Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 60

Pitanibe Patsogolo Kuuzimu

Pitanibe Patsogolo Kuuzimu

M’maphunzilo onsewa a Baibo, mwaphunzila zoculuka zokhudza Yehova. Zimene mwaphunzila zakulitsa cikondi canu pa Yehova, moti mwina munafika podzipatulila kwa iye na kubatizika. Ngati simunatelobe, n’kutheka kuti mukuganizila zodzabatizika m’tsogolomu. Koma kupita patsogolo kwanu sikuyenela kulekezela pa ubatizo ayi. Muyenela kupitilizabe kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova kwamuyaya. Motani?

1. N’cifukwa ciyani simuyenela kuleka kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova?

Tiyenela kuyesetsa mwakhama kuti tipitilizebe kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova. Cifukwa ciyani? ‘Kuti tisatengeke pang’onopang’ono na kumusiya iye.’ (Aheberi 2:1) N’ciyani cingatithandize kuti tisaleke kutumikila Yehova mokhulupilika? Njila imodzi ni kukhala wokangalika m’nchito yolalikila. Pezaninso njila zina zimene mungawonjezele utumiki wanu kwa Mulungu. (Ŵelengani Afilipi 3:16.) Kutumikila Yehova ndiko umoyo wabwino kopambana.—Salimo 84:10.

2. Kodi muyenelanso kupitiliza kucita ciyani?

Ngakhale kuti lomba mukumaliza maphunzilo a Baibo amenewa, umoyo wanu monga Mkhristu ukupitilizabe. Baibo imanena kuti tiyenela “kuvala umunthu watsopano.” (Aefeso 4:23, 24) Pamene mupitiliza kuphunzila Mawu a Mulungu, na kupezeka pa misonkhano ya mpingo, mudzaphunzila zinthu zatsopano zokhudza Yehova na makhalidwe ake. Yesetsani kutengela kwambili makhalidwe ake pa umoyo wanu. Pitilizani kukonza umoyo wanu kuti Yehova azikondwela nanu.

3. Kodi Yehova adzakuthandizani bwanji kuti mupitebe patsogolo?

Baibo imakamba kuti: “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani, ndi kukupatsani mphamvu.” (1 Petulo 5:10) Tonsefe timakumana na mayeselo otikopa. Koma Yehova amatithandiza kuti tisagonje ku mayeselo amenewo. (Salimo 139:23, 24) Iye akulonjeza kuti adzalimbikitsa cifuno canu cakuti mum’tumikile mokhulupilika.—Ŵelengani Afilipi 2:13.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani zimene muyenela kucita kuti mupitebe patsogolo, na mmene Yehova angakudalitsileni.

4. Osaleka kumalakhulana na bwenzi lanu la pamtima

Pemphelo na kuphunzila Baibo zakuthandizani kupalana ubwenzi na Yehova. Koma kodi zinthu ziŵili zimenezi zingakuthandizeni bwanji kuti cikondi canu pa Yehova cizingokulila-kulila?

Ŵelengani Salimo 62:8, na kukambilana funso ili:

  • Kuti mulimbitse ubwenzi wanu na Yehova, kodi muyenela kuwongolela mbali ziti za mapemphelo anu?

Ŵelengani Salimo 1:2, kenako kambilanani funso ili:

  • Kuti mulimbitse bwino ubwenzi wanu na Yehova, kodi muyenela kuwongolela mbali ziti pa kuŵelenga kwanu Baibo?

Kodi muyenela kucita ciyani kuti phunzilo la inumwini lizikupindulilani kwambili? Kuti muone zimene mungacite, tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Kodi mwaona zotani mu vidiyo iyi zimene mungakonde kugwilitsa nchito?

  • Ni nkhani ziti zimene mungakonde kuziŵelenga?

5. Dziikileni zolinga zauzimu

Kukhala na zolinga mu utumiki wanu kwa Yehova kudzakuthandizani kupitabe patsogolo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Mu vidiyo iyi, kodi kudziikila zolinga zauzimu kunam’pindulila bwanji Cameron?

Si onse amene angasamukile ku dziko lina kukagwila nchito yolalikila. Koma tonsefe tikhoza kudziikila zolinga zimene tingazikwanitse. Ŵelengani Miyambo 21:5, na kuona zolinga zimene mungadziikile . . .

  • mu mpingo.

  • pa nchito yolalikila.

Kodi mfundo ya pa lembali, ingakuthandizeni bwanji kukwanilitsa zolinga zanu?

Zolinga zina zimene mungaziganizile

  • Kuwongolela mapemphelo anu.

  • Kuŵelenga Baibo yonse kuitsiliza.

  • Kudziŵa munthu aliyense mu mpingo wanu.

  • Kuyambitsa phunzilo la Baibo na kumalitsogoza.

  • Kutumikila monga mpainiya wothandiza kapena wa nthawi zonse.

  • Ngati ndinu m’bale, kulimbikila kuti mukakhale mtumiki wothandiza.

6. Kondwelani na moyo kwamuyaya!

Ŵelengani Salimo 37:11, 29, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mungacite ciyani kuti mukondwele na moyo lelo komanso kwamuyaya?

CIDULE CAKE

Pitilizani kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova, na kudziikila zolinga zauzimu. Mukatelo, mudzakondwela na moyo kwamuyaya!

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani muyenela kukhala na cidalilo conse kuti Yehova adzakuthandizani kuti mum’tumikile mokhulupilika?

  • Muyenela kucita ciyani kuti mulimbitse ubwenzi wanu na Yehova?

  • Kodi kudziikila zolinga zauzimu kungakuthandizeni bwanji kupita patsogolo?

Zolinga Zotenga Nthawi Yaitali

FUFUZANI

Kodi n’citi cimene Yehova amayamikila kwambili, kukangalika kwambili pa nthawi inayake cabe, kapena kukhulupilika kwa moyo wonse?

Khalani Okhulupilika Monga Abulahamu (9:20)

Mtumiki wa Yehova wokhulupilika aliyense akhoza kutayikidwa cimwemwe cake. Onani njila yopezelanso cimwemwe.

Pezaninso Cimwemwe mwa Kuphunzila na Kusinkha-sinkha (5:25)

Kodi mungadziikile zolinga zauzimu zotani, ndipo mungazikwanilitse bwanji?

“Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu” (Nsanja ya Olonda, July 15, 2004)

N’cifukwa ciyani kukhwima kuuzimu kuli kofunika? Nanga muyenela kucita ciyani kuti mufikepo pa kukhwima kuuzimu?

“Yesetsani Kukula Mwauzimu Chifukwa ‘Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi’” (Nsanja ya Olonda, May 15, 2009)