Mawu Akumapeto

Mawu Akumapeto
  1.  Kodi Babulo Wamkulu Tingamudziwe Bwanji?

  2.  Kodi Mesiya Anaonekera Liti?

  3.  Njira Zothandizira Odwala Zokhudza Magazi

  4.  Kodi Okwatirana Angapatukane pa Zifukwa Ziti?

  5.  Maholide Ndiponso Zikondwerero

  6.  Matenda Opatsirana

  7.  Nkhani Zokhudza Bizinesi Ndi Malamulo

 1. Kodi Babulo Wamkulu Tingamudziwe Bwanji?

Kodi timadziwa bwanji kuti “Babulo Wamkulu” amaimira zipembedzo zonyenga zonse? (Chivumbulutso 17:5) Taonani mfundo izi:

  • Akupezeka padziko lonse lapansi. Baibulo limanena kuti Babulo Wamkulu wakhala pamwamba pa ‘makamu ndi mayiko’ ndipo ‘akulamulira mafumu a dziko lapansi.’​—Chivumbulutso 17:15, 18.

  • Iye sangakhale gulu landale kapenanso lochita zamalonda. Zili choncho chifukwa “mafumu a dziko lapansi” ndi “amalonda oyendayenda,” sadzawonongedwa pa nthawi yomwe Babulo Wamkulu azidzawonongedwa.​—Chivumbulutso 18:9, 15.

  • Amachititsa anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu. Iye amatchedwa kuti hule chifukwa choti amachita mgwirizano ndi maboma n’cholinga choti apeze ndalama ndi zinthu zina zomukomera. (Chivumbulutso 17:1, 2) Amasocheretsa anthu amitundu yonse ndiponso waphetsa anthu ambirimbiri.​—Chivumbulutso 18:23, 24.

Bwererani pa phunziro 13 mfundo 6

 2. Kodi Mesiya Anaonekera Liti?

Baibulo linalosera kuti Mesiya adzaonekera pakadzadutsa milungu 69.​—Werengani Danieli 9:25.

  • Kodi milungu 69 inayamba liti? Inayamba m’chaka cha 455 B.C.E. Pa nthawiyi Bwanamkubwa Nehemiya anafika ku Yerusalemu kuti ‘akonze ndi kumanganso’ mzindawo.​—Danieli 9:25; Nehemiya 2:1, 5-8.

  • Kodi milungu 69 inatenga nthawi yaitali bwanji? M’maulosi ena a m’Baibulo, tsiku limodzi limaimira chaka chimodzi. (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Choncho, mlungu umodzi ukuimira zaka 7. Mu ulosiwu milungu 69 ikuimira zaka 483 (69 x 7).

  • Kodi milungu 69 inatha liti? Tikawerengera zaka 483 kuyambira m’chaka cha 455  B.C.E., zikutifikitsa m’chaka cha 29 C.E. a Chaka chimenechi n’chimene Yesu anabatizidwa n’kukhala Mesiya.​​​—Luka 3:1, 2, 21, 22.

Bwererani pa phunziro 15 mfundo 5

 3. Njira Zothandizira Odwala Zokhudza Magazi

Pali njira zina zothandizira odwala zomwe achipatala amafunika kugwiritsa ntchito magazi a munthu yemwe akudwala. Koma zina mwa njirazi ndi zosaloleka kwa Akhristu. Njirazi ndi monga kupereka magazi kapena kugwiritsa ntchito magazi a wodwalayo, omwe asungidwa poyembekezera kumuchita opaleshoni.​—Deuteronomo 15:23.

Komabe pali njira zina zomwe zingakhale zololeka kwa Mkhristu. Njirazi ndi monga kuyeza, kusefa magazi, kusungunula magazi, kugwiritsa ntchito mashini opulumutsira magazi kapenanso mashini omwe amagwira ntchito ngati mtima ndi mapapo pa nthawi yopanga opaleshoni. Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha mmene achipatala angagwiritsire ntchito magazi ake pamene akumupanga opaleshoni, kumuyeza magazi kapenanso pa nthawi imene akumupatsa chithandizo chinachake. Dokotala aliyense angagwiritse ntchito njira zimenezi mosiyanako ndi dokotala wina. Choncho, Mkhristu ayenera kufufuza kaye kuti adziwe mmene dokototala wake angagwiritsire ntchito magazi ake asanamupange opaleshoni, kumuyeza kapenanso kumupatsa chithandizo chilichonse. Ganizirani mafunso awa:

  • Kodi magazi anga ena adzafunika kuwapatutsa kaye m’thupi langa ndipo mwina adzasiya kuyenda kwa kanthawi? Zikadzatero, kodi chikumbumtima changa chidzandilola kuona kuti magazi amenewa adakali mbali ya thupi langa moti si ofunika kuti ‘athiridwe pansi’?​—Deuteronomo 12:23, 24.

  • Nanga bwanji ngati pamene akundipatsa thandizo lachipatala pakufunika kuti magazi anga ena awatenge, kuwasakaniza ndi zinthu zina kenako n’kuwabwezeretsa m’thupi langa? Kodi chikumbumtima changa chingandilole kapena sichingandilole kulandira chithandizo choterechi mogwirizana ndi zimene ndimaphunzira m’Baibulo?

Bwererani pa phunziro 39 mfundo 3

 4. Kodi Okwatirana Angapatukane pa Zifukwa Ziti?

Baibulo sililimbikitsa kuti anthu okwatirana azipatukana ndipo limanena kuti ngati angapatukane, alibe ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso. (1 Akorinto 7:10, 11) Komabe, pali zifukwa zina zimene zimachititsa Akhristu ena kusankha kupatukana.

  • Kulephera kusamalira banja mwadala: Mwamuna sakusamalira banja lake mwadala mpaka kufika poti banjalo likusoweratu zinthu zofunika pa moyo.​—1 Timoteyo 5:8.

  • Kuchita nkhanza zoopsa: Nkhanza zingachititse kuti thanzi kapena moyo wa munthu ukhale pachiopsezo.​—Agalatiya 5:19-21.

  • Kuchititsa kuti mnzake asiyiretu kulambira Yehova: Ngati mwamuna kapena mkazi akuchititsa kuti mnzake asiyiretu kutumikira Yehova.​—Machitidwe 5:29.

Bwererani pa phunziro 42 mfundo 3

 5. Maholide Ndiponso Zikondwerero

Akhristu sachita nawo maholide omwe sasangalatsa Yehova. Komabe, Mkhristu aliyense ayenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chake posankha zoyenera kuchita pa nkhani imeneyi mogwirizana ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. Taonani zitsanzo izi:

  • Munthu wina wakufunirani zabwino pa holide inayake. Mungangomuyankha kuti, “Zikomo.” Ngati munthuyo akufuna kudziwa zambiri, mungamufotokozere chifukwa chimene simukondwerera nawo holide imeneyo.

  • Mwamuna kapena mkazi wanu, yemwe si wa Mboni za Yehova, wakuitanirani kuti mukadye limodzi chakudya ndi achibale pa holide inayake. Ngati chikumbumtima chanu chikukulolani kupita, mungachite bwino kumufotokozera kuti ngati kuphwandoko kungakachitike miyambo ina yosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, simukachita nawo.

  • Kuntchito kwanu kapena abwana anu akukupatsani bonasi pa nthawi yomwe anthu akukondwerera holide inayake. Kodi muyenera kukana bonasiyo? Osati kwenikweni. Kodi akukupatsani bonasiyo n’cholinga choti mukondwerere nawo holideyo kapena yangokhala njira yokuyamikirani chifukwa choti mumagwira ntchito bwino?

  • Munthu wina akukupatsani mphatso pa nthawi ya holide inayake. Mwina anganene kuti: “Ndikudziwa kuti simukondwerera nawo holideyi, koma ndangofuna kukupatsani mphatsoyi.” N’kutheka kuti akukupatsani mphatsoyo chifukwa chongofuna kukuchitirani zabwino basi. Komabe, kodi sizingakhale bwino kuganizira ngati akukupatsani mphatsoyo pofuna kukuyesani kapenanso kuti mukondwerere nawo holideyo? Choncho pambuyo poganizira mfundo zimenezi, mungasankhe kulandira kapena kukana mphatsoyo. Nthawi zonse tikamasankha zochita, timafuna kukhala ndi chikumbumtima chabwino komanso kukhala okhulupirika kwa Yehova.​​​—Machitidwe 23:1.

Bwererani pa phunziro 44 mfundo 1

 6. Matenda Opatsirana

Timayesetsa kuchita zinthu mosamala kwambiri popewa kufalitsa matenda opatsirana chifukwa chakuti timakonda anzathu. Choncho ngati tikudwala matenda opatsirana kapena tikuona zizindikiro zoti mwina tikudwala ndipo tingapatsire ena, tiyenera kukhala osamala kwambiri. Timachita zimenezi chifukwa Baibulo limatiuza kuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”​—Aroma 13:8-10.

Kodi munthu yemwe ali ndi matenda opatsirana ayenera kuchita zotani pomvera mfundo imeneyi? Sayenera kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti ena atenge matendawo monga kuwapatsa moni wa m’manja, kuwahaga kapenanso kuwakisa. Munthu wotereyu sayenera kukhumudwa anthu ena akasankha kuti asamuitanire kunyumba kwawo pofuna kuteteza banja lawo. Ngati munthuyo akufuna kubatizidwa, ayenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu za matenda ake n’cholinga choti asapatsire matendawo anthu enanso omwe akufuna kubatizidwa. Munthu yemwe anadwalapo matenda opatsirana kapena akudzikayikira kuti angakhale ndi matendawa, angachite bwino kukayezetsa magazi asanayambe chibwenzi ndi munthu wina. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ‘sitikuganizira zofuna zathu zokha, koma tikuganiziranso zofuna za ena.’​—Afilipi 2:4.

Bwererani pa phunziro 56 mfundo 2

 7. Nkhani Zokhudza Bizinesi Ndi Malamulo

Kuti tipewe mavuto ambiri pa nkhani za bizinesi komanso ndalama, tiyenera kulemberana kapena kusainirana mgwirizano uliwonse ngakhale pamene tikuchita mgwirizanowo ndi Mkhristu mnzathu. (Yeremiya 32:9-12) Komabe, nthawi zina Akhristu akhoza kusemphana maganizo pa nkhani zing’onozing’ono zokhudza ndalama kapena zinthu zina. Zikatero, iwo ayenera kuthetsa kusamvanako mwamsanga, mwamtendere komanso paokha.

Koma kodi tiyenera kuchita chiyani tikasemphana maganizo pa nkhani zikuluzikulu monga kuba ndalama mwachinyengo kapena kuipitsa mbiri ya munthu wina? (Werengani Mateyu 18:​15-17.) Yesu ananena kuti tizitsatira mfundo zitatu izi:

  1. Muziyesetsa kukambirana nkhaniyo panokha.​—Onani vesi 15.

  2. Zikakanika, mungapiteko ndi munthu mmodzi kapena anthu awiri odalirika amumpingo mwanu kuti mukakambirane nkhaniyo.​—Onani vesi 16.

  3. Zikavutabe, m’pamene mungapemphe akulu kuti akuthandizeni.​—Onani vesi 17.

Tiyenera kuyesetsa kupewa kutengera abale athu kukhoti chifukwa kuchita zimenezi kungaipitse dzina la Yehova ndiponso mpingo. (1 Akorinto 6:1-8) Komabe, pali nkhani zina zomwe zingafunike kuweruzidwa ndi khoti. Mwachitsanzo, kuthetsa banja, kusankha kholo lomwe liyenera kulera mwana makolo akasiyana, ndalama zimene mwamuna kapena mkazi ayenera kumapereka kwa mnzakeyo banja likatha, woyenera kulandira inshulansi, ndalama zimene muyenera kulandira bizinesi ikalowa pansi kapenanso kusainira mawilu. Mkhristu amene angapite kukhoti ndi nkhani zimenezi n’cholinga choti athetse nkhanizo mwamtendere sakuchita zinthu mosemphana ndi malangizo a m’Baibulo.

Mkhristu sangaphwanye malangizo a m’Baibulo ngati angapititse kupolisi kapena kukhoti nkhani yokhudza munthu yemwe wapalamula mlandu waukulu monga kugwiririra, kuchitira mwana nkhanza, kuvulaza munthu, kuba zinthu zochuluka kapenanso kupha munthu.

Bwererani pa phunziro 56 mfundo 3

a Kuchokera mu 455 B.C.E. kufika mu 1 B.C.E. ndi zaka 454. Kuchokera mu 1 B.C.E. kufika mu 1 C.E. ndi chaka chimodzi. Ndipo kuchokera mu 1 C.E. kufika mu 29 C.E. ndi zaka 28. Choncho tikaphatikiza zakazi (454 + 1 + 28) tikupeza zaka 483.