Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitonthozo

Chitonthozo

Mfundo zotonthoza za m’Baibulo zimene zingatithandize tikakhumudwa

Nkhawa

Onani “Nkhawa

Kupwetekedwa mtima; kusunga mkwiyo

Anthu ena amasiya kusangalala chifukwa cha mavuto kapena zinthu zopanda chilungamo zimene zikuwachitikira

Mla 9:11, 12

Onaninso Sl 142:4; Mla 4:1; 7:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ru 1:11-13, 20​—Naomi anakhumudwa kwambiri ndipo ankaona ngati Yehova wamutaya mwamuna wake ndi ana ake awiri atamwalira

    • Yob 3:1, 11, 25, 26; 10:1​—Yobu anamva kupweteka kwambiri mumtima atataya chuma chake, ana ake 10 komanso atadwala matenda aakulu

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

Anthu ena amasiya kusangalala chifukwa cha zochita za ena

Mla 4:1, 2

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 1:6, 7, 10, 13-16 ​—Hana anakhumudwa kwambiri chifukwa cha nkhanza zimene Penina ankamuchitira komanso chifukwa chakuti Mkulu wa Ansembe Eli ankamuganizira kuti waledzera

    • Yob 8:3-6; 16:1-5; 19:2, 3​—Anzake atatu a Yobu omwe ankayenera kumutonthoza, ankadziona ngati olungama ndipo anamuweruza molakwika zomwe zinachititsa Yobu kukhumudwa

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

Kudziimba kwambiri mlandu

Eza 9:6; Sl 38:3, 4, 8; 40:12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mf 22:8-13; 23:1-3​—Mfumu Yosiya ndi anthu ake anazindikira kulakwa kwawo pamene buku la Chilamulo linkawerengedwa mokweza

    • Eza 9:10-15; 10:1-4​—Wansembe Ezara anakhumudwa kwambiri chifukwa choti anthu ena anakwatira akazi achilendo zomwe zinali zosemphana ndi malamulo a Yehova

    • Lu 22:54-62​—Mtumwi Petulo atakana Yesu katatu kuti sakumudziwa, anadziimba mlandu kwambiri

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • 2Mb 33:9-13, 15, 16​—Manase anachita zoipa kwambiri kuposa mafumu ena onse a ku Yuda, komabe analapa ndipo Yehova anamuchitira chifundo

    • Lu 15:11-32​—Yesu anafotokoza fanizo la mwana wolowerera pofuna kutiphunzitsa kuti Yehova amakhululuka ndi mtima wonse

Kukhumudwa anthu ena akatichitira zinthu zopweteketsa mtima, zokhumudwitsa kapena akatichitira zinthu mosakhulupirika

Onani “Kukhumudwa

Kukhumudwa chifukwa cha zimene timalakwitsa kapena machimo athu

Onani “Kukhumudwa

Kudzikayikira kuti ndife osafunika

Onani “Kudzikayikira

Kudziona kuti sitingakwanitse kupirira vuto linalake lalikulu kapenanso utumiki wovuta

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Eks 3:11; 4:10​—Mneneri Mose ankaona kuti sangakwanitse kukakumana ndi Farao komanso kutsogolera anthu a Mulungu kuchoka ku Iguputo

    • Yer 1:4-6​—Yeremiya ankadziona kuti anali mwana moti sakanakwanitsa kupereka uthenga wachiweruzo kwa anthu ovuta

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • Eks 3:12; 4:11, 12​—Yehova anachita zinthu moleza mtima ndi Mose pomutsimikizira kuti amuthandiza kuchita utumiki umene anamupatsa

    • Yer 1:7-10​—Yehova anatsimikizira mneneri Yeremiya kuti asachite mantha chifukwa Iye amuthandiza kuchita utumiki wovuta

Nsanje; kaduka

Onani “Nsanje

Kulephera kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba

Sl 71:9, 18; Mla 12:1-7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mf 20:1-3​—Mfumu Hezekiya atauzidwa kuti amwalira ndi matenda amene ankadwala, analira kwambiri

    • Afi 2:25-30​—Epafurodito anavutika maganizo chifukwa mpingo unali utadziwa kuti iye akudwala choncho anali ndi nkhawa kuti abalewo aona ngati walephera kuchita utumiki wake

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • 2 Sa 17:27-29; 19:31-38​—Mfumu inakomera mtima Barizilai, n’kumupempha kuti apitire limodzi ku Yerusalemu, koma modzichepetsa iye anakana kupita podziwa kuti sangakwanitse chifukwa anali wokalamba

    • Sl 41:1-3, 12​—Mfumu Davide atadwala kwambiri, anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova amuthandiza

    • Mko 12:41-44​—Yesu anayamikira mayi wamasiye wosauka chifukwa anapereka zonse zimene anali nazo

Kumangoganizira zoipa zimene ena anatichitira

Onani “Kuchitiridwa Zoipa

Mantha osayenerera; kuopa

Onani “Mantha

Chizunzo

Onani “Chizunzo