Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira

Kupirira

N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova amafunika kupirira?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa anthu ena akamakana kapena kutsutsa uthenga wabwino umene timalalikira?

Mt 10:22; Yoh 15:18, 19; 2Ak 6:4, 5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Pe 2:5; Ge 7:23; Mt 24:37-39​—Ngakhale kuti Nowa “ankalalikira za chilungamo cha Mulungu,” anthu ambiri sankamvetsera, koma iye ndi anthu am’banja lake lokha anapulumuka pa nthawi ya Chigumula

    • 2Ti 3:10-14​—Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mavuto amene anakumana nawo m’mbuyomu polimbikitsa Timoteyo kuti nayenso angakwanitse kupirira

N’chifukwa chiyani sitimadabwa anthu am’banja lathu kapena achibale akamatitsutsa kuti tisiye kutumikira Yehova?

Mt 10:22, 36-38; Lu 21:16-19

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 4:3-11; 1Yo 3:11, 12​—Kaini anapha m’bale wake chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa, koma za Abale zinali zolungama

    • Ge 37:5-8, 18-28​—Chifukwa china chomwe chinachititsa kuti azibale ake a Yosefe amukonzere chiwembu n’kumugulitsa, chinali chakuti anawauza zimene iye analota

Tikamazunzidwa, n’chifukwa chiyani sitimaopa imfa?

Mt 10:28; 2Ti 4:6, 7

Onaninso Chv 2:10

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 3:1-6, 13-18​—Shadireki, Misheki ndi Abedinego analolera kufa m’malo molambira fano limene mfumu inaimika

    • Mac 5:27-29, 33, 40-42​—Atumwi anasonyeza kupirira ndipo anapitirizabe kulalikira ngakhale kuti anthu ankawaopseza kuti awapha

Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova tikapatsidwa chilango?

Miy 3:11, 12; Ahe 12:5-7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Nu 20:9-12; De 3:23-28; 31:7, 8​—Ngakhale kuti mneneri Mose anakhumudwa chifukwa cha chilango chimene Yehova anamupatsa, iye anapitirizabe kumutumikira mokhulupirika mpaka mapeto

    • 2Mf 20:12-18; 2Mb 32:24-26​—Pamene Mfumu Hezekiya analakwitsa, Yehova anamudzudzula kudzera mwa mneneri wake ndipo anadzichepetsa n’kupitiriza kutumikira Yehova

N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kupirira anthu ena akasiya kutumikira Yehova?

Yer 1:16-19; Hab 1:2-4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 73:2-24​—Wamasalimo ataona kuti anthu ochita oipa zinthu zikuwayendera bwino, anayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kunali ndi phindu lililonse

    • Yoh 6:60-62, 66-68​—Ngakhale kuti ophunzira a Yesu ambiri anamusiya, mtumwi Petulo sanamusiye chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba

N’chiyani chimene chingatithandize kuti tizipirira?

Kuyandikira Yehova

Kuwerenga Mawu a Mulungu komanso kuganizira mozama

Kupemphera kwa Yehova nthawi zonse komanso mochokera pansi pa mtima

Aro 12:12; Akl 4:2; 1Pe 4:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 6:4-11​—Mneneri Danieli anapitiriza kupemphera pamalo oonekera komanso nthawi zonse, ngakhale kuti anthu ena anamukonzera chiwembu kuti amuphe

    • Mt 26:36-46; Ahe 5:7​—Pa usiku wake womaliza padzikoli, Yesu anapemphera kwa nthawi yaitali komanso mochonderera ndipo analimbikitsa ophunzira ake kuchitanso zomwezo

Kusonkhana nthawi zonse ndi Akhristu anzathu

Kuganizira za madalitso amene Yehova watilonjeza m’tsogolo

Kukonda kwambiri Yehova, abale ndi alongo athu komanso mfundo zolungama za Mulungu

Kulimbitsa chikhulupiriro chathu

Kukumbukira mmene Yehova amamvera tikakhala okhulupirika pamene takumana ndi mavuto

Kodi timapindula bwanji tikapitiriza kupirira mokhulupirika?

Timalemekeza Yehova Mulungu

Miy 27:11; Yoh 15:7, 8; 1Pe 1:6, 7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yob 1:6-12; 2:3-5​—Satana ananena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha madalitso kapena chitetezo chimene amapeza potumikira Yehova. Koma kupirira kwa Yobu kunasonyeza kuti zimene Satana ananenazi n’zabodza

    • Aro 5:19; 1Pe 1:20, 21​—Mosiyana ndi Adamu, yemwe sanamvere Mulungu, Yesu anapirira mokhulupirika mpaka imfa ndipo zimenezi zinapereka yankho la funso ili: Kodi munthu wangwiro angakwanitse kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova pamene wakumana ndi mayesero aakulu?

Timalimbikitsa ena kupirira

Tikamapirira pa utumiki wathu, timalandira madalitso

Tikamapirira timasangalatsa Yehova, ndipo amatidalitsa