Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

Buku la Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu likuthandizani kuti musamavutike kupeza mavesi ndi nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuthana ndi mavuto. Lingakuthandizeninso kupeza mavesi amene mungawagwiritse ntchito polimbikitsa ena komanso kuwathandiza kusankha zochita zimene zingalemekeze Yehova. Sankhani mutu wa nkhani imene mukufuna. Pa mutu uliwonse, pali mafunso othandiza komanso mawu achidule ofotokozera nkhani za m’Baibulo. (Onani kabokosi kakuti “ Mmene Mungapezere Mitu ya Nkhani M’bukuli.”) Mupeza malemba osiyanasiyana amene angakuthandizeni kupeza malangizo, kukulimbikitsani ndiponso kukutonthozani. Mupezanso mfundo za m’Baibulo zomwe mungatsitsimule nazo anthu amene afooka, kuwathandiza kuthana ndi mavuto komanso kuwapatsa malangizo ndi kuwalimbikitsa.

Bukuli silinasonyeze m’ndandanda wa malemba onse okhudza mitu ya nkhani. Koma lakonzedwa kuti likuthandizeni kupeza malemba ofunika kwambiri koma ngati mukufuna kudziwa zambiri mungafufuze m’mabuku ena. (Miy 2:1-6) Kuti mufufuze mozama, gwiritsani ntchito malifalensi amudanga lapakati komanso mfundo zothandiza pophunzira mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Kuti mumvetse bwino tanthauzo la lemba linalake, gwiritsani ntchito Buku Lofufuzira Nkhani la Mboni za Yehova komanso buku la Chingelezi lakuti Watch Tower Publications Index. Muzifufuza m’mabuku omwe afalitsidwa chaposachedwapa kuti mutsimikizire ngati mfundo za m’Malemba zomwe mukudziwa zikugwirizana ndi kamvekedwe katsopano.

Buku la Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu likuthandizeni pamene mukufufuza nzeru, kudziwa zinthu komanso kumvetsa zinthu m’Malemba Opatulika. Mukamagwiritsa ntchito bukuli, mudzafika potsimikizira kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu.”—Ahe 4:12.