Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pamene Mungayambile Kuŵelenga Baibo

Pamene Mungayambile Kuŵelenga Baibo

Mungakondwele nako kuŵelenga Baibo! Kuti mupeze poyambila pabwino, sankhani nkhani imene mwakonda, ndipo ŵelengani malemba ake.

Anthu Ochuka komanso Nkhani Zawo

  • Nowa na Cigumula: Genesis 6:9–9:19

  • Mose pa Nyanja Yofiila: Ekisodo 13:17–14:31

  • Rute na Naomi: Rute macaputala 1-4

  • Davide na Goliyati: 1 Samueli caputala 17

  • Abigayeli: 1 Samueli 25:2-35

  • Danieli mu dzenje la mikango: Danieli caputala 6

  • Elizabeti na Mariya: Luka macaputala 1-2

Nzelu Zothandiza pa Umoyo

  • Umoyo wa Banja: Aefeso 5:28, 29, 33; 6:1-4

  • Mabwenzi: Miyambo 13:20; 17:17; 27:17

  • Pemphelo: Salimo 55:22; 62:8; 1 Yohane 5:14

  • Ulaliki wa pa Phili: Mateyu macaputala 5-7

  • Nchito: Miyambo 14:23; Mlaliki 3:12, 13; 4:6

Mukafunikila Thandizo . . .

  • Pamene mwalefulidwa: Salimo 23; Yesaya 41:10

  • Pamene muli pacisoni: 2 Akorinto 1:3, 4; 1 Petulo 5:7

  • Pamene mwapalamula mlandu: Salimo 86:5; Ezekieli 18:21, 22

Zimene Baibo Imakamba za . . .

  • Masiku otsiliza: Mateyu 24:3-14; 2 Timoteyo 3:1-5

  • Ciyembekezo ca zam’tsogolo: Salimo 37:10, 11, 29; Chivumbulutso 21:3, 4

MFUNDO YOTHANDIZA: Kuti muwamvetse bwino malemba ali pamwambapa, ŵelengani caputala kapena macaputala onse. Ndiponso kuti mulondoloze bwino kaŵelengedwe kanu, seŵenzetsani chati yakuti “Congani Mbali Zimene Mwaŵelenga.” Onetsetsani kuti tsiku lililonse mukuŵelengako gawo la m’Baibo.