Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufooka

Kufooka

Kodi pangakhale vuto lanji ngati atumiki a Yehova atafooka?

N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza kulimbana ndi zinthu zofooketsa?

Sl 23:1-6; 113:6-8; Yes 40:11; 41:10, 13; 2Ak 1:3, 4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 11:28-30​—Yesu yemwe amatsatira Atate ake mosalakwitsa kanthu ndi wachifundo komanso wotsitsimula

    • Mt 12:15-21​—Yesu anakwaniritsa ulosi wa pa Yesaya 42:1-4, pokomera mtima anthu ofooka

Malemba othandiza kulimbana ndi zinthu zomwe zingatichititse kuti tikhumudwe

Onani “Chitonthozo

N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbikitsa ena?

Mt 18:6; Aef 4:29

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Nu 32:6-15​—Amuna osakhulupirika 10 amene anakazonda dziko la Kanani anafooketsa Aisiraeli ndipo mtundu wonsewo unakumana ndi mavuto

    • 2Mb 15:1-8​—Uthenga wochokera kwa Yehova unathandiza Mfumu Asa kuchita zinthu molimba mtima pothana ndi khalidwe lachiwerewere