Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Obweleza a Cigawo 1

Mafunso Obweleza a Cigawo 1

Kambilanani na mphunzitsi wanu mafunso aya:

  1. Pa malonjezo a m’Baibo onena za m’tsogolo, kodi m’makondapo kwambili ati?

    (Onani Phunzilo 02.)

  2. N’cifukwa ciyani mumakhulupilila kuti Baibo ni Mawu a Mulungu?

    (Onani Phunzilo 03 na 05.)

  3. N’cifukwa ciyani kuli kofunika kumachula ­dzina lakuti Yehova?

    (Onani Phunzilo 04.)

  4. Baibo imanena kuti Mulungu ndiye “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Kodi mumakhulupilila zimenezi?

    (Onani Phunzilo 06.)

  5. Ŵelengani Miyambo 3:​32.

    • N’cifukwa ciyani sitingapeze Bwenzi ­lopambana Yehova?

    • Kodi Yehova amayembekezela ciyani kwa mabwenzi ake? Kodi muganiza kuti ­zimenezi n’zotheka?

      (Onani Phunzilo 07 na 08.)

  6. Ŵelengani Salimo 62:8.

    • Kodi ni zinthu ziti zimene mwapemphelelapo kwa Yehova? Nanga zinanso zimene ­mungapemphelele n’zotani?

    • Kodi Yehova amayankha bwanji ­mapemphelo?

      (Onani Phunzilo 09.)

  7. Ŵelengani Aheberi 10:​24, 25.

    • Kodi misonkhano ya Mboni za Yehova ­ingakupindulileni bwanji?

    • Kodi muganiza m’pofunikiladi kucita ­khama kuti muzipezeka kumisonkhano?

      (Onani Phunzilo 10.)

  8. N’cifukwa ciyani kuŵelenga Baibo nthawi zonse kuli kofunika? Kodi mumaŵelenga nthawi yanji Baibo tsiku lililonse?

    (Onani Phunzilo 11.)

  9. Kodi pofika pano, n’ciyani cakukondweletsani kwambili pa kuphunzila kwanu Baibo?

  10. Kucokela pamene munayamba kuphunzila Baibo, kodi mwakumanapo na zovuta zilizonse? N’ciyani cingakuthandizeni kuti musaleke ­kuphunzila?

    (Onani Phunzilo 12.)