aroma 8:35, 37-39, komanso Afilipi 4:13. Pambuyo poŵelenga lililonse la malembawa, kambilanani funso ili:

  • Kodi lemba limeneli likukutsimikizilani bwanji kuti mukhoza kupilila mayeso alionse?

Ŵelengani Mateyu 5:10-12, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani mungakhalebe acimwemwe ngakhale pamene mukuzunzidwa?

Mamiliyoni a olambila Yehova apilila mosagonja kwa owatsutsa. Inunso mukhoza kutelo!

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ine siningakwanitse kupilila cizunzo.”

  • Kodi ni malemba ati angawapatse cidalilo?

CIDULE CAKE

Yehova amayamikila tikamacitabe khama kumutumikila pamene tikuzunzidwa. Mwa thandizo lake, tidzakwanitsa kupilila!

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani Akhristu ayenela kuyembekezela kuti adzazunzidwa?

  • Kodi muyenela kucita ciyani pali pano kuti mukakhale wokonzeka pamene cizunzo cidzafika?

  • Kodi n’ciyani cingakupatseni cidalilo cakuti mudzamutumikilabe Yehova ngakhale pokumana na mayeso alionse?

Colinga

FUFUZANI

Onani mmene m’bale wacicepele akufotokozela mmene Yehova anamuthandizila kupilila atamangidwa cifukwa cosakhalila mbali m’nkhani za dziko.

Kupilila Pozunzidwa (2:34)

Onani cimene cinathandiza okwatilana aŵili kutumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili, mosasamala kanthu za kutsutsidwa.

Anatumikira Yehova Panthawi Imene Zinthu Zinali Zitasintha (7:11)

Onani mmene mungakhalile olimba mtima pamene mukuzunzidwa.

“Konzekelani Cizunzo Pali Pano” (Nsanja ya Mlonda, July 2019)

Kodi tiyenela kukumbukila ciyani a m’banja mwathu akamatitsutsa, ndipo tingathane nawo bwanji mavuto amene amakhalapo?

“Coonadi ‘Sicibweletsa Mtendele Koma Lupanga’” (Nsanja ya Mlonda, October 2017)