Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kubwereza Gawo 2

Kubwereza Gawo 2

Kambiranani mafunsowa ndi mphunzitsi wanu:

  1. Kodi Mulungu adzachita zotani ndi zipembedzo zonyenga?

    (Onani Phunziro 13.)

  2. Werengani Ekisodo 20:4-6.

    • Kodi Yehova amamva bwanji anthu amene amanena kuti akumulambira akamagwiritsa ntchito zifaniziro?

      (Onani Phunziro 14.)

  3. Kodi Yesu ndi ndani?

    (Onani Phunziro 15.)

  4. Kodi ndi makhalidwe ati a Yesu amene amakusangalatsani kwambiri?

    (Onani Phunziro 17.)

  5. Werengani Yohane 13:34, 35 ndi Machitidwe 5:42.

    • Kodi Akhristu enieni ndi ndani masiku ano? N’chiyani chimakutsimikizirani kuti ndi Akhristu enieni?

      (Onani Phunziro 18 ndi 19.)

  6. Kodi mutu wa mpingo ndi ndani, nanga amautsogolera bwanji?

    (Onani Phunziro 20.)

  7. Werengani Mateyu 24:14.

    • Kodi ulosi umenewu ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

    • Ndi ndani amene mwamuuzako uthenga wabwino?

      (Onani Phunziro 21 ndi 22.)

  8. Kodi mukuganiza kuti ubatizo ungakuthandizeni kukhala ndi tsogolo labwino? N’chifukwa chiyani mukutero?

    (Onani Phunziro 23.)

  9. Mungatani kuti musamavutitsidwe ndi Satana komanso ziwanda?

    (Onani Phunziro 24.)

  10. Kodi cholinga cha Mulungu ndi choti tikhale ndi moyo wotani?

    (Onani Phunziro 25.)

  11. N’chifukwa chiyani anthu amavutika komanso kufa?

    (Onani Phunziro 26.)

  12. Werengani Yohane 3:16.

    • Kodi Yehova wachita zotani kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa?

      (Onani Phunziro 27.)

  13. Werengani Mlaliki 9:5.

    • N’chiyani chimachitikira munthu amene wamwalira?

    • Kodi Yesu adzawachitira chiyani anthu ambirimbiri amene anamwalira?

      (Onani Phunziro 29 ndi 30.)

  14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Ufumu wa Mulungu ndi wabwino kwambiri kuposa boma lina lililonse?

    (Onani Phunziro 31 ndi 33.)

  15. Kodi mumakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira panopa? N’chifukwa chiyani mukutero? Kodi unayamba liti kulamulira?

    (Onani Phunziro 32.)