Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kubweleza Cigawo 4

Kubweleza Cigawo 4

Kambilanani mafunso aya na mphunzitsi wanu:

  1. Ŵelengani Miyambo 13:20.

    • Kodi n’cifukwa ciyani muyenela kusankha anzanu mwanzelu?

      (Onani Phunzilo 48.)

  2. Kodi ni ulangizi wotani wa m’Baibo umene ungakuthandizeni ngati ndinu . . .

    • mwamuna wokwatila kapena mkazi wokwatiwa?

    • kholo kapena mwana?

      (Onani Phunzilo 49 komanso 50.)

  3. Kodi ni malankhulidwe otani amene amakondweletsa Yehova? Ndipo ni ati amene amamukhumudwitsa?

    (Onani Phunzilo 51.)

  4. Kodi ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingakuthandizeni kupanga zisankho zanzelu pa nkhani ya maonekedwe anu?

    (Onani Phunzilo 52.)

  5. Kodi mungacite bwanji kuti musankhe zosangalatsa zovomelezeka kwa Yehova?

    (Onani Phunzilo 53.)

  6. Ŵelengani Mateyu 24:45-47.

    • Kodi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” ndani?

      (Onani Phunzilo 54.)

  7. Kodi mpingo wanu mungauthandize bwanji na nthawi yanu, mphamvu zanu, komanso cuma canu?

    (Onani Phunzilo 55.)

  8. Ŵelengani Salimo 133:1.

    • Kodi mungathandizile kusungitsa mgwilizano wa mpingo m’njila ziti?

      (Onani Phunzilo 56.)

  9. Kodi tingalandile bwanji thandizo la Yehova tikacita chimo lalikulu?

    (Onani Phunzilo 57.)

  10. Ŵelengani 1 Mbiri 28:9.

    • Kodi pamene ena akutsutsa kulambila koona kapena kusiya coonadi, mungaonetse bwanji kuti ndinu wodzipeleka kwa Yehova na “mtima wathunthu”?

    • Kuti mukhale wokhulupilikabe kwa Yehova, komanso kuti mulekane naco cipembedzo conyenga, kodi pali mbali zina zimene muyenela kusintha pa umoyo wanu?

      (Onani Phunzilo 58.)

  11. Kodi mazunzo mungawakonzekele motani?

    (Onani Phunzilo 59.)

  12. Kodi mukukonzekela kucita zotani kuti musaleke kupita patsogolo kuuzimu?

    (Onani Phunzilo 60.)