Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhumudwa

Kukhumudwa

Kukhumudwa chifukwa choti anthu ena atinenera zoipa

Sl 55:12-14; Lu 22:21, 48

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 8:1-6​—Mneneri Samueli anakhumudwa Aisiraeli atakakamira kuti awasankhire mfumu

    • 1Sa 20:30-34​—Yonatani anakhumudwa komanso kuchita manyazi bambo ake, Mfumu Sauli atamulusira

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • Sl 55:12-14, 16-18, 22​—Ngakhale kuti Mfumu Davide anaukiridwa ndi mnzake wapamtima Ahitofeli, iye anatulira Yehova nkhawa zake ndipo anatonthozedwa

    • 2Ti 4:16-18​—Pamene mtumwi Paulo ankaimbidwa mlandu m’khoti, anzake onse anamusiya yekha koma iye anapeza mphamvu atalimbikitsidwa ndi Yehova komanso chifukwa cha chiyembekezo chimene Iye amapereka

Kukhumudwa chifukwa cha zofooka komanso machimo athu

Yob 14:4; Aro 3:23; 5:12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 51:1-5​—Mfumu Davide anamva kupweteka kwambiri mumtima chifukwa cha machimo amene analakwira Yehova

    • Aro 7:19-24 ​—Mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni chifukwa chakuti anali pa nkhondo yolimbana ndi maganizo ochita zoipa m’malo mochita zabwino

  • Malemba otonthoza:

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • 1Mf 9:2-5​—Ngakhale kuti Mfumu Davide anachita machimo akuluakulu, Yehova amamukumbukira kuti ndi munthu wokhulupirika

    • 1Ti 1:12-16​—Mtumwi Paulo anali ndi chikhulupiriro kuti Mulungu amuchitira chifundo ngakhale anachita machimo akuluakulu m’mbuyomu