Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumwa Mowa

Kumwa Mowa

Kodi Baibulo limanena kuti kumwa mowa n’kulakwa?

Sl 104:14, 15; Mla 9:7; 10:19; 1Ti 5:23

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yoh 2:1-11​—Yesu anachita chozizwitsa chake choyamba posandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri ndipo zimenezi zinathandiza kuti mkwati ndi mkwatibwi asachititsidwe manyazi paphwando la ukwati wawo

Kodi kumwa kwambiri komanso kuledzera kumabweretsa mavuto otani?

Kodi atumiki a Mulungu amakuona bwanji kuledzera?

1Ak 5:11; 6:9, 10; Aef 5:18; 1Ti 3:2, 3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 9:20-25​—Nowa ataledzera, zinachititsa kuti mdzukulu wake achite tchimo lalikulu

    • 1Sa 25:2, 3, 36​—Nabala yemwe anali wouma mtima komanso wopanda nzeru anachita zinthu zochititsa manyazi kuphatikizapo kuledzera

    • Da 5:1-6, 22, 23, 30, 31​—Mfumu Belisazara atamwa vinyo wambiri, ananyoza Yehova Mulungu ndipo zotsatirapo zake anaphedwa usiku womwewo

N’chifukwa chiyani tifunika kusamala kwambiri ndi kuchuluka kwa mowa umene timamwa ngakhale kuti sitingaledzere?

Kodi tingathandize bwanji Akhristu anzathu omwe akulimbana ndi chizolowezi choledzera?