Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kubweleza Cigawo 2

Kubweleza Cigawo 2

Kambilanani na mphunzitsi wanu mafunso aya:

  1. Kodi zipembedzo zonyenga Mulungu adzacita nazo bwanji?

    (Onani Phunzilo 13.)

  2. Ŵelengani Ekisodo 20:4-6.

    • Kodi Yehova amamva bwanji pamene anthu ayesa kumulambila na zifanizilo?

      (Onani Phunzilo 14.)

  3. Kodi Yesu Ndani?

    (Onani Phunzilo 15.)

  4. Kodi ni makhalidwe ati a Yesu amene mumakopeka nawo?

    (Onani Phunzilo 17.)

  5. Ŵelengani Yohane 13:34, 35, komanso Machitidwe 5:42.

    • Kodi Akhristu enieni masiku ano ndani? Nanga cimakukhutilitsani n’ciyani kuti ndiwo Akhristu oona?

      (Onani Phunzilo 18 komanso 19.)

  6. Kodi mutu wa mpingo ndani, ndipo amautsogolela motani?

    (Onani Phunzilo 20.)

  7. Ŵelengani Mateyu 24:14.

    • Kodi ulosi umenewu ukukwanilitsidwa bwanji masiku ano?

    • Kodi mwakhala mukuuzako ndani uthenga wabwino?

      (Onani Phunzilo 21 komanso 22.)

  8. Kodi muganiza kuti kukhala na colinga cokabatizika n’kofunikadi? Cifukwa ciyani?

    (Onani Phunzilo 23.)

  9. Kodi muyenela kucita ciyani kuti mudziteteze kwa Satana na ziŵanda zake?

    (Onani Phunzilo 24.

  10. Kodi Mulungu ali nafe colinga canji?

    (Onani Phunzilo 25.)

  11. N’cifukwa ciyani anthufe timakumana na mavuto komanso kumwalila?

    (Onani Phunzilo 26.)

  12. Ŵelengani Yohane 3:16.

    • Kodi Yehova anacita ciyani kuti atimasule ku ucimo na imfa?

      (Onani Phunzilo 27.)

  13. Ŵelengani Mlaliki 9:5.

    • Kodi munthu akamwalila n’ciyani cimacitika pambuyo pake?

    • Kodi Yesu adzacita ciyani kwa anthu mabiliyoni amene anamwalila?

      (Onani Phunzilo 29 komanso 30.)

  14. N’cifukwa ciyani Ufumu wa Mulungu umapambana boma lina lililonse?

    (Onani Phunzilo 31 na 33.)

  15. Kodi mukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila pali pano? Cifukwa ciyani? Ndipo unayamba liti kulamulila?

    (Onani Phunzilo 32.)